Traduction des sens du Noble Coran - La traduction tchétchène - Khâlid Ibrâhîm Bîtâlâ

Numéro de la page:close

external-link copy
78 : 3

وَإِنَّ مِنۡهُمۡ لَفَرِيقٗا يَلۡوُۥنَ أَلۡسِنَتَهُم بِٱلۡكِتَٰبِ لِتَحۡسَبُوهُ مِنَ ٱلۡكِتَٰبِ وَمَا هُوَ مِنَ ٱلۡكِتَٰبِ وَيَقُولُونَ هُوَ مِنۡ عِندِ ٱللَّهِ وَمَا هُوَ مِنۡ عِندِ ٱللَّهِۖ وَيَقُولُونَ عَلَى ٱللَّهِ ٱلۡكَذِبَ وَهُمۡ يَعۡلَمُونَ

Ndipo ndithu mwa iwo muli gulu lomwe likukhotetsa malirime awo (powerenga) buku kuti muwaganizire (mawu awowo) kuti ndi a m’buku la Allah); pomwe si a m’buku (la Allah). Ndipo akunena: “Izi zachokera kwa Allah.” Pomwe zimenezo sizinachokere kwa Allah; ndipo akumnamizira Allah uku akudziwa. info
التفاسير:

external-link copy
79 : 3

مَا كَانَ لِبَشَرٍ أَن يُؤۡتِيَهُ ٱللَّهُ ٱلۡكِتَٰبَ وَٱلۡحُكۡمَ وَٱلنُّبُوَّةَ ثُمَّ يَقُولَ لِلنَّاسِ كُونُواْ عِبَادٗا لِّي مِن دُونِ ٱللَّهِ وَلَٰكِن كُونُواْ رَبَّٰنِيِّـۧنَ بِمَا كُنتُمۡ تُعَلِّمُونَ ٱلۡكِتَٰبَ وَبِمَا كُنتُمۡ تَدۡرُسُونَ

Sikoyenera kwa munthu yemwe Allah wampatsa buku ndi chiweruzo ndi uneneri, kenako nanena kwa anthu: “Khalani opembedza ine, mmalo mwa Allah.” Koma (awauze): “Khalani opembedza Allah, anzeru, aluntha chifukwa choti mukuphunzitsa buku ndi chifukwanso cha zomwe mukaphunzira.” info
التفاسير:

external-link copy
80 : 3

وَلَا يَأۡمُرَكُمۡ أَن تَتَّخِذُواْ ٱلۡمَلَٰٓئِكَةَ وَٱلنَّبِيِّـۧنَ أَرۡبَابًاۚ أَيَأۡمُرُكُم بِٱلۡكُفۡرِ بَعۡدَ إِذۡ أَنتُم مُّسۡلِمُونَ

Ndipo sangakulamulireni kuwasandutsa angelo ndi aneneri kukhala milungu. Kodi angakulamulireni kusakhulupirira pambuyo poti muli Asilamu (ogonjera)? info
التفاسير:

external-link copy
81 : 3

وَإِذۡ أَخَذَ ٱللَّهُ مِيثَٰقَ ٱلنَّبِيِّـۧنَ لَمَآ ءَاتَيۡتُكُم مِّن كِتَٰبٖ وَحِكۡمَةٖ ثُمَّ جَآءَكُمۡ رَسُولٞ مُّصَدِّقٞ لِّمَا مَعَكُمۡ لَتُؤۡمِنُنَّ بِهِۦ وَلَتَنصُرُنَّهُۥۚ قَالَ ءَأَقۡرَرۡتُمۡ وَأَخَذۡتُمۡ عَلَىٰ ذَٰلِكُمۡ إِصۡرِيۖ قَالُوٓاْ أَقۡرَرۡنَاۚ قَالَ فَٱشۡهَدُواْ وَأَنَا۠ مَعَكُم مِّنَ ٱلشَّٰهِدِينَ

Ndipo (kumbukirani) pamene Allah adatenga lonjezo kwa aneneri, (n’kuwauza): “Ndikakupatsani buku ndi nzeru, nakudzerani Mtumiki wotsimikizira zomwe zili pamodzi ndi inu, mudzamkhulupirire ndi kumthangata.” (Allah) adatinso: “Kodi mwavomereza ndi kulandira pa zimenezi pangano langali?” (Iwo) adati: “Tavomereza.” (Iye) adati: “Tsono chitirani umboni, ine ndili pamodzi nanu mwa oikira umboni.” info
التفاسير:

external-link copy
82 : 3

فَمَن تَوَلَّىٰ بَعۡدَ ذَٰلِكَ فَأُوْلَٰٓئِكَ هُمُ ٱلۡفَٰسِقُونَ

Ndipo amene adzatembenuke pambuyo pa lonjezoli, (Allah adzawalanga chifukwa chakuti) iwo ngopandukiradi chilamulo cha Allah. info
التفاسير:

external-link copy
83 : 3

أَفَغَيۡرَ دِينِ ٱللَّهِ يَبۡغُونَ وَلَهُۥٓ أَسۡلَمَ مَن فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ طَوۡعٗا وَكَرۡهٗا وَإِلَيۡهِ يُرۡجَعُونَ

Kodi akufuna chipembedzo chomwe si cha Allah pomwe chinthu chilichonse chili kumwamba ndi pansi chikugonjera Iye, mofuna kapena mosafuna? Ndipo onse adzabwezedwa kwa Iye. info
التفاسير: