Salin ng mga Kahulugan ng Marangal na Qur'an - Salin sa Wikang Chichewa ni Khalid Ibrahim Bityala

Numero ng Pahina:close

external-link copy
82 : 6

ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَلَمۡ يَلۡبِسُوٓاْ إِيمَٰنَهُم بِظُلۡمٍ أُوْلَٰٓئِكَ لَهُمُ ٱلۡأَمۡنُ وَهُم مُّهۡتَدُونَ

(Palibe chikaiko kwa) amene adakhulupirira ndipo sadasakanize chikhulupiliro chawo ndi kupondereza (shirk), iwowo ali nacho chitetezo. Ndiponso iwo ndi omwe ali oongoka. info
التفاسير:

external-link copy
83 : 6

وَتِلۡكَ حُجَّتُنَآ ءَاتَيۡنَٰهَآ إِبۡرَٰهِيمَ عَلَىٰ قَوۡمِهِۦۚ نَرۡفَعُ دَرَجَٰتٖ مَّن نَّشَآءُۗ إِنَّ رَبَّكَ حَكِيمٌ عَلِيمٞ

Ndipo izi ndi zizindikiro Zathu (mitsutso Yathu), zomwe tidampatsa Ibrahim pa anthu ake. Timamtukulira ulemelero amene tamfuna. Ndithu Mbuye wako Ngwanzeru zakuya, Ngodziwa kwambiri. info
التفاسير:

external-link copy
84 : 6

وَوَهَبۡنَا لَهُۥٓ إِسۡحَٰقَ وَيَعۡقُوبَۚ كُلًّا هَدَيۡنَاۚ وَنُوحًا هَدَيۡنَا مِن قَبۡلُۖ وَمِن ذُرِّيَّتِهِۦ دَاوُۥدَ وَسُلَيۡمَٰنَ وَأَيُّوبَ وَيُوسُفَ وَمُوسَىٰ وَهَٰرُونَۚ وَكَذَٰلِكَ نَجۡزِي ٱلۡمُحۡسِنِينَ

Ndipo tidampatsa (Ibrahim mwana wotchedwa) Ishaq ndi (mdzukulu wotchedwa) Ya’qub. Onse tidawaongola. Nayenso Nuh tidamuongola kale (asadadze Mneneri Ibrahim). Ndipo kuchokera m’mbumba yake (Nuh, tidamuongola) Daud, Sulaiman, Ayubu, Yûsuf, Mûsa, ndi Harun. Ndipo umo ndi momwe timawalipirira ochita zabwino. info
التفاسير:

external-link copy
85 : 6

وَزَكَرِيَّا وَيَحۡيَىٰ وَعِيسَىٰ وَإِلۡيَاسَۖ كُلّٞ مِّنَ ٱلصَّٰلِحِينَ

Tidamutsogoleranso Zakariya, Yahya, Isa (Yesu) ndi Iliyasa. Onse adali mwa anthu abwino. info
التفاسير:

external-link copy
86 : 6

وَإِسۡمَٰعِيلَ وَٱلۡيَسَعَ وَيُونُسَ وَلُوطٗاۚ وَكُلّٗا فَضَّلۡنَا عَلَى ٱلۡعَٰلَمِينَ

Ndi Ismail, Eliya, Yunus (Yona) ndi Luti (Loti). Onsewa tidawapatsa ubwino pa zolengedwa zonse. info
التفاسير:

external-link copy
87 : 6

وَمِنۡ ءَابَآئِهِمۡ وَذُرِّيَّٰتِهِمۡ وَإِخۡوَٰنِهِمۡۖ وَٱجۡتَبَيۡنَٰهُمۡ وَهَدَيۡنَٰهُمۡ إِلَىٰ صِرَٰطٖ مُّسۡتَقِيمٖ

(Ndiponso tidawatsogolera) ena mwa atate awo, ana awo ndi abale awo. Ndipo tidawasankha ndi kuwaongolera ku njira yolunjika. info
التفاسير:

external-link copy
88 : 6

ذَٰلِكَ هُدَى ٱللَّهِ يَهۡدِي بِهِۦ مَن يَشَآءُ مِنۡ عِبَادِهِۦۚ وَلَوۡ أَشۡرَكُواْ لَحَبِطَ عَنۡهُم مَّا كَانُواْ يَعۡمَلُونَ

Ichi ndi chiongoko cha Allah. Ndi icho akuongolera yemwe wamfuna mwa akapolo Ake. Akadakhala kuti (aneneriwo) adamphatikiza (Allah ndi zina) zikadawaonongekera zimene ankachita. info
التفاسير:

external-link copy
89 : 6

أُوْلَٰٓئِكَ ٱلَّذِينَ ءَاتَيۡنَٰهُمُ ٱلۡكِتَٰبَ وَٱلۡحُكۡمَ وَٱلنُّبُوَّةَۚ فَإِن يَكۡفُرۡ بِهَا هَٰٓؤُلَآءِ فَقَدۡ وَكَّلۡنَا بِهَا قَوۡمٗا لَّيۡسُواْ بِهَا بِكَٰفِرِينَ

Iwo ndi omwe tidawapatsa mabuku, chiweruzo, ndi uneneri. Choncho ngati awa (osakhulupirira) azikane izi, basi, tazipereka kale kwa anthu omwe sangazikane. info
التفاسير:

external-link copy
90 : 6

أُوْلَٰٓئِكَ ٱلَّذِينَ هَدَى ٱللَّهُۖ فَبِهُدَىٰهُمُ ٱقۡتَدِهۡۗ قُل لَّآ أَسۡـَٔلُكُمۡ عَلَيۡهِ أَجۡرًاۖ إِنۡ هُوَ إِلَّا ذِكۡرَىٰ لِلۡعَٰلَمِينَ

Iwo ndi omwe Allah adawaongola choncho, tsatira chiongoko chawo. Nena: “Sindikukupemphani malipiro pa izi (zomwe ndikukuphunzitsanizi, koma ndikungotumikira Allah). Ichi sichina koma ndi ulaliki kwa zolengedwa (majini ndi anthu).” info
التفاسير: