[47] Ndime iyi ikusonyeza kuti atumiki maulemelero awo ngosiyanasiyana kwa Allah monga momwenso alili anthu ndi angelo ndi zinthu zinanso. Amaposana pakalandiridwe ka ulemelero wawo kwa Allah chifukwa chakusiyana zochita zawo. Zochita za ena nzazikulu zedi kapena zochuluka kwambiri kuposa zochita za anzawo. Ndipo apa Allah watchulapo atatu mwa atumiki akuluakulu omwe ndi:-
(a) Musa amene Allah adayankhula naye ndi kumpatsa zozizwitsa zoonekera.
(b) Ndi mneneri Isa (Yesu) yemwe adampatsa ulemelero waukulu
(c) ndi mneneri Muhammad (s.a.w). Enanso mwa aneneri akuluakulu pali mneneri Ibrahim ndi mneneri Nuh monga momwe ikufotokozera ndime ya chisanu ndi ziwiri (7) yam’surati Ahzab.
[48] Ndime iyi ikutchedwa Ayat Kursii; ndime yolemekezeka kwambiri. Kwa msilamu aliyense nkofunika kuizindikira bwinobwino ndimeyi kuti azindikire kuti palibe yemwe angamuike patsogolo kapena pambuyo koma lye Allah wapamwambamwamba. Mu hadisi zambiri za Mtumiki akutilimbikitsa kuiwerenga ndimeyi m’malo awa:-
a) tikatha kuchita salamu pa Swala iliyonse ya Faradh
b) tisanagone
c) pamene tikutuluka m’nyumba
d) polowa m’nyumba
e) tikadzazidwa ndi mantha poopa chinthu chomwe tikuchiona ndi chomwe sitikuchiona
[49] Arabu ena a mu Mzinda wa Madina, Mtumiki (madalitso ndi mtendere zikhale naye) asanasamukireko adali kutsata chipembedzo cha Chiyuda. Koma ambiri a iwo adali kupembedza mafano. Pamene chidadza Chisilamu pafupifupi onse omwe ankapembedza mafano adalowa m’ Chisilamu. Koma amene adali m’chipembedzo cha Chiyuda ndiochepa okha omwe adalowa m’Chisilamu. Ndipo ena ngakhale anali Arabu adatsalirabe m’chipembedzo cha Chiyuda. Choncho, omwe adali asilamu adafuna kukakamiza mwamphamvu amene adali m’chipembedzo cha Chiyuda kuti alowe m’Chisilamu. Koma Allah adawaletsa kuti palibe kumkakamiza kuti alowe m’Chisilamu yemwe sakufuna. Munthu aliyense adapatsidwa nzeru yomzindikiritsa chabwino ndi choipa. Ngati afuna kusokera nkufuna kwake iye mwini. Ndipo Allah adzamulanga pa tsiku lachimaliziro osati pano padziko lapansi.