Kilniojo Korano reikšmių vertimas - Vertimas į čevų k. - Khalid Ibrahim Bitala

Puslapio numeris:close

external-link copy
26 : 10

۞ لِّلَّذِينَ أَحۡسَنُواْ ٱلۡحُسۡنَىٰ وَزِيَادَةٞۖ وَلَا يَرۡهَقُ وُجُوهَهُمۡ قَتَرٞ وَلَا ذِلَّةٌۚ أُوْلَٰٓئِكَ أَصۡحَٰبُ ٱلۡجَنَّةِۖ هُمۡ فِيهَا خَٰلِدُونَ

Ndipo omwe achita zabwino, adzapata (malipiro) abwino ndi zoonjezera. Ndipo fumbi silikavindikira nkhope zawo. Ndiponso kunyozeka sikukawapeza. Iwowo ndiwo anthu a ku Munda wamtendere; mmenemo akakhala nthawi yaitali. info
التفاسير:

external-link copy
27 : 10

وَٱلَّذِينَ كَسَبُواْ ٱلسَّيِّـَٔاتِ جَزَآءُ سَيِّئَةِۭ بِمِثۡلِهَا وَتَرۡهَقُهُمۡ ذِلَّةٞۖ مَّا لَهُم مِّنَ ٱللَّهِ مِنۡ عَاصِمٖۖ كَأَنَّمَآ أُغۡشِيَتۡ وُجُوهُهُمۡ قِطَعٗا مِّنَ ٱلَّيۡلِ مُظۡلِمًاۚ أُوْلَٰٓئِكَ أَصۡحَٰبُ ٱلنَّارِۖ هُمۡ فِيهَا خَٰلِدُونَ

Ndipo amene akolola zoipa (kuchokera m’zochita zawo zoipa) mphoto ya choipa ndiyofanana ndi icho; ndipo kunyozeka kudzawapeza; sadzakhala ndi aliyense wotha kuwateteza ku chilango cha Allah. Nkhope zawo zidzakhala ngati zaphimbidwa ndi zidutswa za usiku wa m’dima, (zidzakhala zakuda kwambiri); awo ndiwo anthu a ku Moto. Iwo mmenemo adzakhala nthawi yaitali. info
التفاسير:

external-link copy
28 : 10

وَيَوۡمَ نَحۡشُرُهُمۡ جَمِيعٗا ثُمَّ نَقُولُ لِلَّذِينَ أَشۡرَكُواْ مَكَانَكُمۡ أَنتُمۡ وَشُرَكَآؤُكُمۡۚ فَزَيَّلۡنَا بَيۡنَهُمۡۖ وَقَالَ شُرَكَآؤُهُم مَّا كُنتُمۡ إِيَّانَا تَعۡبُدُونَ

Ndipo (akumbutse za) tsiku lomwe tidzawasonkhanitsa onse. Kenako tidzawauza amene ankaphatikiza (Allah ndi mafano kuti): “Imani pompo inu pamodzi ndi aphatikizi anuwo.” Ndipo tidzawasiyanitsa pakati pawo; koma aphatikizi awowo adzati: “Simudali kutipembedza ife (koma mudali kupembedza zilakolako zanu).” info
التفاسير:

external-link copy
29 : 10

فَكَفَىٰ بِٱللَّهِ شَهِيدَۢا بَيۡنَنَا وَبَيۡنَكُمۡ إِن كُنَّا عَنۡ عِبَادَتِكُمۡ لَغَٰفِلِينَ

“Allah akukwanira kukhala mboni pakati pathu ndi pakati panu. Ndithu ife sitidali kuzindikira za mapemphero anu. (Sitinkazindikira kuti inu mukutipembedza).” info
التفاسير:

external-link copy
30 : 10

هُنَالِكَ تَبۡلُواْ كُلُّ نَفۡسٖ مَّآ أَسۡلَفَتۡۚ وَرُدُّوٓاْ إِلَى ٱللَّهِ مَوۡلَىٰهُمُ ٱلۡحَقِّۖ وَضَلَّ عَنۡهُم مَّا كَانُواْ يَفۡتَرُونَ

Kumeneko munthu aliyense adzadziwa zimene adatsogoza; ndipo adzabwezedwa kwa Allah, Mbuye wawo Woona ndipo zidzawasowa zimene adali kupeka. info
التفاسير:

external-link copy
31 : 10

قُلۡ مَن يَرۡزُقُكُم مِّنَ ٱلسَّمَآءِ وَٱلۡأَرۡضِ أَمَّن يَمۡلِكُ ٱلسَّمۡعَ وَٱلۡأَبۡصَٰرَ وَمَن يُخۡرِجُ ٱلۡحَيَّ مِنَ ٱلۡمَيِّتِ وَيُخۡرِجُ ٱلۡمَيِّتَ مِنَ ٱلۡحَيِّ وَمَن يُدَبِّرُ ٱلۡأَمۡرَۚ فَسَيَقُولُونَ ٱللَّهُۚ فَقُلۡ أَفَلَا تَتَّقُونَ

Nena: “Kodi ndani akukupatsani (zopatsa) kuchokera kumwamba (povumbwitsa mvula), ndi pansi (pomeretsa mmera)? Nanga ndani amakupatsani kumva ndi kupenya? Nanga ndani amene akutulutsa chamoyo kuchokera m’chakufa, ndi kutulutsa chakufa kuchokera m’chamoyo? Nanga ndani akukonza zinthu zonse?” Anena: “Ndi Allah.” Choncho, nena: “Kodi bwanji simukumuopa?” info
التفاسير:

external-link copy
32 : 10

فَذَٰلِكُمُ ٱللَّهُ رَبُّكُمُ ٱلۡحَقُّۖ فَمَاذَا بَعۡدَ ٱلۡحَقِّ إِلَّا ٱلضَّلَٰلُۖ فَأَنَّىٰ تُصۡرَفُونَ

Uyo ndi Allah, Mbuye wanu Woona; nanga pali chiyani pambuyo poleka choonadi, sikusokera basi? Kodi nanga mukutembenuzidwa chotani (kusiya choonadi)? info
التفاسير:

external-link copy
33 : 10

كَذَٰلِكَ حَقَّتۡ كَلِمَتُ رَبِّكَ عَلَى ٱلَّذِينَ فَسَقُوٓاْ أَنَّهُمۡ لَا يُؤۡمِنُونَ

Momwemo liwu la Mbuye wako latsimikizika kwa amene adatuluka m’chilamulo cha Allah kuti iwo sadzakhulupirira. info
التفاسير: