[216] Pemphero la okhulupilira lidzakhala kumuyeretsa Allah kuzimene adali kumunenera osakhulupilira pa dziko lapansi. Nayenso Allah adzakhala akuwalonjera. Ndipo nawo adzakhala akulonjerananso wina ndi mnzake. Uku nkutsimikizira mtendere ndi kukhazikika kopanda kutekeseka ndi china chilichonse. Ndipo nthawi zonse kothera kwa mapemphero awo ndi kuthokoza Allah powalimbikitsa pa chikhulupiliro.
[217] Munthu vuto likamkhudza mthupi mwake, kapena pachuma chake ndi mwina motero apo mpomwe amazindikira za kufooka kwake. Amayamba kumkuwira Mbuye wake Allah ndi kumpempha m‘kakhalidwe kake konse- chogona, chokhala, choimilira kuti amchotsere mliri umene wamgwera. Koma Allah akamuyankha namchotsera vutolo amamfulatira Allah napitiriza kumlakwira naiwala ubwino wa Allah ngati kuti vuto silidamkhudze, ngati kutinso sadampempheko Allah. Ichi ndicho chikhalidwe cha anthu ambiri. Amadziwa Allah pomwe mavuto akawagwera. Koma akakhala pamtendere Allah amamuiwala.