Traduction des sens du Noble Coran - La traduction tchétchène - Khâlid Ibrâhîm Bîtâlâ

Numéro de la page:close

external-link copy
270 : 2

وَمَآ أَنفَقۡتُم مِّن نَّفَقَةٍ أَوۡ نَذَرۡتُم مِّن نَّذۡرٖ فَإِنَّ ٱللَّهَ يَعۡلَمُهُۥۗ وَمَا لِلظَّٰلِمِينَ مِنۡ أَنصَارٍ

Ndipo chilichonse chomwe mungapereke kapena naziri (lonjezo) iliyonse yomwe mwalonjeza Allah, ndithudi, Allah akudziwa zonsezi. Ndipo anthu ochita zoipa sadzakhala ndi athandizi. info
التفاسير:

external-link copy
271 : 2

إِن تُبۡدُواْ ٱلصَّدَقَٰتِ فَنِعِمَّا هِيَۖ وَإِن تُخۡفُوهَا وَتُؤۡتُوهَا ٱلۡفُقَرَآءَ فَهُوَ خَيۡرٞ لَّكُمۡۚ وَيُكَفِّرُ عَنكُم مِّن سَيِّـَٔاتِكُمۡۗ وَٱللَّهُ بِمَا تَعۡمَلُونَ خَبِيرٞ

Ngati mupereka sadaka moonetsera, ndibwino; ngati mungaipereke mobisa, ndikuipereka kwa osauka, umenewo ndiubwino woposa kwa inu. Ndipo akufafanizirani zoipa zanu (ngati mutero). Ndipo Allah akudziwa zonse zimene mukuchita. info
التفاسير:

external-link copy
272 : 2

۞ لَّيۡسَ عَلَيۡكَ هُدَىٰهُمۡ وَلَٰكِنَّ ٱللَّهَ يَهۡدِي مَن يَشَآءُۗ وَمَا تُنفِقُواْ مِنۡ خَيۡرٖ فَلِأَنفُسِكُمۡۚ وَمَا تُنفِقُونَ إِلَّا ٱبۡتِغَآءَ وَجۡهِ ٱللَّهِۚ وَمَا تُنفِقُواْ مِنۡ خَيۡرٖ يُوَفَّ إِلَيۡكُمۡ وَأَنتُمۡ لَا تُظۡلَمُونَ

Siudindo wako kuwaongola, koma Allah amamuongola amene wamfuna, (udindo wako nkulalikira kokha). Ndipo chuma chilichonse chimene mungachipereke, (phindu lake) lili pa inu eni, ndipo musapereke pokhapokha pofunafuna chikondi cha Allah. Ndipo chuma chilichonse chimene mungachipereke adzakubwezerani mokwanira (mphoto yake), ndipo simudzaponderezedwa.[55] info

[55] Apa akumuuza Mtumiki (s.a.w) pamodzi ndi aliyense wolamula kuchita zabwino ndikuletsa kuchita zoipa kuti udindo wawo nkufikitsa uthengawo. Pa iwo palibe vuto ngati anthuwo savomereza, iwo adzapezabe mphoto yolamulira zabwino ndikuletsa zoipa ngakhale kuti sanawatsatire.

التفاسير:

external-link copy
273 : 2

لِلۡفُقَرَآءِ ٱلَّذِينَ أُحۡصِرُواْ فِي سَبِيلِ ٱللَّهِ لَا يَسۡتَطِيعُونَ ضَرۡبٗا فِي ٱلۡأَرۡضِ يَحۡسَبُهُمُ ٱلۡجَاهِلُ أَغۡنِيَآءَ مِنَ ٱلتَّعَفُّفِ تَعۡرِفُهُم بِسِيمَٰهُمۡ لَا يَسۡـَٔلُونَ ٱلنَّاسَ إِلۡحَافٗاۗ وَمَا تُنفِقُواْ مِنۡ خَيۡرٖ فَإِنَّ ٱللَّهَ بِهِۦ عَلِيمٌ

(Sadakazo ziperekedwe) kwa amphawi amene atsekerezedwa pa njira ya Allah, amene sangathe kuyenda pa dziko (kukachita ntchito yopezera zofunika pamoyo wawo). Amene sadziwa za chikhalidwe chawo, amawaganizira kuti ngolemera chifukwa chakudziletsa kwawo (kupemphapempha). Ungawazindikire (kuti ngosowedwa) ndi zizindikiro zawo. Sapempha anthu mwaliuma. Ndipo chabwino chilichonse chimene mukupereka, ndithudi, Allah ali Wodziwa za icho. info
التفاسير:

external-link copy
274 : 2

ٱلَّذِينَ يُنفِقُونَ أَمۡوَٰلَهُم بِٱلَّيۡلِ وَٱلنَّهَارِ سِرّٗا وَعَلَانِيَةٗ فَلَهُمۡ أَجۡرُهُمۡ عِندَ رَبِّهِمۡ وَلَا خَوۡفٌ عَلَيۡهِمۡ وَلَا هُمۡ يَحۡزَنُونَ

Amene akupereka chuma chawo usiku ndi usana, mobisa ndi moonekera, ali ndi malipiro awo kwa Mbuye wawo; ndipo pa iwo sipadzakhala mantha, ndiponso sadzadandaula. info
التفاسير: