[128] Ndime 53-54 zikusonyeza kuti zonse zimene Ayuda ankawachitira Asilamu nchifukwa chadumbo basi. Ankawawidwa nawo mitima chifukwa choti Asilamu apeza chisomo cha Allah. Palibe chinthu chimene chimaletsa anthu kutsata choonadi kuposa dumbo. Ngati utamchitira dumbo munthu sungalole kutsata langizo lake lililonse ngakhale litakhala lopindulitsa pano pa dziko lapansi ndi tsiku lachimaliziro Dumbo ndi lomwe likuletsa anthu ambiri kutsata choonadi. Choncho tiyeni tipewe khalidwe limeneli kuti titsatire choonadi paliponse pamene chachokera. Ndikutinso tipeze mtendere m’mitima mwathu. Dziwani kuti dumbo nlomwe lidamchititsa Iblis kukhala wotembeleredwa.
[129] (Ndime 56-57) Apa akutchula za malipiro a anthu ochita zabwino ndi malipiro a anthu ochita zoipa umu ndi momwe ulili ulaliki wa Qur’an. Qur’an ikafotokoza za anthu ochita zoipa imatsatiza pompo kufotokoza zotsatira za anthu ochita zabwino. Pamenepa akunena kuti aliyense adzalandira malipiro a zochita zake, abwino kapena oipa. Sakawomboledwa chifukwa cha ubwino wa munthu wina. Zochita zake ndizo zikamuombola kapena kukamponya kuchionongeko.
[130] Pali anthu ena amene amati anzawo akawasungitsa zinthu kuti akhulupirike pa zimenezo, mwini zinthu uja akafa kapena kuti panalibe umboni wokwanira, amazitenga zinthuzo poganizira kuti palibe chomwe chingawavute popeza mwini zinthuzo adamwalira ndipo umboni wokwanira palibe. Chikhalidwe chotere si cha Chisilamu, Chisilamu sichifuna machitidwe otere.
[131] Aliyense amene amdzoza utsogoleri nkofunika kuti anthu amumvere ngati iye akulamula zabwino. Pagulu la anthu ngati sipakhala mtsogoleri womumvera, ndiye kuti pamapezeka zisokonezo ndi ziwawa kotero kuti zinthu zawo siziyenda bwino. Chisilamu sichiloleza machitidwe achipolowe ndi ziwawa. Chisilamu chimakonda bata ndi mtendere ndi kuti pasapezeke anthu ena owachenjelera anzawo. Komatu atsogoleriwo awamvere akalamula mwa chilungamo popanda kulakwira Allah. Koma ngati akulakwira Allah asawamvere. Pamenepo atsate chomwe Allah wawalamula ndi Mtumiki Wake.