[151] Indedi, Allah sakonda anthu ofalitsa zoipa za anzawo popanda choipa chilichonse chimene awachitira. Koma munthu amene ena amchitira choipa akumlola kutchula kuipa komwe ena amchitira pokamnenera kwa muweruzi kuti muweruziyo amuthandize pa amene amchitira zoipawo. Koma kulengeza kuipa kwa anthu ena nkosaloledwa m’chisilamu. Ndipo ndi uchimo waukulu.
[152] Aliyense mwa anthu yemwe Allah wamuvomereza kuti ndi mtumiki Wake, ndipo iwe nkukana kumkhulupilira, monga Ayuda mmene amamkanira mneneri Isa (Yesu), ndi Akhrisitu mmene amamkanira mneneri Muhammad (s.a.w), kutereko nkusakhulupilira Allah. Asilamu amavomereza aneneri onse owona amene adadza Muhammad (s.a.w) asadabadwe. Asilamu akuvomereza aneneri onse monga momwe Allah wafotokozera m’Qur’an. Ndipo savomereza omwe Allah sadawavomereze kuti ndi aneneri ake, monga Mirza Gulam Ahmad ndi Bahai. Oterewa ndi amene akunama kuti adapatsidwa uneneri pambuyo pa Mneneri Muhammad (s.a.w). Amene akukhulupilira amenewa ndiye kuti ngopandukira Allah. Tero tichenjere ndi udyerekezi wa Akadiani ndi Abahai ndi ena otere.
[153] Ayuda adauza mtumiki Muhammad (s.a.w) kuti sangakhulupirire pokhapokha amuone akukwera kumwamba popanda kugwilira chilichonse ndi kubwera pansi pano buku lili m’manja mwake mutalembedwa umboni wa Allah woti iye Muhammad ndi Mtumiki Wakedi. Ndipo Allah akuti makhalidwe otsutsana ndi aneneri siachilendo kwa Ayuda. Ndipo Musa atalephera kuchita zimenezo adamuda. Tero adapanga fano (lamwana wang’ombe ‘thole’) naliyesa mulungu wawo.
[154] (Ndime 154-156) Allah akupitiriza kufotokoza zoipa zawo. Ndipo zina mwa izo ndiizi: (a) Adakana kutsatira malamulo am’Taurat. Ndipo Allah adazula phiri naliimitsa pamwamba pa mitu yawo nawauza kuti: “Ngati simulola kulonjeza kuti mdzatsata zomwe zili m’Taurat, likusinjani phiri ili. (b) Adakana kulowera pachipata kudziko la Shamu (Kenani) monga momwe Allah adawalangizira. Ndipo adalowa monga momwe iwo amafunira. Shamu ndi dziko lomwe Allah adawapatsa kuti akalowemo ndi kukhazikika pambuyo posamuka ku Eguputo (Egypt). Koma iwo sadathokoze chisomochi potsata zomwe Allah adawauza. (c) Pambuyo polowa m’dzikolo adawauza kuti alemekeze tsiku la Sabata kuti likhale tsiku lamapemphero okhaokha. Lisakhale tsiku logwira ntchito. Koma iwo adachitachita ndale zawo mpaka lidasanduka tsiku logwira ntchito. (d) Ena mwa aneneri awo pamene adawaletsa iwo machitidwe amenewa mwaukali adawapha. (e) Mneneri Muhammad pamene adawafotokozera zizindikiro zomwe zinali m’mabuku mwawo zimene zimasonyeza utumiki wake sadamulabadire. Nanena kuti :“Mitima yathu yakutidwa. Siikumvetsa chilichonse chimene ukunena”. (f) Mneneri Isa (Yesu) pamene adawafotokozera za utumiki wake ndi kuwasonyeza zozizwitsa ndi zonse zomwe zidachitika m’kubadwa kwake, iwo adati Mariya adatenga pakati m’njira yachiwerewere pomwe iwo amadziwa kuti akungonama. (g) Adakonza chiwembu kuti aphe Isa (Yesu). Koma Allah adachiononga chiwembu chawocho pomuveka munthu wina nkhope ya Isa (Yesu) amene adali wamkulu wawo yemwe ankafunisitsa kupha Isa (Yesu). Tero adampachika mnzawoyo pamtanda. Pambuyo pake, akuluakulu aChiyuda adazindikira zonse zomwe zidachitikazi. Ndipo adangonyozera ngati kuti sichidachitike chilichonse chododometsa chifukwa choopa kuti anthu angawaukire. M’malomwake ankangodzidzudzula okha m’mtima mwawo.