Kilniojo Korano reikšmių vertimas - Vertimas į čevų k. - Khalid Ibrahim Bitala

Puslapio numeris:close

external-link copy
62 : 10

أَلَآ إِنَّ أَوۡلِيَآءَ ٱللَّهِ لَا خَوۡفٌ عَلَيۡهِمۡ وَلَا هُمۡ يَحۡزَنُونَ

Tamverani! Ndithu okondedwa a Allah sadzakhala ndi mantha (pa tsiku la Qiyâma), ndipo sadzadandaula. info
التفاسير:

external-link copy
63 : 10

ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَكَانُواْ يَتَّقُونَ

(Amenewo ndi) amene adakhulupirira ndi kumuopa (Allah). info
التفاسير:

external-link copy
64 : 10

لَهُمُ ٱلۡبُشۡرَىٰ فِي ٱلۡحَيَوٰةِ ٱلدُّنۡيَا وَفِي ٱلۡأٓخِرَةِۚ لَا تَبۡدِيلَ لِكَلِمَٰتِ ٱللَّهِۚ ذَٰلِكَ هُوَ ٱلۡفَوۡزُ ٱلۡعَظِيمُ

Iwo ali ndi zabwino pa moyo wa dziko lapansi ndi pa tsiku lachimaliziro. Palibe kusintha pa mawu a Allah. Uku ndiko kupambana kwakukulu. info
التفاسير:

external-link copy
65 : 10

وَلَا يَحۡزُنكَ قَوۡلُهُمۡۘ إِنَّ ٱلۡعِزَّةَ لِلَّهِ جَمِيعًاۚ هُوَ ٱلسَّمِيعُ ٱلۡعَلِيمُ

Ndipo (iwe, Mtumiki) zisakudandaulitse zonena zawo (zomwe akukunenera monyoza). Ndithu ulemelero ndi mphamvu zonse nza Allah. Iye Ngwakumva, Ngodziwa. info
التفاسير:

external-link copy
66 : 10

أَلَآ إِنَّ لِلَّهِ مَن فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَمَن فِي ٱلۡأَرۡضِۗ وَمَا يَتَّبِعُ ٱلَّذِينَ يَدۡعُونَ مِن دُونِ ٱللَّهِ شُرَكَآءَۚ إِن يَتَّبِعُونَ إِلَّا ٱلظَّنَّ وَإِنۡ هُمۡ إِلَّا يَخۡرُصُونَ

Tamverani! Ndithu (zonse) za kumwamba ndi za pansi, nza Allah. Ndipo amene akupembedza zina kusiya Allah, satsatira aphatikizi (a Allah). Akungotsatira zoganizira, ndipo iwo sanena china koma bodza basi. info
التفاسير:

external-link copy
67 : 10

هُوَ ٱلَّذِي جَعَلَ لَكُمُ ٱلَّيۡلَ لِتَسۡكُنُواْ فِيهِ وَٱلنَّهَارَ مُبۡصِرًاۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَأٓيَٰتٖ لِّقَوۡمٖ يَسۡمَعُونَ

Iye (Allah) ndi Yemwe adakupangirani usiku kuti muzipumamo, ndi (adakupangirani) usana kukhala wowala (kuti mupenye). Ndithu m’zimene muli zisonyezo (zosonyeza chifundo cha Allah pa zolengedwa Zake) kwa anthu akumva. info
التفاسير:

external-link copy
68 : 10

قَالُواْ ٱتَّخَذَ ٱللَّهُ وَلَدٗاۗ سُبۡحَٰنَهُۥۖ هُوَ ٱلۡغَنِيُّۖ لَهُۥ مَا فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَمَا فِي ٱلۡأَرۡضِۚ إِنۡ عِندَكُم مِّن سُلۡطَٰنِۭ بِهَٰذَآۚ أَتَقُولُونَ عَلَى ٱللَّهِ مَا لَا تَعۡلَمُونَ

Akunena: “Allah wadzipangira mwana.” Wapatukana ndi zimenezo! Iye Ngokwanira, (salakalaka mwana ngakhale mthangati aliyense). NdiZake (zonse) za kumwamba ndi za pansi. Inu mulibe umboni pa zimenezi. Kodi mukumnenera Allah zomwe simukuzidziwa? info
التفاسير:

external-link copy
69 : 10

قُلۡ إِنَّ ٱلَّذِينَ يَفۡتَرُونَ عَلَى ٱللَّهِ ٱلۡكَذِبَ لَا يُفۡلِحُونَ

Nena: “Ndithu amene akumpekera Allah bodza, sadzapambana.” info
التفاسير:

external-link copy
70 : 10

مَتَٰعٞ فِي ٱلدُّنۡيَا ثُمَّ إِلَيۡنَا مَرۡجِعُهُمۡ ثُمَّ نُذِيقُهُمُ ٱلۡعَذَابَ ٱلشَّدِيدَ بِمَا كَانُواْ يَكۡفُرُونَ

Ndichisangalalo chochepa basi m’dziko lapansi. Kenako kwa Ife ndiwo mabwelero awo. Kenako tidzawalawitsa chilango chaukali chifukwa cha kusakhulupirira kwawo. info
التفاسير: