[218] Ndithudi, anthu mchilengedwe chawo adali a mpingo umodzi wogonjera Allah mwa chilengedwe. Kenako Allah adawatumizira aneneri kuti awatsogolere kunjira Yake molingana ndi chilamulo chake Allah. Koma ngakhale zili tere anthu adali ndi ufulu mwa chilengedwe chawo kulandira choipa kapena chabwino. Potero, choipa chidawagonjetsa ena a iwo natsata zilakolako za satana. Nasiyana ndi anzawo chifukwa chazimenezo. Komatu padali lamulo la Allah la pachiyambi loti oipa sadzawalanga mwachangu koma kufikira nthawi yawo itakwana. Pakadapanda lamuloli ndiye kuti onse akadawalanga nthawi yomweyo.