[122] Apa akuti amuna ndi amene akhale ndi ulamuliro pa akazi awo, powatsogolera ku miyambo yabwino. Osati kuti mkazi adzitukumule kwa mwamuna wake poti iye ngophunzira zedi kapena wanzeru zochuluka kotero kuti mwamuna m’nyumba osamuyesa kanthu. Ngati atero ndiye kuti sakhala Asilamu owona. M’ndimeyi atchulamonso makhalidwe ofunika kuti akazi akhale nawo. Ndipo atchulamo malangizo olangira nawo mkazi ngati samvera. Choyamba amchenjeze ndi mawu. Ngati kuchenjezako sikunathandize, asagone naye limodzi pamphasa. Ndipo ngati akupitirizabe kuchita mnyozo akupatsidwa chilolezo mwamuna kuti amlange pommenya mwakumuopyeza, osati kumenya komgulula nako mano. Komabe mahadisi a Mtumiki (s.a.w) akunena kuti asanaganize zommenya ayeseyese kumkonza ponena naye mofewa ndi kumuonetsa kulakwa kwake. Ngati atalephera zonsezi, aitane anthu kuti adzawayanjanitse m’njira yabwino. Naonso anthuwo akhale ndi cholinga choyanjanitsa osati kupasula. Amunanso akuwachenjeza apa kuti iwo ndi amene ali ndi nyonga ndi udindo. Allah ndiye Wamkulu kuposa iwo amunawo. Mawu oti “Hafizatu Lilighaibi” maulama ena akuwatanthauzira kuti “Akhale osunga chinsinsi,” chimene chili pakati pa iwo ndi amuna awo ndi zonse zomwe zimachitika m’nyumba, pakuti nthawi zambiri akazi sakhalira kuulula za m’nyumba.
[123] M’ndime iyi akuwalamula anthu kuti apembedze Allah yekha ndi kumpempha Iye Yekha. Asapembedzenso china chilichonse, chamoyo kapena chakufa. Ndikuti awachitire zabwino makolo ake ndi onse amene awatchula m’ndimeyi. Sibwino kuthandiza anthu akumbali pomwe anthu omwe uli nawo pafupi sunawathandizepo.
[124] Kubisa zonse zomwe Allah wawapatsa kuli monga munthu kukhala ndi maphunziro koma osaphunzitsa anthu kotero kuti nkufa nawo popanda kuphunzitsapo aliyense. Kutero sibwino. Koma akafuna kukalowa m’Munda wa mtendere wa Allah nkofunika kuti achite zinthu zabwino ncholinga chokondweretsa Allah. Osati kuti anthu amuone ndi kumtama. Amene akuchita chinthu chabwino ncholinga choti anthu amtamande, sakalandira mphoto iliyonse pa tsiku lachimaliziro.