[11] E inu anthu! Idyani za mdziko lapansi zomwe zili zabwino zimene Allah wakulolezani ndipo musapenekere chilolezo chake. Musadye chinthu chosaloledwa monga kudya chinthu cha wina m’njira ya chinyengo. Musakwatule chuma chamnzanu.
Ndipo chenjerani ndi njira za satana yemwe amakukometserani zoipa. Dziwani kuti iyeyu ndi mdani wanu monga adalili mdani watate wanu Adam. Dziwaninso kuti satanayo salamula kuchita zabwino koma zoipa zokhazokha.