[84] M’ndime iyi akunena kuti Asilamu pankhondo zawo zolimbana ndi anthu osakhulupilira Allah, adali kuthandizidwa ndi magulumagulu a Angelo. Angelowo amadza monga anthu ndipo amamenya nkhondo ndi mphamvu zaumunthu, osati zaungelo. Akadamenya nkhondoyo ndimphamvu yaungelo ndiye kuti mngelo mmodzi yekha akadawamaliza osakhulupilira onse psiti.
[85] (Ndime 127-128) Apa Allah akufotokoza zifukwa zomwe adapambanitsira Asilamu. Ndipo akusonyeza ufumu Wake kuti chimene Iye wachifuna nchomwe chingachitike, osati chomwe auje ndi auje akufuna, ngakhale Mtumiki amene. Ngabodza omwe amati chimene akutiakuti afuna chimachitika, eti chifukwa choti iwowo ngolungama kwa Allah, kapena chifukwa chakuti ngoyera. Izi sizoona.
[86] Kuipa kwina kwa malonda a katapira (Riba) ndiko kuti amangoonjezeraonjezera mpaka kuchimaliza chuma chamnzakeyo momchenjelera. Ndipo nchifukwa chake m’ndime yachiwiriyi ya 131 akunenetsa kuti ngati sasiya mchitidwe wa katapira (Riba) ndi kubweza kwa eni zomwe adalandazo, moto wa Jahanama ukuwadikira.