[12] Chikhulupiliro cha munthu kuti chikhale champhamvu ndi chopindula pafunika kuti achidziwe bwinobwino chimene akuchikhulupiliracho. Asangotsatira ndikuchikhulupilira chifukwa choti auje ndi auje adali kuchikhulupilira chimenecho. Zinthu zotere zimawasokeretsa anthu ambiri. Anthu ena amachikhulupilira chinthu chifukwa chakuti makolo awo adali kuchikhulupilira pomwe chinthucho chili chachabe.
Allah adatipatsa dalitso lanzeru kuti tizirigwilitsira ntchito pofuna choonadi cha zinthu, osati kumangotsatira ngati wakhungu.
[13] Apa Allah akutiuza kuti zinthu zinaizi nzoletsedwa kudya koma ngati munthu atavutika kwambiri ndi njala yofuna kufanayo (ndipo kulibe kopeza chakudya chovomerezeka), akumlola kuzidya pamuyeso wothetsa njalayo, osati mokhutitsa.
Chimene chadulidwa pochitchulira dzina lomwe si la Allah monga nyama zomwe zikuzingidwira kukwanitsa maloto a azimu, kapena yomwe yazingidwa chifukwa chotsilika nyumba, kapena kutsilika midzi, ndi zina zomwe zikuzingidwa kuti satana asawavutitse; zonsezi nzoletsedwa.
[14] Ibunu Abbas adati ndime iyi ikufotokoza za atsogoleri a Chiyuda monga Kaabi bun Ashirafi ndi Maliki bun Swaifi ndi Huyaye bun Akhatwabi. Anthuwa adali kulandira mphatso zambiri zochokera kwa anthu awo owatsatira. Pamene Muhammad (s.a.w) adampatsa uneneri iwo sadakhulupirire chifukwa choopa kuti sapeza mitulo yochokera kwa anthu awo. Tero anabisa kwa anthu za uneneri wa Muhammad (s.a.w). Apa mpamene Allah adavumbulutsa Ayah (ndime) iyi, yakuti “Ndithudi, amene akubisa zomwe Allah adavumbulutsa m’buku (la Baibulo) m’malo mwake nasankha zinthu za mtengo wochepa iwo sadya china m’mimba mwawo koma moto basi.”