[80] Tsono amene savomereza Allah potsatira malamulo ake ndi kusiya zomwe lye adaletsa, ngakhale atachita zabwino zotani sakamlipira pa tsiku lachimaliziro. Ngati nkofunika kuti amulipire, ndiye kuti amulipiliratu pompano pa dziko lapansi.
[81] Chimodzi mwa zinthu zazikulu chomwe chimachititsa kuti zochita za anthu zitheke kapena kuti zilongosoke, ndiko kuzikonza zinthuzo mwa chinsinsi. Zioneke pamaso pa anthu zili zothaitha kuzikonza. Chifukwa pali anthu ambiri oipa maganizo omwe safuna kuti zinthu za anzawo zilongosoke. Iwo amafunitsitsa kuti aziononge zisanachitike. Ndipo nchifukwa chake apa akuletsa kuwaululira zachinsinsi anthu omwe sali Asilamu, kapena kuwachita kukhala abwenzi enieni.
Komatu sikuti apa akuletsa ubwenzi wakuti: “Muli bwanji? Tili bwino”. Ndiponso sakuletsa kuwachitira zabwino ndi zachilungamo, monga momwe afotokozera pandime yachisanu nchitatu yam’surat Mumtahina. (Qur’an 60:8)
[82] M’ndime iyi akuwauza kuti asaope ufiti ngakhale kulodzedwa. Koma ayadzamire kwa Allah basi. Chimene Allah wafuna chimachitika. Palibe amene angachitsekereze. Choncho m’bale wanga moyo wako ukhale wokhazikika. Ngati ufuna kuchita chinthu usaope mfiti, wadumbo ndi mdani. dziwa kuti chimene Allah walemba sichingafafanizidwe.
[83] Apa akunena nkhani ya nkhondo yachiwiri yaikulu kwabasi pambiri ya Chisilamu, nkhondo ya Uhudi. Nkhondo imeneyi Asilamu adakumana ndi masautso akulu chifukwa cha Asilamu ena amene adaswa lamulo la Mtumiki (s.a.w). Ndiponso chifukwa cha anthu ena omwe adalowa Chisilamu mwachiphamaso, (achiphamaso) omwe adapita ku nkhondo pamodzi ndi Mtumiki (s.a.w) koma adakathawa kunkhondoko. Ndipo adali ochuluka gawo limodzi mwa magawo atatu a Asilamu (1/3). Pothawapo adathawa ochuluka kuposa nambala yatchulidwayi. Koma ena mwa iwo adabwerera nkudzalumikizananso ndi gulu la nkhondo la Mtumiki (s.a.w).