[37] Apa amuna akuwalangiza kuti awabwelere akazi awo mwachangu nthawi ya edda isanathe kuopa kuti ikatha ndiye kuti akwatiwa ndi amuna ena. Komatu akuwalangiza kuti abwererane nawo akaziwo ncholinga chokhala nawo mwaubwino, osati kubwererana nawo ncholinga chowavutitsa.
[38] Mwana amayamwitsidwa ndi mayi wake m’nthawi yazaka ziwiri. Ndipo akhoza kumuyamwitsa mopitilira zaka ziwiri. Ndipo mayiyo akhoza ngati atagwirizana ndi tate wamwanayo kumsiitsa zaka ziwiri zisanakwane ngati ali ndi chitsimikizo choti mwanayo sapeza masautso. Ndipo tate ngati adalekana naye ukwati mayi wa mwanayo pomwe mayiyo akupitiriza kuyamwitsa mwanayo, nkofunika kwa tate wa mwanayo kupereka malipiro kwa mayi wa mwanayo, monga kumpezera chakudya, zovala, ndalama zolipilira pamalo pokhala ndi zina zotere. Mwamuna asanene kwa mkaziyo kuti: “Uyu mwana wako. Tero uwona chochita naye.’’ Pamenepo mpovuta chifukwa mkaziyo sangapeze munthu womthandiza iye ndi mwanayo. Makamaka izi zingachitike ngati mkaziyo sanakwatiwe ndi mwamuna wina. Nayenso mayi wamwanayo asamkhwimitsire mwamunayo malipiro operekedwawo. Koma zonse zikhale zaubwino. Ngati tate wamwanayo palibe, ndiye kuti mlowam’malo wa tateyo ndiye adzakwaniritse zimenezo.