[74] Ayuda adauza Mtumiki (s.a.w) kuti: “Iwe sukutsata chikhalidwe cha Ibrahim ngakhale umadzinyenga kuti ukumtsata. Nanga bwanji ukudya nyama ya ngamira, pomwe mneneri Ibrahim sadali kudya ngamira?” Apa Allah akuwatsutsa kuti ngabodza. Ndipo buku lawo la Taurat ndilo mboni pa bodza lawoli. atavundukula buku lawo la Taurat apeza kuti yemwe adadziletsa kudya ngamira ndi Yakobo, yemwe ankadziwikanso kuti Israeli, osati mneneri Ibrahim.Yakobo njemwe adasala kudya nyama ya ngamira mwa chifuniro chake. Ndipo izi adazichita popanda kukakamizidwa ndi Allah.
[75] Apa akunenetsa kuti nyumba yoyamba kukhazikitsidwa kwa anthu kuti ikhale yochitira mapemphero ndi Al-Kaaba, osati Baiti Muqaddas monga momwe Ayuda amakhulupilira.