Traduction des sens du Noble Coran - La traduction tchétchène - Khâlid Ibrâhîm Bîtâlâ

Numéro de la page:close

external-link copy
154 : 3

ثُمَّ أَنزَلَ عَلَيۡكُم مِّنۢ بَعۡدِ ٱلۡغَمِّ أَمَنَةٗ نُّعَاسٗا يَغۡشَىٰ طَآئِفَةٗ مِّنكُمۡۖ وَطَآئِفَةٞ قَدۡ أَهَمَّتۡهُمۡ أَنفُسُهُمۡ يَظُنُّونَ بِٱللَّهِ غَيۡرَ ٱلۡحَقِّ ظَنَّ ٱلۡجَٰهِلِيَّةِۖ يَقُولُونَ هَل لَّنَا مِنَ ٱلۡأَمۡرِ مِن شَيۡءٖۗ قُلۡ إِنَّ ٱلۡأَمۡرَ كُلَّهُۥ لِلَّهِۗ يُخۡفُونَ فِيٓ أَنفُسِهِم مَّا لَا يُبۡدُونَ لَكَۖ يَقُولُونَ لَوۡ كَانَ لَنَا مِنَ ٱلۡأَمۡرِ شَيۡءٞ مَّا قُتِلۡنَا هَٰهُنَاۗ قُل لَّوۡ كُنتُمۡ فِي بُيُوتِكُمۡ لَبَرَزَ ٱلَّذِينَ كُتِبَ عَلَيۡهِمُ ٱلۡقَتۡلُ إِلَىٰ مَضَاجِعِهِمۡۖ وَلِيَبۡتَلِيَ ٱللَّهُ مَا فِي صُدُورِكُمۡ وَلِيُمَحِّصَ مَا فِي قُلُوبِكُمۡۚ وَٱللَّهُ عَلِيمُۢ بِذَاتِ ٱلصُّدُورِ

Kenako pambuyo pa kudandaula, adakutsitsirani mpumulo - tulo tomwe tidaphimba gulu lina mwa inu. Padali gulu lina lomwe maganizo awo adawatangwanitsa namuganizira Allah ndizoganizira zopanda choonadi, zoganizira zaumbuli; ankati: “Ha! Kodi tili ndi chiyani ife pa chinthu ichi?” Nena: “Zinthu zonse nza Allah.” Akubisa m’mitima mwawo zomwe sakuzionetsa kwa iwe. Akunena: “Tidakakhala ndi chilichonse pa chinthu ichi, sitikadaphedwa apa.” Nena: “Ngakhale mukadakhala m’nyumba zanu, ndithudi kwa iwo amene imfa idalembedwa (kuti amwalire) akadapita kumalo omwalilirawo, koma Allah (adachita izi) kuti awonetse poyera zomwe zili m’zifuwa zanu. Ndikuyeretsa zomwe zili m’mitima mwanu. Ndipo Allah Ngodziwa za mzifuwa.”[95] info

[95] Gulu la adani lija lidabwerera kwawo. Koma ena mwa Asilamu achinyengo omwe adali m’gulu la Asilamu omwe sadathawe pomwe anzawo amathawa, sadakhulupirire kuti adaniwo abwerera kwawo, chifukwa choopa; amangoganiza kuti akadalipobe ndipo mwina awathiranso nkhondo kachiwiri. Tero adadzazidwa mantha m’mitima mwawo ndipo tulo tidawasowa. Koma Asilamu enieni sadalabadire chilichonse. Amangodya ndi kugona ngati kuti zopweteka sizinawakhudze.

التفاسير:

external-link copy
155 : 3

إِنَّ ٱلَّذِينَ تَوَلَّوۡاْ مِنكُمۡ يَوۡمَ ٱلۡتَقَى ٱلۡجَمۡعَانِ إِنَّمَا ٱسۡتَزَلَّهُمُ ٱلشَّيۡطَٰنُ بِبَعۡضِ مَا كَسَبُواْۖ وَلَقَدۡ عَفَا ٱللَّهُ عَنۡهُمۡۗ إِنَّ ٱللَّهَ غَفُورٌ حَلِيمٞ

Ndithudi, mwa inu amene adabwerera m’mbuyo (kuthawa) tsiku lomwe magulu awiri a nkhondo adakumana (pa nkhondo ya Uhudi; gulu la osakhulupirira ndi gulu lankhondo la Asilamu), satana ndiyemwe adawaterezetsa chifukwa cha zina (zolakwa) zomwe adachita; ndipo Allah (tsopano) wawakhululukira. Ndithudi, Allah Ngokhululuka kwambiri, Ngoleza koposa. info
التفاسير:

external-link copy
156 : 3

يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ لَا تَكُونُواْ كَٱلَّذِينَ كَفَرُواْ وَقَالُواْ لِإِخۡوَٰنِهِمۡ إِذَا ضَرَبُواْ فِي ٱلۡأَرۡضِ أَوۡ كَانُواْ غُزّٗى لَّوۡ كَانُواْ عِندَنَا مَا مَاتُواْ وَمَا قُتِلُواْ لِيَجۡعَلَ ٱللَّهُ ذَٰلِكَ حَسۡرَةٗ فِي قُلُوبِهِمۡۗ وَٱللَّهُ يُحۡيِۦ وَيُمِيتُۗ وَٱللَّهُ بِمَا تَعۡمَلُونَ بَصِيرٞ

E inu amene mwakhulupirira! Musakhale ngati amene sadakhulupirire, nanena za anzawo pamene akuyenda pa dziko kapena pomwe akumenyana nkhondo (ndikufera konko): “Akadakhala ndi ife sakadafa, ndiponso sakadaphedwa.” Allah (adawathira maganizo amenewa) kuti azipange zimenezo kukhala zodandaulitsa m’mitima mwawo. Komatu Allah ndi amene amapereka moyo ndi imfa. Ndipo Allah akuona zonse zomwe mukuchita.[96] info

[96] (Ndime 156-157) Apa Asilamu akuwapepesa kuti asaganizire kuti imfayo yawapeza anzawo chifukwa chopita ku nkhondo nkuti akadapanda kupitako sakadafa. Koma akuwauza kuti adafa chifukwa nthawi yawo yomwe Allah adawalembera kuti akhale pa dziko lapansi idatha. Ndipo ngakhale akadakhala m’nyumba zawo imfa ikadawapezabe. Ndipo akuwauzanso kuti imfa yofera ku nkhondo yoyera njabwino kuposa yofera pakhomo.

التفاسير:

external-link copy
157 : 3

وَلَئِن قُتِلۡتُمۡ فِي سَبِيلِ ٱللَّهِ أَوۡ مُتُّمۡ لَمَغۡفِرَةٞ مِّنَ ٱللَّهِ وَرَحۡمَةٌ خَيۡرٞ مِّمَّا يَجۡمَعُونَ

Ndipo ngati mwaphedwa pa njira ya Allah, kapena kufa, (palibe chotaika kwa inu) pakuti chikhululuko ndi chisoni zochokera kwa Allah nzabwino kuposa zomwe akuzisonkhanitsa (pa moyo wa pa dziko lapansi). info
التفاسير: