[142] Achiphamaso amabisa zochita zawo kwa anthu kuti asazione. Koma salabadira kuonedwa ndi Allah pomwe Allah Njemwe adzawalipira. Pomwe Allah akudziwa zonse zimene zikuyenda m’mitima mwawo ndiponso akumva ndi kuziona zonse zimene akuchita. Kunali kofunika kwa iwo kumuopa Allah amene ali ndi mphamvu zochitira chilichonse chimene wafuna.
[143] M’ndime iyi Allah akuletsa anthu kuti asakhalire kumbuyo anthu oipa koma awaleke kuti awalange chifukwa cha zoipa zawo ndi kuti amene adamuchitirapo zoipa apeze bwino muntima mwake. Choncho aweruzi amilandu achenjere kukhalira kumbuyo anthu oipa omwe ali nawo chitsimikizo kuti adachenjelera anzawo. Asaone ulemelero wa munthu mmene ulili ngakhale ali ndi chuma chotani. Koma m’malomwake akhalire kumbuyo amene ali oponderezedwa. Akatero adzapeza mphoto yomwe Allah walonjeza chifukwa cha kusonyeza choonadi poyera. Aweruzi akagwira njira imeneyi ndiye kuti adzapambana pano padziko lapansi mpaka patsiku la chiweruziro.
[144] Allah akuwalimbikitsa ochimwa: Kuti (a) atembenukire kwa Iye mwachangu ndi kusiya zimene akuchitazo. (b) Atsimikize mu mtima kuti sadzachitanso uchimowo. (c) Adandaule pa uchimo umene adauchitawo. (d) Awabwezere eni zinthu zomwe adazitenga mwachinyengo. (e) Akawapemphe kuti awakhululukire. Akakwaniritsa zonsezi ndiye kuti kulapa kwawo Allah akuvomera.
[145] M’ndime iyi akuti munthu wochitira anthu anzake zoipa.akudzipha yekha pakuti Allah sadzamleka koma amkhaulitsa pompano pa dziko lapansi kapena pakutha kwa dziko.
[146] Pali anthu ena amene amaukwera uchimo. Kenako nkumnamizira wina wake. Munthu wamakhalidwe awa, chiweruzo chake chidzakhala choopsa tsiku lachimaliziro, ngakhale wadzipulumutsa pano pa dziko lapansi chifukwa chakuthyathyalika kwake. Kapena pompano pa dziko lapansi amachiona chomwe chinameta nkhanga mpala.
[147] Apa Allah akunena kuti palibe chisomo chimene Allah wapatsa munthu chachikulu ndi chopindulitsa kuposa luntha. Chilichonse chabwino cha pa dziko lapansi ndi pa tsiku lachimaliziro chimapezeka chifukwa cha kudziwa zinthu. Qur’an yonse ndi hadisi za Mtumiki zikulimbikitsa zakufunafuna luntha lodziwira zinthu zakuti zimkonzere munthu za dziko lapansi ndi za tsiku lachimaliziro, kotero kuti Qur’an ndi hadisizo zikunena kuti munthu apite kunja kunka nafunafuna maphunziro.