[57] Apa akuwalimbikitsa anthu kuti azilemba akamakongozana zinthu kuti pasakhale mkangano ndikukanirana kuti sanakongozane. Ngakhale ngongoleyo ikhale yochepa pafunika ndithu kulemba. Ndipo polembetsa ngongoleyo wokongolayo ndiye adzinena mawu olembedwawo poopa kuti akayankhula wokongoza akhoza kuonjeza mawu ndipo wokongola nkuchita manyazi kumbweza pakuti mkono wopempha ngwapansi pomwe wopereka ngwapamwamba. Ndipo pamene wolemba akuuzidwa kuti asawakanire kuwalembera osadziwa kulemba, akutanthauza kuti anthu azithandizana pakati pawo. Ndipo olemba akuwalangizanso kuti alembe zokhazo zomwe akuuzidwa ndipo afunirepo mboni zotsimikiza kuti alembadi. Ndipo mbonizo zisainire pamenepo. Oikira umboni afunika kukhala amuna awiri a Chisilamu. Ngati palibe amuna awiriwo, mmalo mwa mwamuna mmodzi zilowe mboni ziwiri zachikazi chifukwa chikumbumtima cha akazi nchochepa poyerekeza ndi cha amuna.Ndipo anthu akuwauzanso kuti akawapempha kuti aikire umboni pa chinthu asakane. Kuikira umboni ndi ntchito yabwino yotsimikizira choona ndi kukana chonama. Koma pa malonda ogulitsana dzanja ndi dzanja sipafunika kulemba koma pamangofunika mboni basi. Ndipo pomwe kwanenedwa kuti: “Asavutitsidwe olembawo ndi oikira umboniwo,’’ akusonyeza kuti ngati ntchito yolembayo ndi kuikira umboniwo nzotenga nthawi yaitali kotero kuti olembawo ndi mbonizo iwachedwetsera ntchito zawo zomwe amapezera zowathandiza pa moyo wawo, ayenera kuwalipira.