[170] Apa tanthauzo nkuti tayendani padziko mukayang’ane ndi kulingalira zilango zopweteka zimene zidawatsikira anthu akale. Kuyang’ana ndi kulingalira zoterezo kuti zikhale phunziro kwa inu kuti musachitenso zimene zidawagwetsa kuchionongeko.
[171] Mu Ayah iyi Allah akuuza Mtumiki Wake ndi omtsatira ake kuti ngati masautso, umphawi ndi matenda zitampeza, palibe amene angamchotsere zimenezi koma Allah basi. Ndiponso ngati zitamkhudza zabwino, monga kukhala ndi moyo wangwiro ndi chuma chambiri, palibe amene angazichotse zimenezi kwa iye ngati Allah safuna. Choncho tiyeni tiike chikhulupiliro chathu chonse mwa Allah.