ترجمهٔ معانی قرآن کریم - ترجمه‌ى چوایی - خالد ابراهیم بيتالا

An-Nisâ’

external-link copy
1 : 4

يَٰٓأَيُّهَا ٱلنَّاسُ ٱتَّقُواْ رَبَّكُمُ ٱلَّذِي خَلَقَكُم مِّن نَّفۡسٖ وَٰحِدَةٖ وَخَلَقَ مِنۡهَا زَوۡجَهَا وَبَثَّ مِنۡهُمَا رِجَالٗا كَثِيرٗا وَنِسَآءٗۚ وَٱتَّقُواْ ٱللَّهَ ٱلَّذِي تَسَآءَلُونَ بِهِۦ وَٱلۡأَرۡحَامَۚ إِنَّ ٱللَّهَ كَانَ عَلَيۡكُمۡ رَقِيبٗا

E inu anthu! Opani Mbuye wanu yemwe adakulengani kuchokera mwa munthu mmodzi (Adam) ndipo adalenga mmenemo mkazi wake (Hawa), ndipo adafalitsa amuna ndi akazi ambiri kuchokera mwa awiriwo. Ndipo opani Allah yemwe kupyolera mwa Iye mumapemphana. Ndipo (sungani) chibale. Ndithudi Allah Ndimyang’aniri pa inu (akuona chilichonse chimene muchita).[105] info

[105] Ndime iyi ikulimbikitsa za kuopa Allah ndi kumulemekeza potsatira malamulo ake ndi kupewa zomwe Iye waletsa. Iye ndi amene adakulenga. Ndiyemwenso adalenga zonse zimene iwe adakulengera. Ngakhale iwe amene utafuna chithandizo kwa anzako umampempha ponena kuti: ‘‘Ndikukupempha m’dzina la Allah kuti undichitire chakuti.” Izi umachita poona kuti iye adzalemekeza dzina la Allah, ndipo adzakwaniritsa chomwe ukufunacho. Koma nanga bwanji ukuchita zimene Allah waletsa? Bwanji sukulemekeza lamulo lake pomwe iwe ukufuna kuti anthu achite zomwe sukuchita. Apa akutiuzanso kuti Allah akuona chilichonse chimene anthu ake akuchita, ngakhale chikhale chochepa chotani.

التفاسير:

external-link copy
2 : 4

وَءَاتُواْ ٱلۡيَتَٰمَىٰٓ أَمۡوَٰلَهُمۡۖ وَلَا تَتَبَدَّلُواْ ٱلۡخَبِيثَ بِٱلطَّيِّبِۖ وَلَا تَأۡكُلُوٓاْ أَمۡوَٰلَهُمۡ إِلَىٰٓ أَمۡوَٰلِكُمۡۚ إِنَّهُۥ كَانَ حُوبٗا كَبِيرٗا

Ndipo apatseni ana amasiye chuma chawo; musasinthanitse choipa ndi chabwino. Ndipo musadye chuma chawo pochiphatikiza ndi chuma chanu. Ndithudi, (zonsezo) ndiuchimo waukulu. info
التفاسير:

external-link copy
3 : 4

وَإِنۡ خِفۡتُمۡ أَلَّا تُقۡسِطُواْ فِي ٱلۡيَتَٰمَىٰ فَٱنكِحُواْ مَا طَابَ لَكُم مِّنَ ٱلنِّسَآءِ مَثۡنَىٰ وَثُلَٰثَ وَرُبَٰعَۖ فَإِنۡ خِفۡتُمۡ أَلَّا تَعۡدِلُواْ فَوَٰحِدَةً أَوۡ مَا مَلَكَتۡ أَيۡمَٰنُكُمۡۚ ذَٰلِكَ أَدۡنَىٰٓ أَلَّا تَعُولُواْ

Ngati mwaopa kuti simungachite chilungamo pa amasiye (opaninso kusawachitira chilungamo akazi pamitala), choncho kwatirani amene mukuwafuna mwa akazi; awiri, kapena atatu, kapena anayi (basi). Koma ngati mukuopa kuti simungathe kuchita chilungamo, (kwatirani) mmodzi basi kapena amene manja anu akumanja adapeza (mdzakazi). Kutero kudzakuchititsani kuti musapendekere (kumbali yosalungama).[106] info

[106] Maulama onse a malamulo a Chisilamu adamvana kuti ndime iyi yaika malire amitala yomwe munthu akhoza kukwatira. Ndipo ikuletsa kukwatira akazi opyola anayi pa nthawi imodzi.

التفاسير:

external-link copy
4 : 4

وَءَاتُواْ ٱلنِّسَآءَ صَدُقَٰتِهِنَّ نِحۡلَةٗۚ فَإِن طِبۡنَ لَكُمۡ عَن شَيۡءٖ مِّنۡهُ نَفۡسٗا فَكُلُوهُ هَنِيٓـٔٗا مَّرِيٓـٔٗا

Ndipo akazi apatseni chiwongo chawo monga mphatso. Koma (akazi anuwo) ngati atakupatsani mokoma mtima chilichonse (m’chiwongocho), idyani mokondwa ndi mothandizika nacho.[107] info

[107] Kumuitanitsa chiwongo mkazi wako chimene udampatsa kapena kumlipitsa ndalama iliyonse, zotere nzosaloledwa. Koma ngati iye mwini atakugawira mokoma mtima kachinthu kam’chiwongocho landira usamkanire. Monga iwe umampatsa, iyenso akhoza kukupatsa.

التفاسير:

external-link copy
5 : 4

وَلَا تُؤۡتُواْ ٱلسُّفَهَآءَ أَمۡوَٰلَكُمُ ٱلَّتِي جَعَلَ ٱللَّهُ لَكُمۡ قِيَٰمٗا وَٱرۡزُقُوهُمۡ فِيهَا وَٱكۡسُوهُمۡ وَقُولُواْ لَهُمۡ قَوۡلٗا مَّعۡرُوفٗا

Ozerezeka musawapatse chuma chanu chomwe Allah wachichita kukhala cholimbitsa matupi anu ndi moyo wanu. Koma adyetseni nacho ndikuwaveka nacho ndikuwauza mawu abwino (monga kuti: Mukadzakula ndikukhala olungama, tidzakupatsani chuma chanu).[108] info

[108] Ayang’aniri a ana amasiye, monga momwe awauzira kuti asawachenjelere ana amasiye koma kuti awapatse chuma chawo mokwanira, apa akuwauzanso kuti apitirize kuyang’anira chuma cha ana amasiyewo. Asawapatse pomwe sali ozindikira zinthu, ali ofooka m’maganizo pomwe sakuzindikira kufunika kwa chuma kuopa kuti angasakaze chumacho. Tero asawapatse ngakhale misinkhu yawo ili yaikulu. Koma apitirize kuwasungira chumacho ndi kumawauza mawu abwino ponena kuti: “Mpaka pano ndikuona kuti mwanokha simungathe kuchiyendetsa bwino chuma chanu. Tero ndiloleni ndikusungirenibe mpaka nthawi yochepa kutsogoloku. Ndikadzaona kuti nzeru zakhazikika apo mpomwe ndidzakupatsani chumachi.”

التفاسير:

external-link copy
6 : 4

وَٱبۡتَلُواْ ٱلۡيَتَٰمَىٰ حَتَّىٰٓ إِذَا بَلَغُواْ ٱلنِّكَاحَ فَإِنۡ ءَانَسۡتُم مِّنۡهُمۡ رُشۡدٗا فَٱدۡفَعُوٓاْ إِلَيۡهِمۡ أَمۡوَٰلَهُمۡۖ وَلَا تَأۡكُلُوهَآ إِسۡرَافٗا وَبِدَارًا أَن يَكۡبَرُواْۚ وَمَن كَانَ غَنِيّٗا فَلۡيَسۡتَعۡفِفۡۖ وَمَن كَانَ فَقِيرٗا فَلۡيَأۡكُلۡ بِٱلۡمَعۡرُوفِۚ فَإِذَا دَفَعۡتُمۡ إِلَيۡهِمۡ أَمۡوَٰلَهُمۡ فَأَشۡهِدُواْ عَلَيۡهِمۡۚ وَكَفَىٰ بِٱللَّهِ حَسِيبٗا

Ayeseni amasiye (akayandikira kukula nsinkhu kuti muone kuti atha kuchita ntchito yabwino ndi chuma chawo mukawapatsa), kufikira atafika nthawi yokwatira/kukwatiwa. Ndipo ngati mutawaona kuti ali ndi nzeru zabwino, apatseni chuma chawo. Musachidye mosasamala ndi mwachangu poopa kuti angakule. Ndipo amene ali opeza bwino adziletse (kulandira mphoto yolelera ana amasiyewo). Koma amene ali wosauka adye mwa ubwino (osati moononga). Ndipo pamene mukuwapatsa chuma chawo, funani mboni (zoonelera kuperekedwa kwa chumacho). Ndipo Allah ali Wokwana kukhala Muwelengeri (ndi Woyang’anira).[109] info

[109] Komatu akhale akumuyesayesa wamasiyeyo pomusiira kuti nthawi zina aziyendetsapo yekha chumacho kuti aphunzire kasamalidwe kake. Akaona kuti akukhoza, ampatse asamuchedwetsere mwadala.

التفاسير: