[101] Ayuda adali kuchitira zamwano Mtumiki akamawalimbikitsa olemera kuti adzithandiza osauka. Ankati: “Kodi Allah wasauka tsopano kuti ife ndife tidzimdyetsera zolengedwa zake?” Taonani momwe adali kumchitira zamwano Allah!
[103] Ayuda pamene Mtumiki (s.a.w) amawauza kuti amtsate amanena kuti: “Ife sadatilamule kutsata Mtumiki yemwe akuloleza sadaka. Koma atilamula kutsata atumiki okhawo omwe akulamula kuti sadaka zonse azisonkhanitse pamodzi kenako azitenthe ndi moto. Kapena moto udze kudzapsereza.” Zoonadi, atumiki otero adadza koma sadawatsate monga momwe Allah wanenera apa. Komabe sanawalamule kutsata atumiki otero okhawo. Kutero nkungofuna kupeza chonamizira basi.
[104] Apa anthu akuwauza kuti achite zinthu molimbika zokawalowetsa ku Munda wa mtendere ndi kupewa kuchita zinthu zokawalowetsa ku Moto. Chifukwa anthu akaponyedwa ku Moto kupyolera m’zochita zawo zoipa.