Salin ng mga Kahulugan ng Marangal na Qur'an - Salin sa Wikang Chichewa ni Khalid Ibrahim Bityala

Numero ng Pahina:close

external-link copy
9 : 6

وَلَوۡ جَعَلۡنَٰهُ مَلَكٗا لَّجَعَلۡنَٰهُ رَجُلٗا وَلَلَبَسۡنَا عَلَيۡهِم مَّا يَلۡبِسُونَ

Ndipo tikadampanga iyeyo kukhala mngelo, tikadamsandutsa kukhala munthu (chifukwa iwo sangathe kumuona mngelo), ndipo tikadati asakanikirane nawo monga momwe eni amasakanikirana (kotero kuti sakadamdziwa kuti mngelo ndi uyu). info
التفاسير:

external-link copy
10 : 6

وَلَقَدِ ٱسۡتُهۡزِئَ بِرُسُلٖ مِّن قَبۡلِكَ فَحَاقَ بِٱلَّذِينَ سَخِرُواْ مِنۡهُم مَّا كَانُواْ بِهِۦ يَسۡتَهۡزِءُونَ

Ndithudi, adachitidwa chipongwe atumiki patsogolo pako; koma (mapeto ake) aja mwa iwo omwe adachita chipongwe zidawazinga zomwe adali kuzichitira chipongwe. info
التفاسير:

external-link copy
11 : 6

قُلۡ سِيرُواْ فِي ٱلۡأَرۡضِ ثُمَّ ٱنظُرُواْ كَيۡفَ كَانَ عَٰقِبَةُ ٱلۡمُكَذِّبِينَ

Nena: “Yendani pa dziko, kenako tayang’anani momwe adalili mapeto a otsutsa.” [170] info

[170] Apa tanthauzo nkuti tayendani padziko mukayang’ane ndi kulingalira zilango zopweteka zimene zidawatsikira anthu akale. Kuyang’ana ndi kulingalira zoterezo kuti zikhale phunziro kwa inu kuti musachitenso zimene zidawagwetsa kuchionongeko.

التفاسير:

external-link copy
12 : 6

قُل لِّمَن مَّا فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِۖ قُل لِّلَّهِۚ كَتَبَ عَلَىٰ نَفۡسِهِ ٱلرَّحۡمَةَۚ لَيَجۡمَعَنَّكُمۡ إِلَىٰ يَوۡمِ ٱلۡقِيَٰمَةِ لَا رَيۡبَ فِيهِۚ ٱلَّذِينَ خَسِرُوٓاْ أَنفُسَهُمۡ فَهُمۡ لَا يُؤۡمِنُونَ

Nena (mowafunsa): “Nzayani zomwe zili kumwamba ndi pansi?” Nena kwa iwo (ngati sakuyankha): “Nza Allah.” Iye wadzikakamiza kuwachitira chifundo (anthu Ake). (Pachifukwa chimenechi amawapatsa nthawi osawalanga mwachangu). Ndithudi adzakusonkhanitsani tsiku la Qiyâma lopanda chikaiko. Amene adzitaya okha, sakhulupirira (za tsikulo). info
التفاسير:

external-link copy
13 : 6

۞ وَلَهُۥ مَا سَكَنَ فِي ٱلَّيۡلِ وَٱلنَّهَارِۚ وَهُوَ ٱلسَّمِيعُ ٱلۡعَلِيمُ

Nza Iye (Allah) zonse zili mu nthawi ya usiku ndi usana. Iye Ngwakumva, Ngodziwa. info
التفاسير:

external-link copy
14 : 6

قُلۡ أَغَيۡرَ ٱللَّهِ أَتَّخِذُ وَلِيّٗا فَاطِرِ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ وَهُوَ يُطۡعِمُ وَلَا يُطۡعَمُۗ قُلۡ إِنِّيٓ أُمِرۡتُ أَنۡ أَكُونَ أَوَّلَ مَنۡ أَسۡلَمَۖ وَلَا تَكُونَنَّ مِنَ ٱلۡمُشۡرِكِينَ

Nena: “Ndidzipangire mtetezi wanga kusiya Allah, Mlengi wa thambo ndi nthaka? Iye Njemwe amadyetsa ndipo sadyetsedwa.” Nena: “Ndalamulidwa kukhala woyamba mwa olowa m’Chisilamu.” Ndipo (ndauzidwa kuti): “Usakhale mwa ophatikiza (Allah ndi mafano)” info
التفاسير:

external-link copy
15 : 6

قُلۡ إِنِّيٓ أَخَافُ إِنۡ عَصَيۡتُ رَبِّي عَذَابَ يَوۡمٍ عَظِيمٖ

Nena (kwa iwo): “Ine ndikuopa chilango cha tsiku lalikulu ngati ndinyoza Mbuye wanga.” info
التفاسير:

external-link copy
16 : 6

مَّن يُصۡرَفۡ عَنۡهُ يَوۡمَئِذٖ فَقَدۡ رَحِمَهُۥۚ وَذَٰلِكَ ٱلۡفَوۡزُ ٱلۡمُبِينُ

Yemwe adzapewetsedwe ku chilangocho tsiku limenelo, ndiye kuti wamchitira chifundo; kumeneko nkupambana kowonekera. info
التفاسير:

external-link copy
17 : 6

وَإِن يَمۡسَسۡكَ ٱللَّهُ بِضُرّٖ فَلَا كَاشِفَ لَهُۥٓ إِلَّا هُوَۖ وَإِن يَمۡسَسۡكَ بِخَيۡرٖ فَهُوَ عَلَىٰ كُلِّ شَيۡءٖ قَدِيرٞ

Ngati Allah atakukhudza ndi mazunzo, palibe aliyense angathe kukuchotsera, koma Iye basi; ndipo ngati atakukhudza ndi zabwino (palibe amene angakutsekereze ku zabwinozo). Iye ali ndi mphamvu pa chilichonse.[171] info

[171] Mu Ayah iyi Allah akuuza Mtumiki Wake ndi omtsatira ake kuti ngati masautso, umphawi ndi matenda zitampeza, palibe amene angamchotsere zimenezi koma Allah basi. Ndiponso ngati zitamkhudza zabwino, monga kukhala ndi moyo wangwiro ndi chuma chambiri, palibe amene angazichotse zimenezi kwa iye ngati Allah safuna. Choncho tiyeni tiike chikhulupiliro chathu chonse mwa Allah.

التفاسير:

external-link copy
18 : 6

وَهُوَ ٱلۡقَاهِرُ فَوۡقَ عِبَادِهِۦۚ وَهُوَ ٱلۡحَكِيمُ ٱلۡخَبِيرُ

Iye ndi Mgonjetsi pa anthu ake (onse); Iye Ngwanzeru zakuya, Wodziwa nkhani zonse. info
التفاسير: