Kilniojo Korano reikšmių vertimas - Vertimas į čevų k. - Khalid Ibrahim Bitala

Puslapio numeris:close

external-link copy
43 : 10

وَمِنۡهُم مَّن يَنظُرُ إِلَيۡكَۚ أَفَأَنتَ تَهۡدِي ٱلۡعُمۡيَ وَلَوۡ كَانُواْ لَا يُبۡصِرُونَ

Ndipo alipo ena mwa iwo amene akukutong’olera maso (kukuyang’ana monyoza). Kodi iwe ungathe kuwatsogolera akhungu, chikhalirecho sali openya? info
التفاسير:

external-link copy
44 : 10

إِنَّ ٱللَّهَ لَا يَظۡلِمُ ٱلنَّاسَ شَيۡـٔٗا وَلَٰكِنَّ ٱلنَّاسَ أَنفُسَهُمۡ يَظۡلِمُونَ

Ndithu Allah sachitira anthu choipa chilichonse. Koma anthu akudzichitira okha zoipa. (Adapatsidwa nzeru, koma sazigwiritsa ntchito). info
التفاسير:

external-link copy
45 : 10

وَيَوۡمَ يَحۡشُرُهُمۡ كَأَن لَّمۡ يَلۡبَثُوٓاْ إِلَّا سَاعَةٗ مِّنَ ٱلنَّهَارِ يَتَعَارَفُونَ بَيۡنَهُمۡۚ قَدۡ خَسِرَ ٱلَّذِينَ كَذَّبُواْ بِلِقَآءِ ٱللَّهِ وَمَا كَانُواْ مُهۡتَدِينَ

Ndipo (akumbutse za) tsiku lomwe adzawasonkhanitsa (onse) ngati kuti sadakhale (pa dziko lapansi) koma ola limodzi la usana (atathedwa nzeru). Adzazindikirana pakati pawo; (koma aliyense sadzalabadira mnzake). Ndithu aonongeka amene adatsutsa za kukumana ndi Allah ndipo sadali oongoka. info
التفاسير:

external-link copy
46 : 10

وَإِمَّا نُرِيَنَّكَ بَعۡضَ ٱلَّذِي نَعِدُهُمۡ أَوۡ نَتَوَفَّيَنَّكَ فَإِلَيۡنَا مَرۡجِعُهُمۡ ثُمَّ ٱللَّهُ شَهِيدٌ عَلَىٰ مَا يَفۡعَلُونَ

Ndipo ngati tingakusonyeze (pompano pa dziko lapansi) zina mwa zomwe tikuwalonjeza ndikuwachenjeza nazo, kapena kukubweretsera imfa (usadazione zimenezo), kobwerera kwawo nkwa Ife basi. Kenako Allah ndi mboni pa zomwe akuchita. info
التفاسير:

external-link copy
47 : 10

وَلِكُلِّ أُمَّةٖ رَّسُولٞۖ فَإِذَا جَآءَ رَسُولُهُمۡ قُضِيَ بَيۡنَهُم بِٱلۡقِسۡطِ وَهُمۡ لَا يُظۡلَمُونَ

Ndipo fuko lililonse lili ndi Mtumiki ndipo akazabwera Mtumiki wawo (tsiku la chiweruziro), kudzaweruzidwa pakati pawo mwa chilungamo ndipo sadzaponderezedwa. info
التفاسير:

external-link copy
48 : 10

وَيَقُولُونَ مَتَىٰ هَٰذَا ٱلۡوَعۡدُ إِن كُنتُمۡ صَٰدِقِينَ

Ndipo akunena (osakhulupirira): “Kodi lonjezo ili lidzachitika liti ngati mukunena zoona?” info
التفاسير:

external-link copy
49 : 10

قُل لَّآ أَمۡلِكُ لِنَفۡسِي ضَرّٗا وَلَا نَفۡعًا إِلَّا مَا شَآءَ ٱللَّهُۗ لِكُلِّ أُمَّةٍ أَجَلٌۚ إِذَا جَآءَ أَجَلُهُمۡ فَلَا يَسۡتَـٔۡخِرُونَ سَاعَةٗ وَلَا يَسۡتَقۡدِمُونَ

Nena: “Ndilibe mphamvu mwandekha pa (kudzichotsera) vuto ngakhale (kudzibweretsera) thandizo. (Nanga za zimenezo ndingadziweponji)? Koma chimene Allah wafuna (ndi chomwe chimachitika). M’badwo uli wonse uli ndi nthawi yake (yofera). Nthawi yawo (yofera) ikadza sangathe kuichedwetsa ola limodzi ngakhale kuifulumizitsa.” info
التفاسير:

external-link copy
50 : 10

قُلۡ أَرَءَيۡتُمۡ إِنۡ أَتَىٰكُمۡ عَذَابُهُۥ بَيَٰتًا أَوۡ نَهَارٗا مَّاذَا يَسۡتَعۡجِلُ مِنۡهُ ٱلۡمُجۡرِمُونَ

Nena: “Kodi mukuona bwanji, ngati chilango chakecho chitakudzerani usiku kapena usana (mungathe kuthawa)? Nanga bwanji ochimwa akuchifulumizitsa (kuti chidze mwachangu)?” info
التفاسير:

external-link copy
51 : 10

أَثُمَّ إِذَا مَا وَقَعَ ءَامَنتُم بِهِۦٓۚ ءَآلۡـَٰٔنَ وَقَدۡ كُنتُم بِهِۦ تَسۡتَعۡجِلُونَ

“Kodi chikadza ndipamene mudzachikhulupirire?” Panthawiyo mudzauzidwa): “Kodi tsopano (ndi pamene mukukhulupirira), chikhalirecho mudali kuchifulumizitsa (kale)?” info
التفاسير:

external-link copy
52 : 10

ثُمَّ قِيلَ لِلَّذِينَ ظَلَمُواْ ذُوقُواْ عَذَابَ ٱلۡخُلۡدِ هَلۡ تُجۡزَوۡنَ إِلَّا بِمَا كُنتُمۡ تَكۡسِبُونَ

Kenako kudzanenedwa kwa amene adachita zoipa: “Lawani chilango chamuyaya! Kodi mungalipidwe zina osakhala zomwe mudazipata (kuchokera m’zochita zanu zoipa)?” info
التفاسير:

external-link copy
53 : 10

۞ وَيَسۡتَنۢبِـُٔونَكَ أَحَقٌّ هُوَۖ قُلۡ إِي وَرَبِّيٓ إِنَّهُۥ لَحَقّٞۖ وَمَآ أَنتُم بِمُعۡجِزِينَ

Eti akukufunsa: “Kodi nzoona izo (zimene ukunena)?” Nena: “Inde! Ndikulumbira kwa Mbuye wanga, zimenezo ndi zoona. Ndipo inu simuli olepheretsa (Allah).” info
التفاسير: