আল-কোৰআনুল কাৰীমৰ অৰ্থানুবাদ - চিচেৱা অনুবাদ- খালিদ ইব্ৰাহীম বেতালা

পৃষ্ঠা নং:close

external-link copy
20 : 4

وَإِنۡ أَرَدتُّمُ ٱسۡتِبۡدَالَ زَوۡجٖ مَّكَانَ زَوۡجٖ وَءَاتَيۡتُمۡ إِحۡدَىٰهُنَّ قِنطَارٗا فَلَا تَأۡخُذُواْ مِنۡهُ شَيۡـًٔاۚ أَتَأۡخُذُونَهُۥ بُهۡتَٰنٗا وَإِثۡمٗا مُّبِينٗا

Ndipo ngati mufuna kusintha mkazi wina m’malo mwa wina (pokwatira wina kusiya wakale) pomwe mmodzi wa iwo (woyambayo) mudampatsa milumilu ya chuma, musatenge (kulanda) chilichonse. Kodi mungachitenge mwa chinyengo ndi uchimo woonekera? info
التفاسير:

external-link copy
21 : 4

وَكَيۡفَ تَأۡخُذُونَهُۥ وَقَدۡ أَفۡضَىٰ بَعۡضُكُمۡ إِلَىٰ بَعۡضٖ وَأَخَذۡنَ مِنكُم مِّيثَٰقًا غَلِيظٗا

Kodi mungachitenge bwanji pomwe mudalowana wina ndi mnzake, ndipo (akazi) adalandira kwa inu chipangano cholimba? info
التفاسير:

external-link copy
22 : 4

وَلَا تَنكِحُواْ مَا نَكَحَ ءَابَآؤُكُم مِّنَ ٱلنِّسَآءِ إِلَّا مَا قَدۡ سَلَفَۚ إِنَّهُۥ كَانَ فَٰحِشَةٗ وَمَقۡتٗا وَسَآءَ سَبِيلًا

Ndipo musakwatire akazi amene adakwatiwapo ndi atate anu, kupatula zomwe zidapita, (musabwerezenso kuzichita). Ndithudi, chinthu ichi nchauve ndipo nchodedwa ndiponso ndinjira yoipa.[117] info

[117] Ndime iyi ndi zinzake zotsatira zikufotokoza za akazi omwe ngoletsedwa kuwakwatira pa Shariya ya Chisilamu. Ena mwa akaziwo ndi awa:-
1) Munthu sangakwatire mkazi yemwe bambo wake adamkwatirapo kapena yemwe adakwatiwapo ndi gogo wake wakuchimuna kapena kuchikazi. Koma osati amene adasiidwa ndimalume ake kapena m’bale watate wake. Amenewa akhoza kuwakwatira.
2) Mayi wako yemwe adakubereka ndi mayi wamayi wako.
3) Mwana wako wodziberekera wekha, kapena mwana amene mwana wako adabereka.
4) Tate wako wamkazi (zakhali) ndi alongo agogo ako.
5) Mayi wako wamng’ono (m’bale wamayi wako) ndi m’bale wamkazi wa agogo ako akuchikazi.
6) Mwana wa m’bale wako wobadwa naye bambo ndi mayi mmodzi kapena wobadwa naye mayi mmodzi kapena bambo mmodzi ndi ana onse akazi oberekedwa ndi mwanayo.
7) Mwana wamkazi wa mlongo wako (mfumukazi) wamayi ndi bambo mmodzi kapena wakumbali yabambo yokha kapenanso wakumbali yamayi yokha.
8) Mkazi yemwe adakuyamwitsapo ndi mayi ake amkaziyo kapena omwe adamuyamwitsaponso iye.
9) Mkazi yemwe unayamwa naye bere limodzi.
10) Mayi wamkazi wanu.

التفاسير:

external-link copy
23 : 4

حُرِّمَتۡ عَلَيۡكُمۡ أُمَّهَٰتُكُمۡ وَبَنَاتُكُمۡ وَأَخَوَٰتُكُمۡ وَعَمَّٰتُكُمۡ وَخَٰلَٰتُكُمۡ وَبَنَاتُ ٱلۡأَخِ وَبَنَاتُ ٱلۡأُخۡتِ وَأُمَّهَٰتُكُمُ ٱلَّٰتِيٓ أَرۡضَعۡنَكُمۡ وَأَخَوَٰتُكُم مِّنَ ٱلرَّضَٰعَةِ وَأُمَّهَٰتُ نِسَآئِكُمۡ وَرَبَٰٓئِبُكُمُ ٱلَّٰتِي فِي حُجُورِكُم مِّن نِّسَآئِكُمُ ٱلَّٰتِي دَخَلۡتُم بِهِنَّ فَإِن لَّمۡ تَكُونُواْ دَخَلۡتُم بِهِنَّ فَلَا جُنَاحَ عَلَيۡكُمۡ وَحَلَٰٓئِلُ أَبۡنَآئِكُمُ ٱلَّذِينَ مِنۡ أَصۡلَٰبِكُمۡ وَأَن تَجۡمَعُواْ بَيۡنَ ٱلۡأُخۡتَيۡنِ إِلَّا مَا قَدۡ سَلَفَۗ إِنَّ ٱللَّهَ كَانَ غَفُورٗا رَّحِيمٗا

Kwaletsedwa kwa inu kukwatira amayi anu, ana anu, alongo anu, azakhali anu, amayi anu aang’ono kapena aakulu, ana achikazi am’bale wanu, ana achikazi a mlongo wanu, amayi anu amene adakuyamwitsani, alongo anu oberekedwa ndi amene adakuyamwitsanipo. Mayi a akazi anu, ana achikazi owapeza amene mukuwasunga woberekedwa ndi akazi anu omwe mwalowana nawo. Koma ngati simudalowane nawo, nkosaletsedwa kwa inu kukwatira ana awowo; ndi akazi a ana amuna omwe ngochokera kumisana yanu. Ndiponso nkoletsedwa kwa inu kukwatira mophatikiza mkazi ndi mchemwali wake obadwa naye, kupatula zomwe zidapita. Ndithudi Allah Ngokhululuka kwambiri Ngwachisoni zedi. info
التفاسير: