Traduction des sens du Noble Coran - La traduction tchétchène - Khâlid Ibrâhîm Bîtâlâ

Numéro de la page:close

external-link copy
283 : 2

۞ وَإِن كُنتُمۡ عَلَىٰ سَفَرٖ وَلَمۡ تَجِدُواْ كَاتِبٗا فَرِهَٰنٞ مَّقۡبُوضَةٞۖ فَإِنۡ أَمِنَ بَعۡضُكُم بَعۡضٗا فَلۡيُؤَدِّ ٱلَّذِي ٱؤۡتُمِنَ أَمَٰنَتَهُۥ وَلۡيَتَّقِ ٱللَّهَ رَبَّهُۥۗ وَلَا تَكۡتُمُواْ ٱلشَّهَٰدَةَۚ وَمَن يَكۡتُمۡهَا فَإِنَّهُۥٓ ءَاثِمٞ قَلۡبُهُۥۗ وَٱللَّهُ بِمَا تَعۡمَلُونَ عَلِيمٞ

Ndipo ngati muli pa ulendo, ndipo simudapeze mlembi, choncho (wokongoza) apatsidwe chikole (pinyolo) m’manja mwake. Ngati wina wasungitsa mmodzi wa inu chinthu (pomudalira wokhulupirika) choncho amene wayesedwa wokhulupirikayo abweze chinthucho kwa mwini wake, ndipo aope Allah, Mbuye wake. Ndipo musabise umboni (ngakhale uli wokuipirani). Ndipo amene abise ndiye kuti mu mtima mwake mwalowa uchimo; ndipo Allah akudziwa zonse zimene mukuchita.[58] info

[58] Apa akunena kuti ngati anthu ali pamalo pomwe palibe wodziwa kulemba ndipo akukongozana, wokongozedwayo apereke chikole kwa wokongoza kuti achisunge wokongozayo. Ndipo adzabwezera akadzabweza ngongoleyo. Ngati atalephera kubweza ngongoleyo chikolecho chigulitsidwe ndi muweruzi nkumpatsa wokongozayo ndalama zolingana nzomwe adamkongoza. Zotsalira pa chinthu chogulitsidwacho azipereke kwa mwini chikolecho. Uwu ndiwo ubwino wachikole pa malamulo a Chisilamu. Akalephera kubweza ngongoleyo chinthucho chimagulitsidwa ndi boma ndikumpatsa mwini ngongoleyo choyenerana naye pomwe chotsaliracho amachipereka kwa mwini wake. Kwa amene wagwirizira chikolecho saloledwa kuchita nacho chilichonse. Ngati akuchita nacho ntchito nkumachidyelera ndiye kuti akuchita machitidwe akatapira omwe ali oletsedwa. Koma chinthucho angochisunga.

التفاسير:

external-link copy
284 : 2

لِّلَّهِ مَا فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَمَا فِي ٱلۡأَرۡضِۗ وَإِن تُبۡدُواْ مَا فِيٓ أَنفُسِكُمۡ أَوۡ تُخۡفُوهُ يُحَاسِبۡكُم بِهِ ٱللَّهُۖ فَيَغۡفِرُ لِمَن يَشَآءُ وَيُعَذِّبُ مَن يَشَآءُۗ وَٱللَّهُ عَلَىٰ كُلِّ شَيۡءٖ قَدِيرٌ

Zonse zakumwamba ndi zapansi nza Allah. Kaya muonetsera poyera zomwe zili m’mitima mwanu kapena kuzibisa, Allah adzakuchitirani nazo chiwerengero. Kenako adzakhululukira amene wamfuna (atalapa). Ndipo adzamlanga amene wamfuna (akapanda kulapa). Ndipo Allah Ngokhoza chilichonse. info
التفاسير:

external-link copy
285 : 2

ءَامَنَ ٱلرَّسُولُ بِمَآ أُنزِلَ إِلَيۡهِ مِن رَّبِّهِۦ وَٱلۡمُؤۡمِنُونَۚ كُلٌّ ءَامَنَ بِٱللَّهِ وَمَلَٰٓئِكَتِهِۦ وَكُتُبِهِۦ وَرُسُلِهِۦ لَا نُفَرِّقُ بَيۡنَ أَحَدٖ مِّن رُّسُلِهِۦۚ وَقَالُواْ سَمِعۡنَا وَأَطَعۡنَاۖ غُفۡرَانَكَ رَبَّنَا وَإِلَيۡكَ ٱلۡمَصِيرُ

Mtumiki wakhulupirira zimene zavumbulutsidwa kwa iye kuchokera kwa Mbuye wake. Naonso asilamu (akhulupirira). Onse akhulupirira Allah, angelo Ake, mabuku Ake ndi atumiki Ake. (Iwo pamodzi ndi Mtumiki wawoyo akunena kuti): “Sitingalekanitse aliyense pakati pa atumiki Ake, (onse tikuwakhulupirira).” Ndipo akunena: “Tamva ndiponso tamvera, (choncho tikukupemphani) chikhululuko chanu. E Mbuye wathu! Ndipo kwa Inu nkobwerera.”[59] info

[59] (Ndime 285-286) ndime ziwirizi zili ndi ubwino ndi madalitso ambiri monga momwe ilili ndime ya Ayatu Kursii yanambala 255 m’sura yomweyi.
Akutilangiza kuziwerenga ndimezi m’malo monse momwe Ayatu Kursii imawerengedwa. Qur’an yonse ikuphunzitsa asilamu kuti asasiyanitse pakati pa aneneri. Koma awavomereze onse ndi kuwakhulupilira amene adadza patsogolo pa Mtumiki Muhammad (s.a.w). Mtumiki Muhammad (s.a.w) ndiye womaliza mwa aneneriwo. Ndipo amadziwika ndi dzina lakuti “Khatamu nNabiyyina’’ “womaliza mwa Aneneri.” Ndipo amene sakhulupilira kuti Muhammad (s.a.w) ngomaliza mwa aneneri nakhulupilira munthu wamba yemwe akungodzinamiza kuti iye ndi mneneri, monga momwe chikhulupiliro cha Akadiyani chilili ndiye kuti iyeyo watuluka m’Chisilamu ndipo ndi munthu wakunja.
Asilamu sakana mneneri aliyense mwa Aneneri omwe adalipo Mtumiki Muhammad (s.a.w) asanadze. Koma iwo amakhulupilira kuti malamulo akayendetsedwe ka zipembedzo zawo kadafafanizidwa chifukwa chakudza kwa mtumiki Muhammad (s.a.w). Nyengo ino ndinyengo yotsatira mtumiki Muhammad (s.a.w) pazochitachita. Koma pazinthu zokhudza chikhulupiliro, Aneneri onse adadza ndi lamulo limodzi monga momwe Allah akufotokozera m’ndime ya 13, Sûrat Shura.
Ndipo m’ndime zimenezi za 285 ndi 286 zikuphunzitsanso miyambo ya Chisilamu ndi mapemphero (maduwa) momwe tingampemphere Allah. Ndimezi zikufotokoza za chisomo cha Allah chomwe chili pa ife anthu Ake kuti Allah sakakamiza koma chimene angathe kuchichita akapolo Ake. Ndiponso sawalanga ngati atachita zinthu molakwitsa kapena moiwala.
Ndime ziwirizi zikusonyeza makhalidwe a Asilamu ndi zinthu zawo zimene amazikhulupilira.

التفاسير:

external-link copy
286 : 2

لَا يُكَلِّفُ ٱللَّهُ نَفۡسًا إِلَّا وُسۡعَهَاۚ لَهَا مَا كَسَبَتۡ وَعَلَيۡهَا مَا ٱكۡتَسَبَتۡۗ رَبَّنَا لَا تُؤَاخِذۡنَآ إِن نَّسِينَآ أَوۡ أَخۡطَأۡنَاۚ رَبَّنَا وَلَا تَحۡمِلۡ عَلَيۡنَآ إِصۡرٗا كَمَا حَمَلۡتَهُۥ عَلَى ٱلَّذِينَ مِن قَبۡلِنَاۚ رَبَّنَا وَلَا تُحَمِّلۡنَا مَا لَا طَاقَةَ لَنَا بِهِۦۖ وَٱعۡفُ عَنَّا وَٱغۡفِرۡ لَنَا وَٱرۡحَمۡنَآۚ أَنتَ مَوۡلَىٰنَا فَٱنصُرۡنَا عَلَى ٱلۡقَوۡمِ ٱلۡكَٰفِرِينَ

Allah sakakamiza mzimu uliwonse koma chimene chili cholingana ndi kukhoza kwake. (Ndipo phindu la) zimene mzimuwo udapeza ndilake ndiponso kuluza kwa zomwe udapeza nkwake. (Asilamuwo amanena) “E Mbuye wathu! Musatilange tikaiwala kapena tikalakwitsa, E Mbuye wathu! Musatisenzetse mtolo (wamalamulo) monga munawasenzetsera amene adalipo patsogolo pathu. E Mbuye wathu! Musatisenzetse chimene sitingachithe. Tifafanizireni machimo athu, tikhululukireni zolakwa zathu, ndiponso tichitireni chifundo. Inu Ndinu Mtetezi wathu. Choncho tithangateni ku anthu osakhulupirira.” info
التفاسير: