Salin ng mga Kahulugan ng Marangal na Qur'an - Salin sa Wikang Chichewa ni Khalid Ibrahim Bityala

Numero ng Pahina:close

external-link copy
69 : 6

وَمَا عَلَى ٱلَّذِينَ يَتَّقُونَ مِنۡ حِسَابِهِم مِّن شَيۡءٖ وَلَٰكِن ذِكۡرَىٰ لَعَلَّهُمۡ يَتَّقُونَ

Palibe chilichonse chimene chingawapeze oopa Allah chochokera m’chiwerengero cha oipawo, koma chofunika kwa iwo (oopa Allah) ndikuwakumbutsa (oipawo) kuti aope (aleke zomwe akunenazo). info
التفاسير:

external-link copy
70 : 6

وَذَرِ ٱلَّذِينَ ٱتَّخَذُواْ دِينَهُمۡ لَعِبٗا وَلَهۡوٗا وَغَرَّتۡهُمُ ٱلۡحَيَوٰةُ ٱلدُّنۡيَاۚ وَذَكِّرۡ بِهِۦٓ أَن تُبۡسَلَ نَفۡسُۢ بِمَا كَسَبَتۡ لَيۡسَ لَهَا مِن دُونِ ٱللَّهِ وَلِيّٞ وَلَا شَفِيعٞ وَإِن تَعۡدِلۡ كُلَّ عَدۡلٖ لَّا يُؤۡخَذۡ مِنۡهَآۗ أُوْلَٰٓئِكَ ٱلَّذِينَ أُبۡسِلُواْ بِمَا كَسَبُواْۖ لَهُمۡ شَرَابٞ مِّنۡ حَمِيمٖ وَعَذَابٌ أَلِيمُۢ بِمَا كَانُواْ يَكۡفُرُونَ

Asiye amene achita chipembedzo chawo kukhala masewera ndi chibwana. Ndipo wawanyenga moyo wadziko lapansi. Choncho, akumbutse ndi Qur’aniyo (kuti achenjere), kuti ungaonongedwe mtima uliwonse (ndi kuikidwa m’ndende) kupyolera mu zomwe udapata. Ndipo sukhala ndi mtetezi ngakhale muomboli posakhala Allah, ngakhale utayesera kupereka dipo lamtundu uliwonse silingavomerezedwe (kwa mzimuwo). Awo ndi omwe aonongeka ndi kunjatidwa chifukwa cha zomwe adapeza. Iwo adzakhala ndi chakumwa cha madzi a moto owira kwambiri, ndi chilango chopweteka chifukwa cha kusakhulupirira kwawo (Allah). info
التفاسير:

external-link copy
71 : 6

قُلۡ أَنَدۡعُواْ مِن دُونِ ٱللَّهِ مَا لَا يَنفَعُنَا وَلَا يَضُرُّنَا وَنُرَدُّ عَلَىٰٓ أَعۡقَابِنَا بَعۡدَ إِذۡ هَدَىٰنَا ٱللَّهُ كَٱلَّذِي ٱسۡتَهۡوَتۡهُ ٱلشَّيَٰطِينُ فِي ٱلۡأَرۡضِ حَيۡرَانَ لَهُۥٓ أَصۡحَٰبٞ يَدۡعُونَهُۥٓ إِلَى ٱلۡهُدَى ٱئۡتِنَاۗ قُلۡ إِنَّ هُدَى ٱللَّهِ هُوَ ٱلۡهُدَىٰۖ وَأُمِرۡنَا لِنُسۡلِمَ لِرَبِّ ٱلۡعَٰلَمِينَ

Nena: “Kodi tipembedze omwe sali Allah, omwe sangatipatse phindu (ngati titawapembedza), ndiponso sangathe kutivutitsa (tikasiya kuwapembedza), ndetibwezedwe m’mbuyo pambuyo potitsogolera Allah? Tikhale chimodzimodzi aja omwe satana adawasokeretsa, nkukhala achewuchewu pa dziko? Ali nawo anzawo omwe akuwaitanira ku chiongoko (kuti) ‘Bwerani kwathu, (koma samva. Sitingakhale monga anthu otere).” Nena: “Utsogozi weniweni ngwa Allah, ndipo talamulidwa kuti tigonjere Mbuye wa zolengedwa zonse.” info
التفاسير:

external-link copy
72 : 6

وَأَنۡ أَقِيمُواْ ٱلصَّلَوٰةَ وَٱتَّقُوهُۚ وَهُوَ ٱلَّذِيٓ إِلَيۡهِ تُحۡشَرُونَ

Ndikuti: “Pempherani Swala, ndipo muopeni Iye, Yemwe kwa Iye mudzasonkhanitsidwa.” info
التفاسير:

external-link copy
73 : 6

وَهُوَ ٱلَّذِي خَلَقَ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضَ بِٱلۡحَقِّۖ وَيَوۡمَ يَقُولُ كُن فَيَكُونُۚ قَوۡلُهُ ٱلۡحَقُّۚ وَلَهُ ٱلۡمُلۡكُ يَوۡمَ يُنفَخُ فِي ٱلصُّورِۚ عَٰلِمُ ٱلۡغَيۡبِ وَٱلشَّهَٰدَةِۚ وَهُوَ ٱلۡحَكِيمُ ٱلۡخَبِيرُ

Iye ndiye adalenga thambo ndi nthaka mwa choonadi. Ndipo panthawi imene akunena (kuchiuza chinthu): “Chitika,” ndipo chimachitikadi. Mawu ake ndioona. Ndipo ufumu udzakhala Wakewake tsiku limene Lipenga lidzaimbidwa. Ngodziwa zamseri ndi zooneka. Iye Ngwanzeru zakuya, Wodziwa nkhani zonse. info
التفاسير: