क़ुरआन के अर्थों का अनुवाद - चेवा अनुवाद - ख़ालिद अबराहीम बेताला

पृष्ठ संख्या:close

external-link copy
89 : 2

وَلَمَّا جَآءَهُمۡ كِتَٰبٞ مِّنۡ عِندِ ٱللَّهِ مُصَدِّقٞ لِّمَا مَعَهُمۡ وَكَانُواْ مِن قَبۡلُ يَسۡتَفۡتِحُونَ عَلَى ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ فَلَمَّا جَآءَهُم مَّا عَرَفُواْ كَفَرُواْ بِهِۦۚ فَلَعۡنَةُ ٱللَّهِ عَلَى ٱلۡكَٰفِرِينَ

Ndipo pamene buku lidawadzera (m’nyengo ya mtumiki Muhammad {s.a.w}) lochokera kwa Allah, loikira umboni zomwe zili pamodzi ndi iwo (adalikana), pomwe kale (lisadadze bukulo) adali kupempha chithandizo (kupyolera kwa mtumiki wolonjezedwa) chogonjetsera amene sadakhulupirire. Koma pamene chidawadzera chimene adachidziwa, (Qur’an) adachikana. Choncho matembelero a Allah ali pa osakhulupirira. info
التفاسير:

external-link copy
90 : 2

بِئۡسَمَا ٱشۡتَرَوۡاْ بِهِۦٓ أَنفُسَهُمۡ أَن يَكۡفُرُواْ بِمَآ أَنزَلَ ٱللَّهُ بَغۡيًا أَن يُنَزِّلَ ٱللَّهُ مِن فَضۡلِهِۦ عَلَىٰ مَن يَشَآءُ مِنۡ عِبَادِهِۦۖ فَبَآءُو بِغَضَبٍ عَلَىٰ غَضَبٖۚ وَلِلۡكَٰفِرِينَ عَذَابٞ مُّهِينٞ

N’choipa zedi chimene asinthanitsira (chisangalalo cha tsiku lachimaliziro cha) mitima yawo pa kukana kwao zimene Allah adavumbulutsa, chifukwa cha njiru basi kuti Allah watsitsira chifundo chake amene wamfuna mwa akapolo Ake (amene sali Myuda). Potero adabwerera ndi mkwiyo wa Allah kuonjezera pa mkwiyo wakale. Ndipo osakhulupirira adzakhala ndi chilango chosambula. info
التفاسير:

external-link copy
91 : 2

وَإِذَا قِيلَ لَهُمۡ ءَامِنُواْ بِمَآ أَنزَلَ ٱللَّهُ قَالُواْ نُؤۡمِنُ بِمَآ أُنزِلَ عَلَيۡنَا وَيَكۡفُرُونَ بِمَا وَرَآءَهُۥ وَهُوَ ٱلۡحَقُّ مُصَدِّقٗا لِّمَا مَعَهُمۡۗ قُلۡ فَلِمَ تَقۡتُلُونَ أَنۢبِيَآءَ ٱللَّهِ مِن قَبۡلُ إِن كُنتُم مُّؤۡمِنِينَ

Ndipo akauzidwa (Ayuda): “Khulupirirani zimene Allah wavumbulutsa (kwa mtumiki Muhammad {s.a.w}).” Amanena: “Tikukhulupirira zimene zidavumbulitsidwa kwa ife,” ndipo amazikana zomwe sizili zimenezo ngakhale izo zili zoona, zomwe zikutsimikizira pa zimene ali nazo pamodzi. Nena: “Nanga bwanji mudapha aneneri a Allah kalelo ngati muli okhulupiriradi?” info
التفاسير:

external-link copy
92 : 2

۞ وَلَقَدۡ جَآءَكُم مُّوسَىٰ بِٱلۡبَيِّنَٰتِ ثُمَّ ٱتَّخَذۡتُمُ ٱلۡعِجۡلَ مِنۢ بَعۡدِهِۦ وَأَنتُمۡ ظَٰلِمُونَ

Ndipo adakudzerani Mûsa ndi zisonyezo zoonekera, koma pambuyo pake mudapembedza thole (mwana wa ng’ombe), ndipo potero mudali anthu ochita zoipa kwabasi. info
التفاسير:

external-link copy
93 : 2

وَإِذۡ أَخَذۡنَا مِيثَٰقَكُمۡ وَرَفَعۡنَا فَوۡقَكُمُ ٱلطُّورَ خُذُواْ مَآ ءَاتَيۡنَٰكُم بِقُوَّةٖ وَٱسۡمَعُواْۖ قَالُواْ سَمِعۡنَا وَعَصَيۡنَا وَأُشۡرِبُواْ فِي قُلُوبِهِمُ ٱلۡعِجۡلَ بِكُفۡرِهِمۡۚ قُلۡ بِئۡسَمَا يَأۡمُرُكُم بِهِۦٓ إِيمَٰنُكُمۡ إِن كُنتُم مُّؤۡمِنِينَ

Ndipo (kumbukirani nkhani iyi, inu ana a Israyeli) pamene tidalandira kwa inu pangano lamphamvu, ndipo tidakukwezerani phiri pamwamba panu (uku tikuti): “Gwiritsani mwamphamvu (malamulo) amene takupatsani, ndipo mverani.” (Iwo) adati: “Tamva (mawu anu), koma tanyozera.” Ndipo adamwetsedwa m’mitima mwawo kukonda kupembedza thole (mwana wang’ombe) chifukwa cha kusakhulupirira kwawo. Nena: “N’choipa zedi chimene chikhulupiliro chanu chikukulamulirani ngati inu mulidi okhulupirira.” info
التفاسير: