[95] Gulu la adani lija lidabwerera kwawo. Koma ena mwa Asilamu achinyengo omwe adali m’gulu la Asilamu omwe sadathawe pomwe anzawo amathawa, sadakhulupirire kuti adaniwo abwerera kwawo, chifukwa choopa; amangoganiza kuti akadalipobe ndipo mwina awathiranso nkhondo kachiwiri. Tero adadzazidwa mantha m’mitima mwawo ndipo tulo tidawasowa. Koma Asilamu enieni sadalabadire chilichonse. Amangodya ndi kugona ngati kuti zopweteka sizinawakhudze.
[96] (Ndime 156-157) Apa Asilamu akuwapepesa kuti asaganizire kuti imfayo yawapeza anzawo chifukwa chopita ku nkhondo nkuti akadapanda kupitako sakadafa. Koma akuwauza kuti adafa chifukwa nthawi yawo yomwe Allah adawalembera kuti akhale pa dziko lapansi idatha. Ndipo ngakhale akadakhala m’nyumba zawo imfa ikadawapezabe. Ndipo akuwauzanso kuti imfa yofera ku nkhondo yoyera njabwino kuposa yofera pakhomo.