Translation of the Meanings of the Noble Qur'an - Chewa translation - Khaled Ibrahim Batyala

Page Number:close

external-link copy
53 : 6

وَكَذَٰلِكَ فَتَنَّا بَعۡضَهُم بِبَعۡضٖ لِّيَقُولُوٓاْ أَهَٰٓؤُلَآءِ مَنَّ ٱللَّهُ عَلَيۡهِم مِّنۢ بَيۡنِنَآۗ أَلَيۡسَ ٱللَّهُ بِأَعۡلَمَ بِٱلشَّٰكِرِينَ

Ndipo momwemo tawasankha ena (osauka) kukhala mayeso a ena (olemera) kuti (osauka) anene: “Kodi awa ndi omwe Allah wawasankhira ubwino mwa ife (ndikutisiya ife?)” Kodi Allah sali Wodziwa zedi amene akumthokoza? info
التفاسير:

external-link copy
54 : 6

وَإِذَا جَآءَكَ ٱلَّذِينَ يُؤۡمِنُونَ بِـَٔايَٰتِنَا فَقُلۡ سَلَٰمٌ عَلَيۡكُمۡۖ كَتَبَ رَبُّكُمۡ عَلَىٰ نَفۡسِهِ ٱلرَّحۡمَةَ أَنَّهُۥ مَنۡ عَمِلَ مِنكُمۡ سُوٓءَۢا بِجَهَٰلَةٖ ثُمَّ تَابَ مِنۢ بَعۡدِهِۦ وَأَصۡلَحَ فَأَنَّهُۥ غَفُورٞ رَّحِيمٞ

Ndipo (iwe Mneneri) akakudzera (awo osauka) amene akhulupirira zizindikiro zathu (atalakwa pang’ono), auze: “Mtendere ukhale pa inu. Mbuye wanu wadzikakamiza kukhala Wachifundo, kuti mwa inu amene achite choipa mwaumbuli, koma pambuyo pake nkulapa, nachita zabwino, Allah amkhululukira; Iye Ngokhululuka kwambiri, Ngwachisoni chosatha.” info
التفاسير:

external-link copy
55 : 6

وَكَذَٰلِكَ نُفَصِّلُ ٱلۡأٓيَٰتِ وَلِتَسۡتَبِينَ سَبِيلُ ٱلۡمُجۡرِمِينَ

Mmenemo ndi momwe tikufotokozera zizindikiro mwatsatanetsatane (kuti choonadi chioneke) ndi kuti njira ya oipa idziwike bwinobwino. info
التفاسير:

external-link copy
56 : 6

قُلۡ إِنِّي نُهِيتُ أَنۡ أَعۡبُدَ ٱلَّذِينَ تَدۡعُونَ مِن دُونِ ٱللَّهِۚ قُل لَّآ أَتَّبِعُ أَهۡوَآءَكُمۡ قَدۡ ضَلَلۡتُ إِذٗا وَمَآ أَنَا۠ مِنَ ٱلۡمُهۡتَدِينَ

Nena: “Ndithu ine ndaletsedwa kupembedza amene mukuwapembedza kusiya Allah.” Nena: “Sinditsata zilakolako zanu; ndikadatero ndikadasokera ndipo sindikadakhala mwa owongoka.” info
التفاسير:

external-link copy
57 : 6

قُلۡ إِنِّي عَلَىٰ بَيِّنَةٖ مِّن رَّبِّي وَكَذَّبۡتُم بِهِۦۚ مَا عِندِي مَا تَسۡتَعۡجِلُونَ بِهِۦٓۚ إِنِ ٱلۡحُكۡمُ إِلَّا لِلَّهِۖ يَقُصُّ ٱلۡحَقَّۖ وَهُوَ خَيۡرُ ٱلۡفَٰصِلِينَ

Nena: “Ndithu ine ndili ndi umboni wowoneka wochokera kwa Mbuye wanga (wotsimikizira zomwe ndikunenazi), koma inu mwautsutsa. Ndilibe (chilango) chimene mukuchifulumizitsacho. Palibe kulamula koma nkwa Allah. Amakamba zoona zokhazokha; Iye Ngwabwino mwa oweruza (onse).” info
التفاسير:

external-link copy
58 : 6

قُل لَّوۡ أَنَّ عِندِي مَا تَسۡتَعۡجِلُونَ بِهِۦ لَقُضِيَ ٱلۡأَمۡرُ بَيۡنِي وَبَيۡنَكُمۡۗ وَٱللَّهُ أَعۡلَمُ بِٱلظَّٰلِمِينَ

Nena: “Ndikadakhala nacho chimene mukuchifulumizitsacho, ndiye kuti chinthucho chikadachitika pakati pa ine ndi inu (ndikadakuonongani koma ndilibe nyonga). Ndipo Allah akuwadziwa bwino anthu ochita zoipa.” info
التفاسير:

external-link copy
59 : 6

۞ وَعِندَهُۥ مَفَاتِحُ ٱلۡغَيۡبِ لَا يَعۡلَمُهَآ إِلَّا هُوَۚ وَيَعۡلَمُ مَا فِي ٱلۡبَرِّ وَٱلۡبَحۡرِۚ وَمَا تَسۡقُطُ مِن وَرَقَةٍ إِلَّا يَعۡلَمُهَا وَلَا حَبَّةٖ فِي ظُلُمَٰتِ ٱلۡأَرۡضِ وَلَا رَطۡبٖ وَلَا يَابِسٍ إِلَّا فِي كِتَٰبٖ مُّبِينٖ

Ndipo Iye (Allah) ali nawo Makiyi a zobisika palibe akuwadziwa koma Iye basi. Ndipo akudziwa za pamtunda ndi za panyanja. Ndipo palibe tsamba limene limagwa koma amalidziwa. Ndipo (siigwa) njere mu mdima wa m’nthaka (koma iye akudziwa). Ndipo (sichigwa) chachiwisi ngakhale chouma, koma chili m’buku loonetsa chilichonse. info
التفاسير: