Translation of the Meanings of the Noble Qur'an - Chewa translation - Khaled Ibrahim Batyala

Page Number:close

external-link copy
152 : 6

وَلَا تَقۡرَبُواْ مَالَ ٱلۡيَتِيمِ إِلَّا بِٱلَّتِي هِيَ أَحۡسَنُ حَتَّىٰ يَبۡلُغَ أَشُدَّهُۥۚ وَأَوۡفُواْ ٱلۡكَيۡلَ وَٱلۡمِيزَانَ بِٱلۡقِسۡطِۖ لَا نُكَلِّفُ نَفۡسًا إِلَّا وُسۡعَهَاۖ وَإِذَا قُلۡتُمۡ فَٱعۡدِلُواْ وَلَوۡ كَانَ ذَا قُرۡبَىٰۖ وَبِعَهۡدِ ٱللَّهِ أَوۡفُواْۚ ذَٰلِكُمۡ وَصَّىٰكُم بِهِۦ لَعَلَّكُمۡ تَذَكَّرُونَ

“Ndipo musachiyandikire chuma cha mwana wamasiye, koma m’njira yabwino (monga kuchichulukitsa ndi malonda) mpaka afike pansinkhu wokwanira. Ndipo kwaniritsani mwachilungamo miyeso ya mbale ndi masikelo; sitikakamiza munthu koma chimene angathe; ndipo pamene mukunena, (popereka umboni), nenani mwachilungamo ngakhale (umboniwo) uli wokhudza achibale. Ndipo kwaniritsani lonjezo la Allah. Izi ndi zomwe akukulangizani kuti mukumbukire.” info
التفاسير:

external-link copy
153 : 6

وَأَنَّ هَٰذَا صِرَٰطِي مُسۡتَقِيمٗا فَٱتَّبِعُوهُۖ وَلَا تَتَّبِعُواْ ٱلسُّبُلَ فَتَفَرَّقَ بِكُمۡ عَن سَبِيلِهِۦۚ ذَٰلِكُمۡ وَصَّىٰكُم بِهِۦ لَعَلَّكُمۡ تَتَّقُونَ

(Auze kuti): “Ndithu iyi ndi njira yanga yoongoka. Choncho itsateni. Ndipo musatsate njira zina zambiri kuopera kuti zingakulekanitseni ndi njira Yake, (Allah) wakulangizani izi kuti mudziteteze kuzoipa.” info
التفاسير:

external-link copy
154 : 6

ثُمَّ ءَاتَيۡنَا مُوسَى ٱلۡكِتَٰبَ تَمَامًا عَلَى ٱلَّذِيٓ أَحۡسَنَ وَتَفۡصِيلٗا لِّكُلِّ شَيۡءٖ وَهُدٗى وَرَحۡمَةٗ لَّعَلَّهُم بِلِقَآءِ رَبِّهِمۡ يُؤۡمِنُونَ

Ndipo Mûsa tidampatsa buku (kukhala) lokwaniritsa (chisomo) kwa yemwe wachita zabwino, lofotokoza chinthu chilichonse, chiongoko ndi chifundo, kuti iwo akhulupirire za kukumana ndi Mbuye wawo. info
التفاسير:

external-link copy
155 : 6

وَهَٰذَا كِتَٰبٌ أَنزَلۡنَٰهُ مُبَارَكٞ فَٱتَّبِعُوهُ وَٱتَّقُواْ لَعَلَّكُمۡ تُرۡحَمُونَ

Ndipo iyi (Qur’an) ndi buku lodalitsika lomwe talivumbulutsa (kwa inu), choncho, litsateni ndi kuopa (Allah) kuti muchitiridwe chifundo; info
التفاسير:

external-link copy
156 : 6

أَن تَقُولُوٓاْ إِنَّمَآ أُنزِلَ ٱلۡكِتَٰبُ عَلَىٰ طَآئِفَتَيۡنِ مِن قَبۡلِنَا وَإِن كُنَّا عَن دِرَاسَتِهِمۡ لَغَٰفِلِينَ

Kuti musadzanene (tsiku la Qiyâma) kuti: “Mabuku adavumbulutsidwa pa magulu awiri omwe adalipo patsogolo pathu, (Ayuda ndi Akhrisitu); ndipo ife sitidadziwe chilichonse pa zomwe adali kuwerenga ndi kuphunzira.” info
التفاسير:

external-link copy
157 : 6

أَوۡ تَقُولُواْ لَوۡ أَنَّآ أُنزِلَ عَلَيۡنَا ٱلۡكِتَٰبُ لَكُنَّآ أَهۡدَىٰ مِنۡهُمۡۚ فَقَدۡ جَآءَكُم بَيِّنَةٞ مِّن رَّبِّكُمۡ وَهُدٗى وَرَحۡمَةٞۚ فَمَنۡ أَظۡلَمُ مِمَّن كَذَّبَ بِـَٔايَٰتِ ٱللَّهِ وَصَدَفَ عَنۡهَاۗ سَنَجۡزِي ٱلَّذِينَ يَصۡدِفُونَ عَنۡ ءَايَٰتِنَا سُوٓءَ ٱلۡعَذَابِ بِمَا كَانُواْ يَصۡدِفُونَ

Kapena kuti musadzati: “Likadavumbulutsidwa buku kwa ife, ndithudi, tikadakhala oongoka kuposa iwo.” Choncho, chakudzerani chizindikiro kuchokera kwa Mbuye wanu, ndi chiongoko ndi mtendere. Kodi ndani woipitsitsa kwambiri kuposa amene watsutsa zizindikiro za Allah ndi kutembenukira kutali Nazo? Tidzawalipira amene akutembenukira kutali ndi zizindikiro zathu, chilango choipa, chifukwa cha kudziika kwawo kutali. info
التفاسير: