[172] Allah sapereka chilango kwa anthu asanawatumizire Mtumiki. Ndiponso sangawalange pa zinthu zomwe nzosatheka kuzizindikira, pokhapokha Mtumiki atawaphunzitsa, monga kupemphera Swala, kusala m’mwezi wa Ramadan. Koma angawalange pazomwe iwo angathe kuzizindikira kuti nzoipa; monga munthu kumchenjelera mnzake ndi zina zotero.
[173] Ayah iyi ikusonyeza kuti munthu wapatsidwa ufulu wochita kapena kusachita poopera kuti angadzanene kuti adakakamizidwa. Apa nzachidziwikire kuti amene wasankha chabwino adzapeza chabwino. Ndipo yemwe wasankha choipa adzapeza choipa.
[174] Kale anthu osakhulupilira pamene ankalima akafuna kubzala, minda yawo adali kuigawa zigawo ziwiri. Ankati: ‘‘Mbewu za chigawo ichi nza Allah, kuti mbewu zakezo adzazigwiritsa ntchito powapatsa masikini, ana a masiye ndi osowa. Ndipo ankatinso: “Mbewu za gawo ili nzamafano athu omwe ankati ngamnzake a Allah kuti zinthu zotuluka m’menemo ziperekedwe kwa anthu ogwira ntchito m’menemo. Choncho ngati patapezeka mliri pachigawo chomwe ankati zokolola zake nzamafano awo, amatenga chigawo chomwe amati dzinthu dzake nza Allah napereka ku mafano. Koma mliri ukagwera pa chigawo cha Allah, sadali kutenga zamafano nkupereka kwa Allah. Izi amachita ngati mafano ngabwino kuposa Allah.