[58] Apa akunena kuti ngati anthu ali pamalo pomwe palibe wodziwa kulemba ndipo akukongozana, wokongozedwayo apereke chikole kwa wokongoza kuti achisunge wokongozayo. Ndipo adzabwezera akadzabweza ngongoleyo. Ngati atalephera kubweza ngongoleyo chikolecho chigulitsidwe ndi muweruzi nkumpatsa wokongozayo ndalama zolingana nzomwe adamkongoza. Zotsalira pa chinthu chogulitsidwacho azipereke kwa mwini chikolecho. Uwu ndiwo ubwino wachikole pa malamulo a Chisilamu. Akalephera kubweza ngongoleyo chinthucho chimagulitsidwa ndi boma ndikumpatsa mwini ngongoleyo choyenerana naye pomwe chotsaliracho amachipereka kwa mwini wake. Kwa amene wagwirizira chikolecho saloledwa kuchita nacho chilichonse. Ngati akuchita nacho ntchito nkumachidyelera ndiye kuti akuchita machitidwe akatapira omwe ali oletsedwa. Koma chinthucho angochisunga.
[59] (Ndime 285-286) ndime ziwirizi zili ndi ubwino ndi madalitso ambiri monga momwe ilili ndime ya Ayatu Kursii yanambala 255 m’sura yomweyi.
Akutilangiza kuziwerenga ndimezi m’malo monse momwe Ayatu Kursii imawerengedwa. Qur’an yonse ikuphunzitsa asilamu kuti asasiyanitse pakati pa aneneri. Koma awavomereze onse ndi kuwakhulupilira amene adadza patsogolo pa Mtumiki Muhammad (s.a.w). Mtumiki Muhammad (s.a.w) ndiye womaliza mwa aneneriwo. Ndipo amadziwika ndi dzina lakuti “Khatamu nNabiyyina’’ “womaliza mwa Aneneri.” Ndipo amene sakhulupilira kuti Muhammad (s.a.w) ngomaliza mwa aneneri nakhulupilira munthu wamba yemwe akungodzinamiza kuti iye ndi mneneri, monga momwe chikhulupiliro cha Akadiyani chilili ndiye kuti iyeyo watuluka m’Chisilamu ndipo ndi munthu wakunja.
Asilamu sakana mneneri aliyense mwa Aneneri omwe adalipo Mtumiki Muhammad (s.a.w) asanadze. Koma iwo amakhulupilira kuti malamulo akayendetsedwe ka zipembedzo zawo kadafafanizidwa chifukwa chakudza kwa mtumiki Muhammad (s.a.w). Nyengo ino ndinyengo yotsatira mtumiki Muhammad (s.a.w) pazochitachita. Koma pazinthu zokhudza chikhulupiliro, Aneneri onse adadza ndi lamulo limodzi monga momwe Allah akufotokozera m’ndime ya 13, Sûrat Shura.
Ndipo m’ndime zimenezi za 285 ndi 286 zikuphunzitsanso miyambo ya Chisilamu ndi mapemphero (maduwa) momwe tingampemphere Allah. Ndimezi zikufotokoza za chisomo cha Allah chomwe chili pa ife anthu Ake kuti Allah sakakamiza koma chimene angathe kuchichita akapolo Ake. Ndiponso sawalanga ngati atachita zinthu molakwitsa kapena moiwala.
Ndime ziwirizi zikusonyeza makhalidwe a Asilamu ndi zinthu zawo zimene amazikhulupilira.