[28] Apa Allah akufotokoza kuti msilamu aliyense adzapeza mavuto pokwaniritsa Chisilamu chake. Palibe chinthu chopindulitsa chimene chimangopezeka mofewa. Mavuto ndi amene amamkonza munthu kuti akhale olimba. Choncho, munthu asaganize kuti adzapeza chinthu chamtengo wapatali popanda kuchivutikira.
[29] Adafunsa izi lisanadze lamulo lakagawidwe ka chuma chamasiye. Pamene lidadza lamulo la kagawidwe ka chuma chamasiye lidaletsa kupereka wasiya (chilawo) kwa anthu owagawira chumacho, chifukwa chakuti aliyense wa iwo Allah adampatsa gawo lakelake. Koma ngati munthu ukufuna kupereka wasiya (chilawo) pachuma chako, pereka wasiyawo iwe usanafe ndipo gawo la wasiyawo lisapyole pa 1/3.