[87] Ndime iyi ikulimbikitsa anthu kuti akangaze kuchita zinthu zowapezetsa chikondi cha Allah.
[88] Ndime 134-135 zikutchula ena mwa makhalidwe omwe munthu atakhala nawo akalowa ku Munda wa mtendere.
[89] M’ndime iyi Allah akukumbutsa Asilamu zinthu zosowetsa mtendere zomwe zidawapeza m’masiku a Uhudi powauza kuti monga iwo adavutitsidwa ndi adani awo, nawonso adaniwo adavutitsidwa. Umo ndi momwe zinthu zimachitikira mosinthasintha. Nthawi zina zigwera awa, kenako zigwera ena, malinga ndi zochita zawo. Allah sakondera.