[76] Pa ndime iyi akulangiza kuti nthawi iliyonse munthu akhale m’chikhalidwe cha Chisilamu chokwanira popewa zoletsedwa ndi kumachita zimene alamulidwa kuchita mmene angathere, chifukwa chakuti munthu sangadziwe nthawi imene imfa ingamufikire.
[77] Ndime izi zikuwauza Asilamu onse kuti akhale ogwirizana pamodzi m’dzina lachipembedzo chawo cha Chisilamu. Asapatukane popatsana maina atsopano kapena kuti awa akuchokera ku dziko lakutilakuti, awa ngamtundu wakutiwakuti. Kuchita zimenezo nkulakwa kwambiri. Koma pakati pa Asilamu pakhale chimvano.