Prijevod značenja časnog Kur'ana - Prijevod na čeva jezik - Halid Ibrahim Betala

Broj stranice:close

external-link copy
30 : 3

يَوۡمَ تَجِدُ كُلُّ نَفۡسٖ مَّا عَمِلَتۡ مِنۡ خَيۡرٖ مُّحۡضَرٗا وَمَا عَمِلَتۡ مِن سُوٓءٖ تَوَدُّ لَوۡ أَنَّ بَيۡنَهَا وَبَيۡنَهُۥٓ أَمَدَۢا بَعِيدٗاۗ وَيُحَذِّرُكُمُ ٱللَّهُ نَفۡسَهُۥۗ وَٱللَّهُ رَءُوفُۢ بِٱلۡعِبَادِ

Tsiku lomwe mzimu uliwonse udzapeza zabwino zomwe udachita zitabweretsedwa, ndiponso zoipa zomwe udachita; udzalakalaka kuti pakadakhala ntunda wautali pakati pa machimo ake ndi iye. Ndipo Allah Mwini akukuchenjezani za chilango Chake. Ndipo Allah Ngoleza kwa akapolo Ake.[64] info

[64] Tsiku la chimaliziro (Qiyâma) munthu adzalakalaka kuti asawaone machimo ake amene adachita. Koma kuti machimowo akhale kutali ndi iye pomwe machimowo akamawachita amakhala wosangalala.

التفاسير:

external-link copy
31 : 3

قُلۡ إِن كُنتُمۡ تُحِبُّونَ ٱللَّهَ فَٱتَّبِعُونِي يُحۡبِبۡكُمُ ٱللَّهُ وَيَغۡفِرۡ لَكُمۡ ذُنُوبَكُمۡۚ وَٱللَّهُ غَفُورٞ رَّحِيمٞ

Nena: (Iwe Mtumiki) “Ngati inu mukumkonda Allah, tsatani ine; Allah akukondani ndikukukhululukirani machimo anu. Ndipo Allah Ngokhululuka, Ngwachisoni chosatha.”[65] info

[65] Kungonena chabe pakamwa kuti ndikumkonda mtumiki Muhammad (s.a.w) pomwe zochita zako nzosalingana ndi malangizo a mtumiki Muhammad (s.a.w), chikondi chotere chilibe phindu la mtundu uliwonse. Ngati Muhammad (s.a.w) tikumkondadi timumvere ndi kumuyesa chitsanzo chathu pa zochita zathu zonse.

التفاسير:

external-link copy
32 : 3

قُلۡ أَطِيعُواْ ٱللَّهَ وَٱلرَّسُولَۖ فَإِن تَوَلَّوۡاْ فَإِنَّ ٱللَّهَ لَا يُحِبُّ ٱلۡكَٰفِرِينَ

Nena: “Mvereni Allah ndi Mtumiki (wake).” Koma ngati akana, (Allah awakhaulitsa). Ndithudi, Allah sakonda anthu osakhulupirira. info
التفاسير:

external-link copy
33 : 3

۞ إِنَّ ٱللَّهَ ٱصۡطَفَىٰٓ ءَادَمَ وَنُوحٗا وَءَالَ إِبۡرَٰهِيمَ وَءَالَ عِمۡرَٰنَ عَلَى ٱلۡعَٰلَمِينَ

Ndithudi Allah adasankha Adam ndi Nuh ndi banja la Ibrahim ndi banja la Imran pa zolengedwa zonse. info
التفاسير:

external-link copy
34 : 3

ذُرِّيَّةَۢ بَعۡضُهَا مِنۢ بَعۡضٖۗ وَٱللَّهُ سَمِيعٌ عَلِيمٌ

Ana ena kuchokera mwa ena pakati pawo. Ndipo Allah Ngwakumva, Ngodziwa.[66] info

[66] Ndime iyi ikusonyeza kuti mawere awa ali olumikizana. Ndipo ikusonyeza kuti anthu abwino ambiri amabala anthu abwino.Tero amene akufuna kukwatira asankhe nyumba yabwino yachipembedzo, yamaphunziro ndi yaluso.

التفاسير:

external-link copy
35 : 3

إِذۡ قَالَتِ ٱمۡرَأَتُ عِمۡرَٰنَ رَبِّ إِنِّي نَذَرۡتُ لَكَ مَا فِي بَطۡنِي مُحَرَّرٗا فَتَقَبَّلۡ مِنِّيٓۖ إِنَّكَ أَنتَ ٱلسَّمِيعُ ٱلۡعَلِيمُ

(Kumbukirani) pamene adanena mkazi wa Imran (mayi wa Mariya), m’mapemphero ake): “Mbuye wanga! Ndapereka kwa Inu chimene chili m’mimba mwanga monga “waqf” (wotumikira m’kachisi Wanu). Tero landirani ichi kwa ine. Ndithudi, Inu ndinu Akumva, Wodziwa.”[67] info

[67] (Ndime 35-36) Mkazi wa Imran pamene adali ndi pakati, ankaganiza kuti adzabereka mwana wa mwamuna. Ndipo adalonjeza kwa Allah kuti mwanayo adzampereka kuti akhale wotumikira ku msikiti wa Baiti Limakadasi (Yelusalemu), ndi kutinso adzatumikire pa zinthu zina za chipembedzo. Ntchito yake idzangokhala yokhayo. Koma mmalomwake adabereka mwana wamkazi. Ndipo kuti adzakhale mwana wabwino nkutinso adzabereke ana abwino, adamutcha dzina loti Mariya (wotumikira Allah). Tero mayi Mariya adali mayi wabwino. Ndipo nayenso adabala mwana wabwino yemwe ndi mneneri Isa (Yesu). Mariya ndi mayi wolemekezeka kwabasi.

التفاسير:

external-link copy
36 : 3

فَلَمَّا وَضَعَتۡهَا قَالَتۡ رَبِّ إِنِّي وَضَعۡتُهَآ أُنثَىٰ وَٱللَّهُ أَعۡلَمُ بِمَا وَضَعَتۡ وَلَيۡسَ ٱلذَّكَرُ كَٱلۡأُنثَىٰۖ وَإِنِّي سَمَّيۡتُهَا مَرۡيَمَ وَإِنِّيٓ أُعِيذُهَا بِكَ وَذُرِّيَّتَهَا مِنَ ٱلشَّيۡطَٰنِ ٱلرَّجِيمِ

Choncho pamene adam’bala adati: “Mbuye wanga! Ndabala wamkazi!” Ndipo Allah akudziwa kwambiri chimene wabereka - “Ndipo wamwamuna (yemwe ndimayembekezera kubala) sali ngati wamkazi (amene ndamubala. Sangathe kutumikira moyenera mkachisi Wanu). Ndipo ine ndamutcha Mariya (wotumikira Allah). Ndipo ndikupempha Chitetezo Chanu pa iye ndi ana ake kwa satana wothamangitsidwayo.” info
التفاسير:

external-link copy
37 : 3

فَتَقَبَّلَهَا رَبُّهَا بِقَبُولٍ حَسَنٖ وَأَنۢبَتَهَا نَبَاتًا حَسَنٗا وَكَفَّلَهَا زَكَرِيَّاۖ كُلَّمَا دَخَلَ عَلَيۡهَا زَكَرِيَّا ٱلۡمِحۡرَابَ وَجَدَ عِندَهَا رِزۡقٗاۖ قَالَ يَٰمَرۡيَمُ أَنَّىٰ لَكِ هَٰذَاۖ قَالَتۡ هُوَ مِنۡ عِندِ ٱللَّهِۖ إِنَّ ٱللَّهَ يَرۡزُقُ مَن يَشَآءُ بِغَيۡرِ حِسَابٍ

Choncho Mbuye wake adamulandira, kulandira kwabwino; namkulitsa, kukulitsa kwabwino. Adampatsa Zakariya kuti amulere. Nthawi iliyonse Zakariya akamulowera mchipinda mwake (mwa Mariya) m’kachisimo, amampeza ali ndi chakudya. Amati: “Iwe Mariya! Ukuzipeza kuti izi?” (Iye) amati: “Izi zikuchokera kwa Allah. Ndipo Allah amampatsa yemwe wamfuna popanda chiyembekezo (mwini wakeyo).”[68] info

[68] Bambo Imran, tate wake wa Mariya, adali munthu wamkulu mwa anthu akuluakulu owopa Allah panthawiyo. Atamubala mwana wakeyu iye adamwalira. Choncho akuluakulu amene adali naye pamodzi, anapikisana pankhani yolera Mariya. Kenako adagwirizana kuti achite mayere. Amene amgwere ndiyemwe alere Mariya. Tero mayerewo adakomera mneneri Zakariya, mwamuna wa mayi wake wamng’ono wa Mariya. Ndipo Allah adamsonyeza Zakariya zododometsa zambiri kwa mwanayo. Zina mwa zododometsa ndiko kupeza chakudya pamalo pomwe ankakhala mwanayo chomwe chidali chosadziwika kwa anthu kumene chachokera. Ndipo akamufunsa amati Allah ndiye wampatsa.

التفاسير: