Prijevod značenja časnog Kur'ana - Prijevod na čeva jezik - Halid Ibrahim Betala

Broj stranice:close

external-link copy
71 : 3

يَٰٓأَهۡلَ ٱلۡكِتَٰبِ لِمَ تَلۡبِسُونَ ٱلۡحَقَّ بِٱلۡبَٰطِلِ وَتَكۡتُمُونَ ٱلۡحَقَّ وَأَنتُمۡ تَعۡلَمُونَ

E inu amene mwapatsidwa buku! Bwanji mukusakaniza choona ndi chabodza, ndipo mukubisa choona uku mukudziwa? info
التفاسير:

external-link copy
72 : 3

وَقَالَت طَّآئِفَةٞ مِّنۡ أَهۡلِ ٱلۡكِتَٰبِ ءَامِنُواْ بِٱلَّذِيٓ أُنزِلَ عَلَى ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَجۡهَ ٱلنَّهَارِ وَٱكۡفُرُوٓاْ ءَاخِرَهُۥ لَعَلَّهُمۡ يَرۡجِعُونَ

Ndipo gulu lina la amene adapatsidwa buku lidati (kwa anzawo): “Khulupirirani chomwe chavumbulutsidwa kwa Asilamu kumayambiliro kwa usana, ndipo chikaneni kumalekezero kwake (kwa usana) mwina angabwelere (kusiya Chisilamu).[73] info

[73] Ena mwa anthu a mabuku adalangizana pakati pawo kuti chikhulupirire chipembedzo cha Chisilamu nthawi zakummawa zokha. Ikakwana nthawi yopemphera Swala akapemphere nawo. Koma ikafika nthawi yamadzulo atuluke m’chipembedzocho ncholinga choti asokoneze Asilamu maganizo, makamaka omwe adali ofooka pomwe aone kuti anthu anzeru adalowa m’chipembedzocho, koma kenako atulukamo, nawonso mwina atuluka poganiza kuti chikadakhala chipembedzo chenicheni anthu anzeru sakadatulukamo. Izi zidali ndale za Ayuda zomwe Allah adaziulula.

التفاسير:

external-link copy
73 : 3

وَلَا تُؤۡمِنُوٓاْ إِلَّا لِمَن تَبِعَ دِينَكُمۡ قُلۡ إِنَّ ٱلۡهُدَىٰ هُدَى ٱللَّهِ أَن يُؤۡتَىٰٓ أَحَدٞ مِّثۡلَ مَآ أُوتِيتُمۡ أَوۡ يُحَآجُّوكُمۡ عِندَ رَبِّكُمۡۗ قُلۡ إِنَّ ٱلۡفَضۡلَ بِيَدِ ٱللَّهِ يُؤۡتِيهِ مَن يَشَآءُۗ وَٱللَّهُ وَٰسِعٌ عَلِيمٞ

Ndipo musakhulupirire aliyense kupatula yekhayo yemwe watsata chipembedzo chanu. (Allah adauza Mtumiki {s.a.w}), nena: “Ndithudi, chiongoko chenicheni ndi chiongoko cha Allah basi.” (Amene adapatsidwa buku Adanena kwa anzawo: “Musakhulupirire) kuti angapatsidwe aliyense zofanana ndi zomwe mwapatsidwa inu (Ayuda ndi Akhrisitu), kapena kuti angakutsutseni kwa Mbuye wanu.” (Allah adati kwa mtumiki{s.a.w}), nena: “Ndithu zabwino zonse zili m’manja mwa Allah; amazipereka kwa yemwe wamfuna. Allah ndi Mataya, Ngodziwa.” info
التفاسير:

external-link copy
74 : 3

يَخۡتَصُّ بِرَحۡمَتِهِۦ مَن يَشَآءُۗ وَٱللَّهُ ذُو ٱلۡفَضۡلِ ٱلۡعَظِيمِ

Amamsankhira chifundo Chake amene wamfuna. Ndipo Allah ndi Mwini ubwino wawukulu. info
التفاسير:

external-link copy
75 : 3

۞ وَمِنۡ أَهۡلِ ٱلۡكِتَٰبِ مَنۡ إِن تَأۡمَنۡهُ بِقِنطَارٖ يُؤَدِّهِۦٓ إِلَيۡكَ وَمِنۡهُم مَّنۡ إِن تَأۡمَنۡهُ بِدِينَارٖ لَّا يُؤَدِّهِۦٓ إِلَيۡكَ إِلَّا مَا دُمۡتَ عَلَيۡهِ قَآئِمٗاۗ ذَٰلِكَ بِأَنَّهُمۡ قَالُواْ لَيۡسَ عَلَيۡنَا فِي ٱلۡأُمِّيِّـۧنَ سَبِيلٞ وَيَقُولُونَ عَلَى ٱللَّهِ ٱلۡكَذِبَ وَهُمۡ يَعۡلَمُونَ

Ndipo mwa iwo muli anthu ena oti ukawasungitsa milumilu ya chuma, akubwezera. Ndipo mwa iwo muli ena oti ukawasungitsa “dinar” (ndalama imodzi) sangakubwezere pokhapokha upitirize kwa iye kuimilira (kulonjelera). Izi nchifukwa chakuti amanena: “Palibe njira pa ife (yotidzudzulira) chifukwa chozibera mbulizi.” Koma akumnamizira Allah uku iwo akudziwa. info
التفاسير:

external-link copy
76 : 3

بَلَىٰۚ مَنۡ أَوۡفَىٰ بِعَهۡدِهِۦ وَٱتَّقَىٰ فَإِنَّ ٱللَّهَ يُحِبُّ ٱلۡمُتَّقِينَ

Sichoncho (monga momwe akunenera)! Koma amene akukwaniritsa lonjezo lake napewa machimo (ndiyemwe ayenera kukhala wokondedwa kwa Allah). Ndithudi, Allah amakonda opewa machimo. info
التفاسير:

external-link copy
77 : 3

إِنَّ ٱلَّذِينَ يَشۡتَرُونَ بِعَهۡدِ ٱللَّهِ وَأَيۡمَٰنِهِمۡ ثَمَنٗا قَلِيلًا أُوْلَٰٓئِكَ لَا خَلَٰقَ لَهُمۡ فِي ٱلۡأٓخِرَةِ وَلَا يُكَلِّمُهُمُ ٱللَّهُ وَلَا يَنظُرُ إِلَيۡهِمۡ يَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِ وَلَا يُزَكِّيهِمۡ وَلَهُمۡ عَذَابٌ أَلِيمٞ

Ndithu anthu amene akusinthanitsa chipangano cha Allah ndi malumbiliro awo, (ndi zinthu za) mtengo wochepa, iwo alibe gawo labwino pa tsiku lachimaliziro. Ndipo Allah sadzawayankhula (ndi mawu abwino); ndipo sadzawayang’ana (ndi diso la chifundo) pa tsiku lachimaliziro. Ndiponso sadzawayeretsa (kumachimo awo); ndipo iwo adzapeza chilango chopweteka. info
التفاسير: