Salin ng mga Kahulugan ng Marangal na Qur'an - Salin sa Wikang Chichewa ni Khalid Ibrahim Bityala

Numero ng Pahina:close

external-link copy
143 : 6

ثَمَٰنِيَةَ أَزۡوَٰجٖۖ مِّنَ ٱلضَّأۡنِ ٱثۡنَيۡنِ وَمِنَ ٱلۡمَعۡزِ ٱثۡنَيۡنِۗ قُلۡ ءَآلذَّكَرَيۡنِ حَرَّمَ أَمِ ٱلۡأُنثَيَيۡنِ أَمَّا ٱشۡتَمَلَتۡ عَلَيۡهِ أَرۡحَامُ ٱلۡأُنثَيَيۡنِۖ نَبِّـُٔونِي بِعِلۡمٍ إِن كُنتُمۡ صَٰدِقِينَ

(Adakulengerani) mitundu isanu ndi itatu ya nyama (pophatikiza zazimuna ndi zazikazi); nkhosa (adalenga) ziwiri (yaimuna ndi yaikazi); mbuzi (adalenga) ziwiri (yaimuna ndi yaikazi). Nena: “Kodi Iye adakuletsani zazimuna zonse ziwiri, (mbuzi ndi nkhosa) kapena zazikazi ziwiri, (nkhosa ndi mbuzi), kapena zomwe zili m’mimba mwa zazikazi ziwirizo? Ndiuzeni mwa nzeru ngati mukunenazi nzoona (kuti Allah adatero). info
التفاسير:

external-link copy
144 : 6

وَمِنَ ٱلۡإِبِلِ ٱثۡنَيۡنِ وَمِنَ ٱلۡبَقَرِ ٱثۡنَيۡنِۗ قُلۡ ءَآلذَّكَرَيۡنِ حَرَّمَ أَمِ ٱلۡأُنثَيَيۡنِ أَمَّا ٱشۡتَمَلَتۡ عَلَيۡهِ أَرۡحَامُ ٱلۡأُنثَيَيۡنِۖ أَمۡ كُنتُمۡ شُهَدَآءَ إِذۡ وَصَّىٰكُمُ ٱللَّهُ بِهَٰذَاۚ فَمَنۡ أَظۡلَمُ مِمَّنِ ٱفۡتَرَىٰ عَلَى ٱللَّهِ كَذِبٗا لِّيُضِلَّ ٱلنَّاسَ بِغَيۡرِ عِلۡمٍۚ إِنَّ ٱللَّهَ لَا يَهۡدِي ٱلۡقَوۡمَ ٱلظَّٰلِمِينَ

Ndipo (adalenganso) ngamira ziwiri, (yaikazi ndi yaimuna). Ng’ombe (adalenganso) ziwiri, (yaimuna ndi yaikazi). Nena: “Kodi (Iye) adakuletsani zazimuna zonse ziwiri (ngamira ndi ng’ombe), kapena zazikazi zonse ziwiri (ngamira ndi ng’ombe), kapena zomwe zili m’mimba mwa zazikazi ziwirizo? Kodi mudali mboni pamene Allah ankakulamulani izi? Kodi ndi ndani woipitsitsa kuposa amene akupekera bodza Allah kuti asokeretse anthu popanda kudziwa (malamulo a Allah)? Ndithu Allah saongola anthu ochita zoipa. info
التفاسير:

external-link copy
145 : 6

قُل لَّآ أَجِدُ فِي مَآ أُوحِيَ إِلَيَّ مُحَرَّمًا عَلَىٰ طَاعِمٖ يَطۡعَمُهُۥٓ إِلَّآ أَن يَكُونَ مَيۡتَةً أَوۡ دَمٗا مَّسۡفُوحًا أَوۡ لَحۡمَ خِنزِيرٖ فَإِنَّهُۥ رِجۡسٌ أَوۡ فِسۡقًا أُهِلَّ لِغَيۡرِ ٱللَّهِ بِهِۦۚ فَمَنِ ٱضۡطُرَّ غَيۡرَ بَاغٖ وَلَا عَادٖ فَإِنَّ رَبَّكَ غَفُورٞ رَّحِيمٞ

Nena: “Sindikupeza m’zimene zavumbulutsidwa kwa ine choletsedwa (kudya) kwa yemwe akufuna kudya. Pokhapokha chikakhala chakufa chokha, kapena liwende lomwe limachucha, kapena nyama ya nkhumba; chifukwa chakuti zonsezi ndi uve (ndiponso kudya zotere) ndiko kutuluka m’chilamulo cha Allah. Kapena (nyama) yozingidwa popanda kutchulapo dzina la Allah. Koma amene wasimidwa (nkudya zoterezi) popanda kukonda kapena kupyoza Malire, ndithu Mbuye wako Ngokhululuka kwambiri, Ngwachisoni chosatha. (Wotere amamkhululukira)”. info
التفاسير:

external-link copy
146 : 6

وَعَلَى ٱلَّذِينَ هَادُواْ حَرَّمۡنَا كُلَّ ذِي ظُفُرٖۖ وَمِنَ ٱلۡبَقَرِ وَٱلۡغَنَمِ حَرَّمۡنَا عَلَيۡهِمۡ شُحُومَهُمَآ إِلَّا مَا حَمَلَتۡ ظُهُورُهُمَآ أَوِ ٱلۡحَوَايَآ أَوۡ مَا ٱخۡتَلَطَ بِعَظۡمٖۚ ذَٰلِكَ جَزَيۡنَٰهُم بِبَغۡيِهِمۡۖ وَإِنَّا لَصَٰدِقُونَ

(Izi ndi zomwe takuletsani). Naonso Ayuda tidawaletsa kudya nyama iliyonse yokhala ndi zikhadabu, ndipo ng’ombe ndi mbuzi tidawaletsa kudya mafuta ake kupatula mafuta omwe misana yake yasenza, kapena okhala m’matumbo, kapena omwe asakanikirana ndi mafupa. Tidawalipira izi chifukwa cha machimo awo. Ndithu Ife ndioona (pa zomwe tikunenazi). info
التفاسير: