Prijevod značenja časnog Kur'ana - Prijevod na čeva jezik - Halid Ibrahim Betala

Broj stranice:close

external-link copy
122 : 3

إِذۡ هَمَّت طَّآئِفَتَانِ مِنكُمۡ أَن تَفۡشَلَا وَٱللَّهُ وَلِيُّهُمَاۗ وَعَلَى ٱللَّهِ فَلۡيَتَوَكَّلِ ٱلۡمُؤۡمِنُونَ

(Kumbukira) pamene magulu awiri mwa inu anafunitsitsa kuti athawe (chifukwa cha mantha monga momwe adathawira achinyengo). Koma Allah adali Mtetezi wa magulu awiriwo. (Choncho adawasunga kuti asathawe). Ndipo okhulupirira ayadzamire kwa Allah Yekha basi. info
التفاسير:

external-link copy
123 : 3

وَلَقَدۡ نَصَرَكُمُ ٱللَّهُ بِبَدۡرٖ وَأَنتُمۡ أَذِلَّةٞۖ فَٱتَّقُواْ ٱللَّهَ لَعَلَّكُمۡ تَشۡكُرُونَ

Allah adakupulumutsani pa (nkhondo) ya Badri pomwe inu munali ofooka (chifukwa chakuchepa ndi kusakhala ndi zida zokwanira). Choncho opani Allah kuti mumthokoze (nthawi zonse pa zomwe akukuchitirani). info
التفاسير:

external-link copy
124 : 3

إِذۡ تَقُولُ لِلۡمُؤۡمِنِينَ أَلَن يَكۡفِيَكُمۡ أَن يُمِدَّكُمۡ رَبُّكُم بِثَلَٰثَةِ ءَالَٰفٖ مِّنَ ٱلۡمَلَٰٓئِكَةِ مُنزَلِينَ

(Kumbukira) pamene umauza okhulupirira: “Kodi sizikukukwanirani pokuonjezerani Mbuye wanu zikwi zitatu za angelo otsitsidwa?[84] info

[84] M’ndime iyi akunena kuti Asilamu pankhondo zawo zolimbana ndi anthu osakhulupilira Allah, adali kuthandizidwa ndi magulumagulu a Angelo. Angelowo amadza monga anthu ndipo amamenya nkhondo ndi mphamvu zaumunthu, osati zaungelo. Akadamenya nkhondoyo ndimphamvu yaungelo ndiye kuti mngelo mmodzi yekha akadawamaliza osakhulupilira onse psiti.

التفاسير:

external-link copy
125 : 3

بَلَىٰٓۚ إِن تَصۡبِرُواْ وَتَتَّقُواْ وَيَأۡتُوكُم مِّن فَوۡرِهِمۡ هَٰذَا يُمۡدِدۡكُمۡ رَبُّكُم بِخَمۡسَةِ ءَالَٰفٖ مِّنَ ٱلۡمَلَٰٓئِكَةِ مُسَوِّمِينَ

Inde, ngati mupirira ndi kudziteteza ku machimo, ndipo (adani anu) nakudzerani mwachangu chawo chimenechi, pamenepo Mbuye wanu adzakuonjezerani ndi zikwi zisanu za angelo odziwa kumenya nkhondo.” info
التفاسير:

external-link copy
126 : 3

وَمَا جَعَلَهُ ٱللَّهُ إِلَّا بُشۡرَىٰ لَكُمۡ وَلِتَطۡمَئِنَّ قُلُوبُكُم بِهِۦۗ وَمَا ٱلنَّصۡرُ إِلَّا مِنۡ عِندِ ٱللَّهِ ٱلۡعَزِيزِ ٱلۡحَكِيمِ

Ndipo Allah sadachite izi (potumiza angelo) koma kuti ukhale uthenga wabwino kwa inu ndi kuti pakutero mitima yanu ikhazikike ndi zimenezo. Ndipo chithandizo sichichokera (kwa wina aliyense) koma kwa Allah basi, Wamphamvu zoposa, Wanzeru zakuya. info
التفاسير:

external-link copy
127 : 3

لِيَقۡطَعَ طَرَفٗا مِّنَ ٱلَّذِينَ كَفَرُوٓاْ أَوۡ يَكۡبِتَهُمۡ فَيَنقَلِبُواْ خَآئِبِينَ

(Kuchita izi) nkuti adule gawo la osakhulupirira (kuti ena a iwo aphedwe) kapena awasambule ndi kuti abwelere ali olephera.[85] info

[85] (Ndime 127-128) Apa Allah akufotokoza zifukwa zomwe adapambanitsira Asilamu. Ndipo akusonyeza ufumu Wake kuti chimene Iye wachifuna nchomwe chingachitike, osati chomwe auje ndi auje akufuna, ngakhale Mtumiki amene. Ngabodza omwe amati chimene akutiakuti afuna chimachitika, eti chifukwa choti iwowo ngolungama kwa Allah, kapena chifukwa chakuti ngoyera. Izi sizoona.

التفاسير:

external-link copy
128 : 3

لَيۡسَ لَكَ مِنَ ٱلۡأَمۡرِ شَيۡءٌ أَوۡ يَتُوبَ عَلَيۡهِمۡ أَوۡ يُعَذِّبَهُمۡ فَإِنَّهُمۡ ظَٰلِمُونَ

Iwe ulibe chako pa izi. Mwina (Allah) angalandire kulapa kwawo kapena kuwalanga pakuti ndithu iwo ndi anthu oipa. info
التفاسير:

external-link copy
129 : 3

وَلِلَّهِ مَا فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَمَا فِي ٱلۡأَرۡضِۚ يَغۡفِرُ لِمَن يَشَآءُ وَيُعَذِّبُ مَن يَشَآءُۚ وَٱللَّهُ غَفُورٞ رَّحِيمٞ

Zonse zakumwamba ndi zapansi nza Allah; amamkhululukira amene wamfuna, ndikumulanga amene wamfuna. Komatu Allah Ngokhululuka kwambiri, Ngwachisoni chosatha. info
التفاسير:

external-link copy
130 : 3

يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ لَا تَأۡكُلُواْ ٱلرِّبَوٰٓاْ أَضۡعَٰفٗا مُّضَٰعَفَةٗۖ وَٱتَّقُواْ ٱللَّهَ لَعَلَّكُمۡ تُفۡلِحُونَ

E inu amene mwakhulupirira! Musadye Riba (chuma cha katapira), kumangoonjezeraonjezera. Ndipo opani Allah kuti mupambane.[86] info

[86] Kuipa kwina kwa malonda a katapira (Riba) ndiko kuti amangoonjezeraonjezera mpaka kuchimaliza chuma chamnzakeyo momchenjelera. Ndipo nchifukwa chake m’ndime yachiwiriyi ya 131 akunenetsa kuti ngati sasiya mchitidwe wa katapira (Riba) ndi kubweza kwa eni zomwe adalandazo, moto wa Jahanama ukuwadikira.

التفاسير:

external-link copy
131 : 3

وَٱتَّقُواْ ٱلنَّارَ ٱلَّتِيٓ أُعِدَّتۡ لِلۡكَٰفِرِينَ

Ndipo opani Moto umene wakonzedwa kwa (anthu) osakhulupirira. info
التفاسير:

external-link copy
132 : 3

وَأَطِيعُواْ ٱللَّهَ وَٱلرَّسُولَ لَعَلَّكُمۡ تُرۡحَمُونَ

Ndipo mverani Allah ndi Mtumiki kuti mumveredwe chisoni. info
التفاسير: