[50] M’nthawi ya mneneri Ibrahim padali mfumu ina yodzikuza yomwe inkadzitcha kuti ndimulungu ndipo anthu ake adali kuipembedza. Pamene mneneri Ibrahim adadza nayamba kuphunzitsa chipembedzo choona ndikuti iyeyo si mulungu, mfumuyo idati kwa mneneri Ibrahim: “Kodi Mulungu wako woonayo amachita chiyani?” Iye adati “Amapereka moyo ndi kuperekanso imfa.” Mfumuyo idachita ngati sidamvetse cholinga cha mawu a mneneri Ibrahim. Idati: “Nanenso ndimachita zimenezo. Taona mmene ndimachitira.” Pompo adalamula kuti abwere nawo anthu awiri omwe adawalamula kuti aphedwe. Iye adalamula kuti mmodzi aphedwe ndipo winayo amsiye. Choncho zidachitika. Tsono adamuuza Ibrahim: “Waona bwanji? Kodi wina sindidampatse moyo ndipo winayo imfa?” Mneneri Ibrahim pomwe anaona kuti mfumuyo ikungodzipusitsa daladala adaiuza chinthu chomwe iyo sikadatha kuchichita. Adati: “Allah amatulutsa dzuwa ku vuma ndipo iwe ulitulutse ku zambwe.” Pamenepo mfumuyo idangoti kakasi, sidachite chilichonse ndiponso sidanene chilichonse.