Prijevod značenja časnog Kur'ana - Prijevod na čeva jezik - Halid Ibrahim Betala

Broj stranice:close

external-link copy
109 : 3

وَلِلَّهِ مَا فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَمَا فِي ٱلۡأَرۡضِۚ وَإِلَى ٱللَّهِ تُرۡجَعُ ٱلۡأُمُورُ

Chilichonse cha kumwamba ndipansi ncha Allah. ndipo zinthu zonse zidzabwezedwa kwa Allah. info
التفاسير:

external-link copy
110 : 3

كُنتُمۡ خَيۡرَ أُمَّةٍ أُخۡرِجَتۡ لِلنَّاسِ تَأۡمُرُونَ بِٱلۡمَعۡرُوفِ وَتَنۡهَوۡنَ عَنِ ٱلۡمُنكَرِ وَتُؤۡمِنُونَ بِٱللَّهِۗ وَلَوۡ ءَامَنَ أَهۡلُ ٱلۡكِتَٰبِ لَكَانَ خَيۡرٗا لَّهُمۚ مِّنۡهُمُ ٱلۡمُؤۡمِنُونَ وَأَكۡثَرُهُمُ ٱلۡفَٰسِقُونَ

Inu (Asilamu) ndinu gulu labwino limene lasankhidwa kwa anthu. Mukulamula (kuchita) zabwino ndi kuletsa zoipa, ndipo mukukhulupirira mwa Allah. Ndipo aja adapatsidwa buku akadakhulupirira monga momwe (adawalamulira) kukadakhala kwabwino kwa iwo. (Koma) mwa iwo alipo okhulupirira pomwe ambiri mwa iwo ngopandukira (chilamulo cha Allah).[78] info

[78] Apa akutchula zifukwa zomwe chipembedzo cha Chisilamu chapambanira zipembedzo zina. Tero tiyeni tigwirizane ndizimenezi kuti tikhaledi opambana.

التفاسير:

external-link copy
111 : 3

لَن يَضُرُّوكُمۡ إِلَّآ أَذٗىۖ وَإِن يُقَٰتِلُوكُمۡ يُوَلُّوكُمُ ٱلۡأَدۡبَارَ ثُمَّ لَا يُنصَرُونَ

Sangakuvutitseni (adani anuwo, makamaka Ayuda) koma ndi timasautso (tochepa); ngati (atayesera) kukuthirani nkhondo, akufulatirani (kuthawa); ndipo kenako sangapulumutsidwe. info
التفاسير:

external-link copy
112 : 3

ضُرِبَتۡ عَلَيۡهِمُ ٱلذِّلَّةُ أَيۡنَ مَا ثُقِفُوٓاْ إِلَّا بِحَبۡلٖ مِّنَ ٱللَّهِ وَحَبۡلٖ مِّنَ ٱلنَّاسِ وَبَآءُو بِغَضَبٖ مِّنَ ٱللَّهِ وَضُرِبَتۡ عَلَيۡهِمُ ٱلۡمَسۡكَنَةُۚ ذَٰلِكَ بِأَنَّهُمۡ كَانُواْ يَكۡفُرُونَ بِـَٔايَٰتِ ٱللَّهِ وَيَقۡتُلُونَ ٱلۡأَنۢبِيَآءَ بِغَيۡرِ حَقّٖۚ ذَٰلِكَ بِمَا عَصَواْ وَّكَانُواْ يَعۡتَدُونَ

Adindidwa chidindo chakunyozeka paliponse pamene angapezeke kupatula (akagwira) chingwe (cha chipembedzo) cha Allah, kapena chingwe cha anthu (pothandizidwa ndi anthu ena. Koma paokha sangakhale ndi nyonga). Abwerera ndi mkwiyo wa Allah; ndipo chidindo chaumphawi chadindidwa pa iwo. Izi nchifukwa chakuti iwo sadali kukhulupirira mawu a Allah, ndipo amapha aneneri popanda choonadi. Izi nchifukwa chakutinso adanyoza ndi kulumpha malire. info
التفاسير:

external-link copy
113 : 3

۞ لَيۡسُواْ سَوَآءٗۗ مِّنۡ أَهۡلِ ٱلۡكِتَٰبِ أُمَّةٞ قَآئِمَةٞ يَتۡلُونَ ءَايَٰتِ ٱللَّهِ ءَانَآءَ ٱلَّيۡلِ وَهُمۡ يَسۡجُدُونَ

Iwo amene adapatsidwa buku sali ofanana. Mwa iwo muli anthu olungama omwe akuwerenga ma Ayah (ndime) a Allah nthawi za usiku uku akumulambira. info
التفاسير:

external-link copy
114 : 3

يُؤۡمِنُونَ بِٱللَّهِ وَٱلۡيَوۡمِ ٱلۡأٓخِرِ وَيَأۡمُرُونَ بِٱلۡمَعۡرُوفِ وَيَنۡهَوۡنَ عَنِ ٱلۡمُنكَرِ وَيُسَٰرِعُونَ فِي ٱلۡخَيۡرَٰتِۖ وَأُوْلَٰٓئِكَ مِنَ ٱلصَّٰلِحِينَ

Amakhulupirira Allah ndi lsiku lomaliza; ndipo amalamulira (kuchita) zabwino ndikuletsa zoipa; ndipo amachita changu pa zinthu zabwino. Ndipo iwo ndi omwe ali mwa anthu abwino. info
التفاسير:

external-link copy
115 : 3

وَمَا يَفۡعَلُواْ مِنۡ خَيۡرٖ فَلَن يُكۡفَرُوهُۗ وَٱللَّهُ عَلِيمُۢ بِٱلۡمُتَّقِينَ

Ndipo chabwino chilichonse chimene angachite sadzakanidwa nacho, (koma adzawalipira malipiro abwino). Ndipo Allah Ngodziwa za amene akuopa Iye.[79] info

[79] Apa akunenetsa kuti aliyense amene akuchita zabwino ndicholinga chabwino ndi kutsata lamulo la Allah, adzalipidwa pa zabwino zakezo.

التفاسير: