Traduction des sens du Noble Coran - La traduction tchétchène - Khâlid Ibrâhîm Bîtâlâ

Numéro de la page:close

external-link copy
127 : 2

وَإِذۡ يَرۡفَعُ إِبۡرَٰهِـۧمُ ٱلۡقَوَاعِدَ مِنَ ٱلۡبَيۡتِ وَإِسۡمَٰعِيلُ رَبَّنَا تَقَبَّلۡ مِنَّآۖ إِنَّكَ أَنتَ ٱلسَّمِيعُ ٱلۡعَلِيمُ

Ndipo (kumbukiraninso) pamene Ibrahim ndi Ismail ankakhazikitsa maziko a nyumba (uku akupempha kwa Allah): “E Mbuye wathu! Tilandireni (ntchito yathuyi), ndithudi, Inu ndinu Akumva; Odziwa.” info
التفاسير:

external-link copy
128 : 2

رَبَّنَا وَٱجۡعَلۡنَا مُسۡلِمَيۡنِ لَكَ وَمِن ذُرِّيَّتِنَآ أُمَّةٗ مُّسۡلِمَةٗ لَّكَ وَأَرِنَا مَنَاسِكَنَا وَتُبۡ عَلَيۡنَآۖ إِنَّكَ أَنتَ ٱلتَّوَّابُ ٱلرَّحِيمُ

“E Mbuye wathu! Tichiteni Kukhalala Asilamu (ogonjera Inu), pamodzinso ndi ana athu muwachite kukhala fuko la Chisilamu (logonjera Inu). Ndipo tidziwitseni (njira) za mapemphero athu; ndipo landirani kulapa kwathu, ndithudi, Inu Ndinu Wolandira kulapa mochuluka; Wachisoni chosatha.” info
التفاسير:

external-link copy
129 : 2

رَبَّنَا وَٱبۡعَثۡ فِيهِمۡ رَسُولٗا مِّنۡهُمۡ يَتۡلُواْ عَلَيۡهِمۡ ءَايَٰتِكَ وَيُعَلِّمُهُمُ ٱلۡكِتَٰبَ وَٱلۡحِكۡمَةَ وَيُزَكِّيهِمۡۖ إِنَّكَ أَنتَ ٱلۡعَزِيزُ ٱلۡحَكِيمُ

“E Mbuye wathu! Atumizireni mtumiki wochokera mwa iwo, kuti awawerengere Ayah (ndime) zanu ndikuwaphunzitsa buku (Lanu) ndi nzeru ndikuti awayeretse. Ndithudi Inu Ndinu Amphamvu zoposa, Anzeru zakuya.” info
التفاسير:

external-link copy
130 : 2

وَمَن يَرۡغَبُ عَن مِّلَّةِ إِبۡرَٰهِـۧمَ إِلَّا مَن سَفِهَ نَفۡسَهُۥۚ وَلَقَدِ ٱصۡطَفَيۡنَٰهُ فِي ٱلدُّنۡيَاۖ وَإِنَّهُۥ فِي ٱلۡأٓخِرَةِ لَمِنَ ٱلصَّٰلِحِينَ

Kodi ndani anganyozere chipembedzo cha Ibrahim posakhala yemwe mtima wake uli wopusa? Ndithudi, tidamsankha (Ibrahim) pa dziko lapansi; ndipo iye tsiku lachimaliziro adzakhala m’modzi wa anthu abwino.” info
التفاسير:

external-link copy
131 : 2

إِذۡ قَالَ لَهُۥ رَبُّهُۥٓ أَسۡلِمۡۖ قَالَ أَسۡلَمۡتُ لِرَبِّ ٱلۡعَٰلَمِينَ

(Kumbukiraninso) pamene Mbuye wake adamuuza kuti: “Khala Msilamu (gonjera).” (Iye) adati: “Ndili Msilamu (ndagonjera) kwa Mbuye wa zolengedwa zonse.” info
التفاسير:

external-link copy
132 : 2

وَوَصَّىٰ بِهَآ إِبۡرَٰهِـۧمُ بَنِيهِ وَيَعۡقُوبُ يَٰبَنِيَّ إِنَّ ٱللَّهَ ٱصۡطَفَىٰ لَكُمُ ٱلدِّينَ فَلَا تَمُوتُنَّ إِلَّا وَأَنتُم مُّسۡلِمُونَ

Ndipo Ibrahim adalangizanso ana ake za zimenezi, chonchonso Ya’qub (adalangizanso ana ake kuti): “E inu ana anga! Ndithudi, Allah wakusankhirani chipembedzo; choncho musafe pokhapokha muli Asilamu (ogonjera Mulungu).” info
التفاسير:

external-link copy
133 : 2

أَمۡ كُنتُمۡ شُهَدَآءَ إِذۡ حَضَرَ يَعۡقُوبَ ٱلۡمَوۡتُ إِذۡ قَالَ لِبَنِيهِ مَا تَعۡبُدُونَ مِنۢ بَعۡدِيۖ قَالُواْ نَعۡبُدُ إِلَٰهَكَ وَإِلَٰهَ ءَابَآئِكَ إِبۡرَٰهِـۧمَ وَإِسۡمَٰعِيلَ وَإِسۡحَٰقَ إِلَٰهٗا وَٰحِدٗا وَنَحۡنُ لَهُۥ مُسۡلِمُونَ

Kapena inu (Ayuda ndi Akhrisitu) mudalipo pamene Ya’qub idamdzera imfa, pamene adati kwa ana ake: “Kodi pambuyo panga mudzapembedza yani?” Iwo adayankha nati: “Tidzapembedza Mulungu wako, Mulungu wa makolo ako; Ibrahim, Ismail ndi Ishâq; Mulungu mmodzi basi. Ndipo ife kwa Iye tili Asilamu (ogonjera).” info
التفاسير:

external-link copy
134 : 2

تِلۡكَ أُمَّةٞ قَدۡ خَلَتۡۖ لَهَا مَا كَسَبَتۡ وَلَكُم مَّا كَسَبۡتُمۡۖ وَلَا تُسۡـَٔلُونَ عَمَّا كَانُواْ يَعۡمَلُونَ

Umenewo ndi mbadwo wa anthu umene udamka kale. Udzapeza zimene udachita, ndipo inunso mudzapeza zimene mudachita. Ndipo inu simudzafunsidwa zimene iwo ankachita. info
التفاسير: