Prijevod značenja časnog Kur'ana - Prijevod na čeva jezik - Halid Ibrahim Betala

Broj stranice:close

external-link copy
45 : 4

وَٱللَّهُ أَعۡلَمُ بِأَعۡدَآئِكُمۡۚ وَكَفَىٰ بِٱللَّهِ وَلِيّٗا وَكَفَىٰ بِٱللَّهِ نَصِيرٗا

Ndipo Allah akudziwa bwinobwino za adani anu. Ndipo Allah akukwanira kukhala Mtetezi. Allah akukwananso kukhala Mthandizi. info
التفاسير:

external-link copy
46 : 4

مِّنَ ٱلَّذِينَ هَادُواْ يُحَرِّفُونَ ٱلۡكَلِمَ عَن مَّوَاضِعِهِۦ وَيَقُولُونَ سَمِعۡنَا وَعَصَيۡنَا وَٱسۡمَعۡ غَيۡرَ مُسۡمَعٖ وَرَٰعِنَا لَيَّۢا بِأَلۡسِنَتِهِمۡ وَطَعۡنٗا فِي ٱلدِّينِۚ وَلَوۡ أَنَّهُمۡ قَالُواْ سَمِعۡنَا وَأَطَعۡنَا وَٱسۡمَعۡ وَٱنظُرۡنَا لَكَانَ خَيۡرٗا لَّهُمۡ وَأَقۡوَمَ وَلَٰكِن لَّعَنَهُمُ ٱللَّهُ بِكُفۡرِهِمۡ فَلَا يُؤۡمِنُونَ إِلَّا قَلِيلٗا

Mwa Ayuda alipo omwe amasintha mawu kuwachotsa m’malo mwake. Ndipo amanena (chabe ndi milomo yawo): “Tamva;” (pomwe mitima yawo ikunena): “Tanyoza.” (Ndipo akunena kuuza Mtumiki): “Imva koma wosamveredwa (ndipo pakati pakuyankhula kwawo amanena mawu akuti) ‘Raaina’ (ncholinga chomnenera kuti iye ndimbutuma), mokhotetsa malilime awo (mu zoyankhula zawo kuti akhale ngati akumunenera zabwino pomwe akumtembelera) ndi cholinga chotukwana chipembedzo (cha Chisilamu). Akadakhala kuti iwo adanena: “Tamva ndipo tamvera; ndipo imva, utiyang’anire,” (mmalo mwa kunena kwawo kwakuti: ‘Raaina’), zikadakhala zabwino ndizolingana kwa iwo. Koma Allah adawatembelera chifukwa cha kusakhulupirira kwawo. Sakhulupirira koma pang’ono basi. info
التفاسير:

external-link copy
47 : 4

يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ أُوتُواْ ٱلۡكِتَٰبَ ءَامِنُواْ بِمَا نَزَّلۡنَا مُصَدِّقٗا لِّمَا مَعَكُم مِّن قَبۡلِ أَن نَّطۡمِسَ وُجُوهٗا فَنَرُدَّهَا عَلَىٰٓ أَدۡبَارِهَآ أَوۡ نَلۡعَنَهُمۡ كَمَا لَعَنَّآ أَصۡحَٰبَ ٱلسَّبۡتِۚ وَكَانَ أَمۡرُ ٱللَّهِ مَفۡعُولًا

E inu amene mwapatsidwa buku! Zikhulupirireni zomwe tavumbulutsa zikutsimikizira zomwe muli nazo tisanazisinthe nkhope zanu ndi kuzitembenuzira kumbuyo kwake, kapena tisanawatembelere monga momwe tidawatembelera omwe sadalemekeze kupatulika kwa tsiku la Sabata. Ndipo lamulo la Allah ndilochitikadi. info
التفاسير:

external-link copy
48 : 4

إِنَّ ٱللَّهَ لَا يَغۡفِرُ أَن يُشۡرَكَ بِهِۦ وَيَغۡفِرُ مَا دُونَ ذَٰلِكَ لِمَن يَشَآءُۚ وَمَن يُشۡرِكۡ بِٱللَّهِ فَقَدِ ٱفۡتَرَىٰٓ إِثۡمًا عَظِيمًا

Ndithudi Allah sangakukhululuke kuphatikizidwa (ndi chinachake), koma amakhululuka (machimo ena) osati amenewa kwa amene wamfuna. Ndipo amene angamphatikize Allah, ndithudi, wadzipekera uchimo waukulu. info
التفاسير:

external-link copy
49 : 4

أَلَمۡ تَرَ إِلَى ٱلَّذِينَ يُزَكُّونَ أَنفُسَهُمۚ بَلِ ٱللَّهُ يُزَكِّي مَن يَشَآءُ وَلَا يُظۡلَمُونَ فَتِيلًا

Kodi sukuwaona omwe akudziyeretsa okha? Koma Allah amamuyeretsa amene wamufuna (pomulimbikitsa kuchita zabwino). Ndipo sadzaponderezedwa ngakhale ndi kachinthu kochepa konga kaulusi kokhala mkati mwakhokho la tende.[126] info

[126] Ayuda adali kunyada chifukwa choti iwo adali nawo aneneri, ndiponso makolo awo omwe adali olungama. Ankati: “Poti makolo athu adali olungama palibe chochititsa mantha pa ife. Uchimo uliwonse umene ife tingachite Allah adzatikhululukira ngakhale uchimowo utakhala waukulu chotani.” Iwo ankadzitchanso kuti adali okondedwa a Allah. Ndipo iwowo ngomwe akuwatchula m’ndime iyi kuti “Kodi saona amene akudziyeretsa okha ndi mawu okha ochokera m’milomo popanda kuchita zimene adawalamula ndi kusiya zomwe adawaletsa?” Mwa Asilamu aliponso ena omwe ali ndi maganizo onga amenewa. Amangonyadira zochita zamakolo awo popanda kutsanzira chikhalidwe chamakolo awowo.

التفاسير:

external-link copy
50 : 4

ٱنظُرۡ كَيۡفَ يَفۡتَرُونَ عَلَى ٱللَّهِ ٱلۡكَذِبَۖ وَكَفَىٰ بِهِۦٓ إِثۡمٗا مُّبِينًا

Taona, momwe akumpekera Allah bodza! Ndipo izi zikukwana kukhala tchimo loonekera! info
التفاسير:

external-link copy
51 : 4

أَلَمۡ تَرَ إِلَى ٱلَّذِينَ أُوتُواْ نَصِيبٗا مِّنَ ٱلۡكِتَٰبِ يُؤۡمِنُونَ بِٱلۡجِبۡتِ وَٱلطَّٰغُوتِ وَيَقُولُونَ لِلَّذِينَ كَفَرُواْ هَٰٓؤُلَآءِ أَهۡدَىٰ مِنَ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ سَبِيلًا

Kodi sukuwaona omwe apatsidwa gawo la nzeru zozindikira buku (la Allah)? Amakhulupirira mafano ndi asatana, ndipo akumati kwa amene sadakhulupirire: “Awa ali panjira yoongoka kwabasi kuposa okhulupirira (Asilamu).”[127] info

[127] Mawu oti “Jibti ndi Twaghut’’ amanena za chinthu chomwe anthu akuchipembedza chamoyo kapena chakufa chomwe sichili Mulungu weniweni monga momwe lilili dzina loti Shaytan. Iloli limatchulidwa kwa aliyense amene akusokeretsa anthu ku njira ya Allah. Chifukwa cha kuipidwa ndi Asilamu, Ayuda adapita ku Makka kukapalana ubwenzi ndi Aquraish ndi Arabu ena opembedza mafano kuti athandizane nawo kumthira nkhondo Mtumiki Muhammad (s.a.w) pamodzi ndi omtsatira ake kuti achithetseretu chipembedzo cha Chisilamu. Choncho akuluakulu a Chiyuda atafika ku Makka adagwadira mafano ncholinga chofuna kukondweretsa Aquraish pomwe Ayudawo adali eni mabuku omwe salola kupembedza mafano. Adawalimbikitsanso Aquraish aja powauza kuti: “Zochita zanu pa chipembedzo chanu nzabwino kuposa zochita za Muhammad pachipembedzo chake chimene wadza nacho.” Iwo amanena izi akudziwa kuti akunama. Cholinga chawo kudali kupeza chithandizo kwa iwo kuti athetse Chisilamu chifukwa chakudzadzidwa ndi njiru m’mitima mwawo ponena kuti: “Nchotani kuti Muhammad (s.a.w) alandire chisomo chauneneri?” Iwo ankachita izi ngati kuti ufumu wa Allah udali m’manja mwawo kuti iwo ndi amene amagawa zachifundo cha Allah, chonsecho, Allah amapereka kwa yemwe wamfuna. Iye amachita chimene wafuna. Safunsidwa ndi aliyense pa chimene wachita. Koma iwo amafunsidwa.

التفاسير: