[105] Ndime iyi ikulimbikitsa za kuopa Allah ndi kumulemekeza potsatira malamulo ake ndi kupewa zomwe Iye waletsa. Iye ndi amene adakulenga. Ndiyemwenso adalenga zonse zimene iwe adakulengera. Ngakhale iwe amene utafuna chithandizo kwa anzako umampempha ponena kuti: ‘‘Ndikukupempha m’dzina la Allah kuti undichitire chakuti.” Izi umachita poona kuti iye adzalemekeza dzina la Allah, ndipo adzakwaniritsa chomwe ukufunacho. Koma nanga bwanji ukuchita zimene Allah waletsa? Bwanji sukulemekeza lamulo lake pomwe iwe ukufuna kuti anthu achite zomwe sukuchita. Apa akutiuzanso kuti Allah akuona chilichonse chimene anthu ake akuchita, ngakhale chikhale chochepa chotani.
[106] Maulama onse a malamulo a Chisilamu adamvana kuti ndime iyi yaika malire amitala yomwe munthu akhoza kukwatira. Ndipo ikuletsa kukwatira akazi opyola anayi pa nthawi imodzi.
[107] Kumuitanitsa chiwongo mkazi wako chimene udampatsa kapena kumlipitsa ndalama iliyonse, zotere nzosaloledwa. Koma ngati iye mwini atakugawira mokoma mtima kachinthu kam’chiwongocho landira usamkanire. Monga iwe umampatsa, iyenso akhoza kukupatsa.
[108] Ayang’aniri a ana amasiye, monga momwe awauzira kuti asawachenjelere ana amasiye koma kuti awapatse chuma chawo mokwanira, apa akuwauzanso kuti apitirize kuyang’anira chuma cha ana amasiyewo. Asawapatse pomwe sali ozindikira zinthu, ali ofooka m’maganizo pomwe sakuzindikira kufunika kwa chuma kuopa kuti angasakaze chumacho. Tero asawapatse ngakhale misinkhu yawo ili yaikulu. Koma apitirize kuwasungira chumacho ndi kumawauza mawu abwino ponena kuti: “Mpaka pano ndikuona kuti mwanokha simungathe kuchiyendetsa bwino chuma chanu. Tero ndiloleni ndikusungirenibe mpaka nthawi yochepa kutsogoloku. Ndikadzaona kuti nzeru zakhazikika apo mpomwe ndidzakupatsani chumachi.”
[109] Komatu akhale akumuyesayesa wamasiyeyo pomusiira kuti nthawi zina aziyendetsapo yekha chumacho kuti aphunzire kasamalidwe kake. Akaona kuti akukhoza, ampatse asamuchedwetsere mwadala.