क़ुरआन के अर्थों का अनुवाद - चेवा अनुवाद - ख़ालिद अबराहीम बेताला

पृष्ठ संख्या:close

external-link copy
265 : 2

وَمَثَلُ ٱلَّذِينَ يُنفِقُونَ أَمۡوَٰلَهُمُ ٱبۡتِغَآءَ مَرۡضَاتِ ٱللَّهِ وَتَثۡبِيتٗا مِّنۡ أَنفُسِهِمۡ كَمَثَلِ جَنَّةِۭ بِرَبۡوَةٍ أَصَابَهَا وَابِلٞ فَـَٔاتَتۡ أُكُلَهَا ضِعۡفَيۡنِ فَإِن لَّمۡ يُصِبۡهَا وَابِلٞ فَطَلّٞۗ وَٱللَّهُ بِمَا تَعۡمَلُونَ بَصِيرٌ

Ndipo fanizo la anthu amene akupereka chuma chawo chifukwa chofuna chiyanjo cha Allah ndi kulimbikitsa mitima yawo (pa chipembedzo cha Allah) lili ngati fanizo la munda umene uli pachitunda, chiufikira chimvula tero nubweretsa zinthu zake dzochuluka moonjeza kawiri (kuposera pachikhalidwe chake). Ndipo ngati chimvula sichidaudzere, ndiye kuti yamawawa (nkuukwanira mundawo). Ndipo Allah akuona zonse zimene mukuchita. info
التفاسير:

external-link copy
266 : 2

أَيَوَدُّ أَحَدُكُمۡ أَن تَكُونَ لَهُۥ جَنَّةٞ مِّن نَّخِيلٖ وَأَعۡنَابٖ تَجۡرِي مِن تَحۡتِهَا ٱلۡأَنۡهَٰرُ لَهُۥ فِيهَا مِن كُلِّ ٱلثَّمَرَٰتِ وَأَصَابَهُ ٱلۡكِبَرُ وَلَهُۥ ذُرِّيَّةٞ ضُعَفَآءُ فَأَصَابَهَآ إِعۡصَارٞ فِيهِ نَارٞ فَٱحۡتَرَقَتۡۗ كَذَٰلِكَ يُبَيِّنُ ٱللَّهُ لَكُمُ ٱلۡأٓيَٰتِ لَعَلَّكُمۡ تَتَفَكَّرُونَ

Kodi mmodzi wa inu angakonde kukhala ndi munda wa mitengo ya kanjedza ndi mphesa womwe pansi pake mitsinje ikuyenda, iye mmenemo napeza dzinthu dzamitundumitundu, numpeza ukalamba uku ali ndi ana ofooka; ndipo kamvuluvulu wa moto naugwera (mundawo), nupseleratu (angazikonde zimenezi)? Umo ndimomwe Allah akukulongosolerani ma Ayah (ndime za mawu Ake) kuti muganizire. info
التفاسير:

external-link copy
267 : 2

يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُوٓاْ أَنفِقُواْ مِن طَيِّبَٰتِ مَا كَسَبۡتُمۡ وَمِمَّآ أَخۡرَجۡنَا لَكُم مِّنَ ٱلۡأَرۡضِۖ وَلَا تَيَمَّمُواْ ٱلۡخَبِيثَ مِنۡهُ تُنفِقُونَ وَلَسۡتُم بِـَٔاخِذِيهِ إِلَّآ أَن تُغۡمِضُواْ فِيهِۚ وَٱعۡلَمُوٓاْ أَنَّ ٱللَّهَ غَنِيٌّ حَمِيدٌ

E inu amene mwakhulupirira! Perekani zabwino zochokera m’zimene mwapeza ndi zimene takutulutsirani m’nthaka, ndipo musalinge kupereka choipa chomwe inu simukadachilandira (ngati akanakupatsani) pokhapokha mochitsinzinira. (Nanga Allah ndiye alandire choipacho)? Ndipo dziwani kuti Allah Ngolemera (ndiponso) Ngotamandidwa. info
التفاسير:

external-link copy
268 : 2

ٱلشَّيۡطَٰنُ يَعِدُكُمُ ٱلۡفَقۡرَ وَيَأۡمُرُكُم بِٱلۡفَحۡشَآءِۖ وَٱللَّهُ يَعِدُكُم مَّغۡفِرَةٗ مِّنۡهُ وَفَضۡلٗاۗ وَٱللَّهُ وَٰسِعٌ عَلِيمٞ

Satana amakuopsezani ndi umphawi ndi kukulamulirani kuchita zoipa (monga umbombo), pomwe Allah akukulonjezani chikhululuko kuchokera kwa Iye ndi ubwino (waukulu ngati mupereka); ndipo Allah ali nazo zambiri, Ngodziwa.[54] info

[54] (Ndime 268-271) apa Allah akuwalimbikitsa mtima amene akupereka kuti panthawi iliyonse pamene akupereka Allah adzawaonjezera. Ndipo akuwachenjeza kuti asamamvetsere udyerekezi wa satana umene amauthira m’mitima yawo powauza kuti: “Ngati mupereka, musauka.” Koma Allah akuwauza kuti: “Perekani simusauka. M’malomwake mupeza bwino pa dziko lapansi ndi pa tsiku lachimaliziro.”
M’ndime zomwezi Allah wafotokoza za (lonjezo) “naziri” kuti naziri iliyonse imene tikumlonjeza Allah akuidziwa.
Mawu oti “Naziri” nga Chiarabu. M’chichewa akuthandauza kuti, “ndikapeza chakuti ndidzachita chakutichakuti,” “kapena kuti, akachira m’bale wanga ndidzapereka chakutichakuti kwa Allah.”
Mawu anaziriwa siabwino pa malamulo a Chisilamu, ngakhale kuti anthu ambiri amakonda kuchita naziri poganizira kuti akatero Allah awayankha mwachangu namaganiziranso kuti naziri nchinthu chabwino m’Chisilamu pomwe chili chosafunika m’Chisilamu.
Kusafunika kwa naziri m’Chisilamu kuli kotere: Umati: “Allah akandichitira chakutichakuti inenso ndichita chakutichakuti.” Mawu oterewa sali mawu abwino ndiponso akusonyeza kupanda mwambo ndiponso akusonyeza umbombo.
Chifukwa chakuti munthu ofuna kupereka kanthu sanganene kuti: “Muyambe mwandichitira chakuti ndipo ndikupatsani.” Koma ngakhale zili choncho akwaniritsebe malonjezowo. Koma ngati malonjezowo ali pa chinthu choletsedwa asawakwaniritse, ndipo m’malo mwake apereke dipo.

التفاسير:

external-link copy
269 : 2

يُؤۡتِي ٱلۡحِكۡمَةَ مَن يَشَآءُۚ وَمَن يُؤۡتَ ٱلۡحِكۡمَةَ فَقَدۡ أُوتِيَ خَيۡرٗا كَثِيرٗاۗ وَمَا يَذَّكَّرُ إِلَّآ أُوْلُواْ ٱلۡأَلۡبَٰبِ

Amapatsa nzeru (zothandiza) amene wamfuna; ndipo amene wapatsidwa nzeru, ndithudi, wapatsidwa zabwino zambiri. Ndipo (zoterezi) sakumbukira koma eni nzeru okha. info
التفاسير: