Prijevod značenja časnog Kur'ana - Prijevod na čeva jezik - Halid Ibrahim Betala

Broj stranice:close

external-link copy
187 : 3

وَإِذۡ أَخَذَ ٱللَّهُ مِيثَٰقَ ٱلَّذِينَ أُوتُواْ ٱلۡكِتَٰبَ لَتُبَيِّنُنَّهُۥ لِلنَّاسِ وَلَا تَكۡتُمُونَهُۥ فَنَبَذُوهُ وَرَآءَ ظُهُورِهِمۡ وَٱشۡتَرَوۡاْ بِهِۦ ثَمَنٗا قَلِيلٗاۖ فَبِئۡسَ مَا يَشۡتَرُونَ

Ndipo (akumbutse) pamene Allah adamanga chipangano ndi amene adapatsidwa buku (ndi kuwauza) kuti ndithudi mudzalifotokoze mwatsatanetsatane (bukulo) kwa anthu, ndipo musadzalibise. Koma Adaliponya kumbuyo kwa misana yawo naligulitsa ndi mtengo wochepa. Taonani kuipa chimene adagula (chimene adasankha)! info
التفاسير:

external-link copy
188 : 3

لَا تَحۡسَبَنَّ ٱلَّذِينَ يَفۡرَحُونَ بِمَآ أَتَواْ وَّيُحِبُّونَ أَن يُحۡمَدُواْ بِمَا لَمۡ يَفۡعَلُواْ فَلَا تَحۡسَبَنَّهُم بِمَفَازَةٖ مِّنَ ٱلۡعَذَابِۖ وَلَهُمۡ عَذَابٌ أَلِيمٞ

Musaganize kuti amene akukondwera ndi zinthu (zoipa) zomwe achita nakonda kutamandidwa ndi zomwe sadachite, musawaganizire kuti akapulumuka. (Koma kuti) pa iwo padzakhala chilango chopweteka. info
التفاسير:

external-link copy
189 : 3

وَلِلَّهِ مُلۡكُ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِۗ وَٱللَّهُ عَلَىٰ كُلِّ شَيۡءٖ قَدِيرٌ

Ndipo ufumu wa kumwamba ndi pansi ngwa Allah; ndipo Allah Ngokhoza chilichonse. info
التفاسير:

external-link copy
190 : 3

إِنَّ فِي خَلۡقِ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ وَٱخۡتِلَٰفِ ٱلَّيۡلِ وَٱلنَّهَارِ لَأٓيَٰتٖ لِّأُوْلِي ٱلۡأَلۡبَٰبِ

Ndithudi, m’kulenga kwa kumwamba ndi dziko lapansi ndi kusinthana kwa usiku ndi usana, muli zisonyezo kwa eni nzeru, info
التفاسير:

external-link copy
191 : 3

ٱلَّذِينَ يَذۡكُرُونَ ٱللَّهَ قِيَٰمٗا وَقُعُودٗا وَعَلَىٰ جُنُوبِهِمۡ وَيَتَفَكَّرُونَ فِي خَلۡقِ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ رَبَّنَا مَا خَلَقۡتَ هَٰذَا بَٰطِلٗا سُبۡحَٰنَكَ فَقِنَا عَذَابَ ٱلنَّارِ

Omwe amakumbukira Allah, ali chiimire, ali chikhalire, ndi ali chigonere chamnthiti mwawo; namalingalira kalengedwe ka thambo ndi nthaka (mmene Allah adazilengera, uku akuti): “E Mbuye wathu! simunalenge izi mwachabe. Ulemelero Ngwanu. Tichinjirizeni ku chilango cha Moto.” info
التفاسير:

external-link copy
192 : 3

رَبَّنَآ إِنَّكَ مَن تُدۡخِلِ ٱلنَّارَ فَقَدۡ أَخۡزَيۡتَهُۥۖ وَمَا لِلظَّٰلِمِينَ مِنۡ أَنصَارٖ

“E Mbuye wathu! Ndithudi, yemwe mudzamulowetse ku Moto ndiye kuti mwamuyalutsa, ndipo sipadzakhala athandizi kwa ochita zoipa.” info
التفاسير:

external-link copy
193 : 3

رَّبَّنَآ إِنَّنَا سَمِعۡنَا مُنَادِيٗا يُنَادِي لِلۡإِيمَٰنِ أَنۡ ءَامِنُواْ بِرَبِّكُمۡ فَـَٔامَنَّاۚ رَبَّنَا فَٱغۡفِرۡ لَنَا ذُنُوبَنَا وَكَفِّرۡ عَنَّا سَيِّـَٔاتِنَا وَتَوَفَّنَا مَعَ ٱلۡأَبۡرَارِ

“E Mbuye wathu! Ndithudi, ife tamva woitana akuitanira ku chikhulupiliro kuti: ‘Khulupirirani Mbuye wanu,’ ndipo takhulupirira. E Mbuye wathu! Tikhululukireni machimo athu ndi kutifafanizira zoipa zathu, ndipo mutenge mizimu yathu tili pamodzi ndi anthu abwino.” info
التفاسير:

external-link copy
194 : 3

رَبَّنَا وَءَاتِنَا مَا وَعَدتَّنَا عَلَىٰ رُسُلِكَ وَلَا تُخۡزِنَا يَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِۖ إِنَّكَ لَا تُخۡلِفُ ٱلۡمِيعَادَ

“E, Mbuye wathu! Tipatseni zimene mudatilonjeza kupyolera mwa atumiki anu ndipo musadzatisambule tsiku lachimaliziro. Ndithudi, inu simuswa lonjezo.” info
التفاسير: