[64] Tsiku la chimaliziro (Qiyâma) munthu adzalakalaka kuti asawaone machimo ake amene adachita. Koma kuti machimowo akhale kutali ndi iye pomwe machimowo akamawachita amakhala wosangalala.
[65] Kungonena chabe pakamwa kuti ndikumkonda mtumiki Muhammad (s.a.w) pomwe zochita zako nzosalingana ndi malangizo a mtumiki Muhammad (s.a.w), chikondi chotere chilibe phindu la mtundu uliwonse. Ngati Muhammad (s.a.w) tikumkondadi timumvere ndi kumuyesa chitsanzo chathu pa zochita zathu zonse.
[66] Ndime iyi ikusonyeza kuti mawere awa ali olumikizana. Ndipo ikusonyeza kuti anthu abwino ambiri amabala anthu abwino.Tero amene akufuna kukwatira asankhe nyumba yabwino yachipembedzo, yamaphunziro ndi yaluso.
[67] (Ndime 35-36) Mkazi wa Imran pamene adali ndi pakati, ankaganiza kuti adzabereka mwana wa mwamuna. Ndipo adalonjeza kwa Allah kuti mwanayo adzampereka kuti akhale wotumikira ku msikiti wa Baiti Limakadasi (Yelusalemu), ndi kutinso adzatumikire pa zinthu zina za chipembedzo. Ntchito yake idzangokhala yokhayo. Koma mmalomwake adabereka mwana wamkazi. Ndipo kuti adzakhale mwana wabwino nkutinso adzabereke ana abwino, adamutcha dzina loti Mariya (wotumikira Allah). Tero mayi Mariya adali mayi wabwino. Ndipo nayenso adabala mwana wabwino yemwe ndi mneneri Isa (Yesu). Mariya ndi mayi wolemekezeka kwabasi.
[68] Bambo Imran, tate wake wa Mariya, adali munthu wamkulu mwa anthu akuluakulu owopa Allah panthawiyo. Atamubala mwana wakeyu iye adamwalira. Choncho akuluakulu amene adali naye pamodzi, anapikisana pankhani yolera Mariya. Kenako adagwirizana kuti achite mayere. Amene amgwere ndiyemwe alere Mariya. Tero mayerewo adakomera mneneri Zakariya, mwamuna wa mayi wake wamng’ono wa Mariya. Ndipo Allah adamsonyeza Zakariya zododometsa zambiri kwa mwanayo. Zina mwa zododometsa ndiko kupeza chakudya pamalo pomwe ankakhala mwanayo chomwe chidali chosadziwika kwa anthu kumene chachokera. Ndipo akamufunsa amati Allah ndiye wampatsa.