আল-কোৰআনুল কাৰীমৰ অৰ্থানুবাদ - চিচেৱা অনুবাদ- খালিদ ইব্ৰাহীম বেতালা

পৃষ্ঠা নং:close

external-link copy
128 : 4

وَإِنِ ٱمۡرَأَةٌ خَافَتۡ مِنۢ بَعۡلِهَا نُشُوزًا أَوۡ إِعۡرَاضٗا فَلَا جُنَاحَ عَلَيۡهِمَآ أَن يُصۡلِحَا بَيۡنَهُمَا صُلۡحٗاۚ وَٱلصُّلۡحُ خَيۡرٞۗ وَأُحۡضِرَتِ ٱلۡأَنفُسُ ٱلشُّحَّۚ وَإِن تُحۡسِنُواْ وَتَتَّقُواْ فَإِنَّ ٱللَّهَ كَانَ بِمَا تَعۡمَلُونَ خَبِيرٗا

Ndipo ngati mkazi ataona kwa mwamuna wake nkhanza ndi kumusala, palibe kulakwa pa iwo kuyanjana pakati pawo mwachimvano. Ndipo chimvano ndichabwino. (Munthu aliyense amaumilira chimene afuna) chifukwa chakuti mitima ya anthu imaumilira umbombo. Koma ngati muchita zabwino ndi kuopa Allah, ndithudi, Allah Ngodziwa nkhani zanu zonse zomwe muchita. info
التفاسير:

external-link copy
129 : 4

وَلَن تَسۡتَطِيعُوٓاْ أَن تَعۡدِلُواْ بَيۡنَ ٱلنِّسَآءِ وَلَوۡ حَرَصۡتُمۡۖ فَلَا تَمِيلُواْ كُلَّ ٱلۡمَيۡلِ فَتَذَرُوهَا كَٱلۡمُعَلَّقَةِۚ وَإِن تُصۡلِحُواْ وَتَتَّقُواْ فَإِنَّ ٱللَّهَ كَانَ غَفُورٗا رَّحِيمٗا

Ndipo inu simungathe kuchita chilungamo (chenicheni) pakati pa akazi ngakhale mutayesetsa chotani. Koma musapendekere (mbali imodzi); kupendekera kwathunthu kotero kuti nkumusiya (yemwe simukumfunayo) ngati kuti wapachikidwa (osadziwika kuti ngokwatiwa kapena ayi). Ndipo ngati mutayanjana ndi kuopa Allah (zingakhale bwino). Ndithudi, Allah Ngokhululuka kwambiri, Ngwachisoni zedi. info
التفاسير:

external-link copy
130 : 4

وَإِن يَتَفَرَّقَا يُغۡنِ ٱللَّهُ كُلّٗا مِّن سَعَتِهِۦۚ وَكَانَ ٱللَّهُ وَٰسِعًا حَكِيمٗا

Koma ngati atalekana, Allah angalemeretse aliyense wa iwo kuchokera m’zabwino zake zochuluka ndipo Allah ali nazo zambiri, Ngwanzeru zakuya. info
التفاسير:

external-link copy
131 : 4

وَلِلَّهِ مَا فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَمَا فِي ٱلۡأَرۡضِۗ وَلَقَدۡ وَصَّيۡنَا ٱلَّذِينَ أُوتُواْ ٱلۡكِتَٰبَ مِن قَبۡلِكُمۡ وَإِيَّاكُمۡ أَنِ ٱتَّقُواْ ٱللَّهَۚ وَإِن تَكۡفُرُواْ فَإِنَّ لِلَّهِ مَا فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَمَا فِي ٱلۡأَرۡضِۚ وَكَانَ ٱللَّهُ غَنِيًّا حَمِيدٗا

Zonse za kumwamba ndi pansi nza Allah. Ndithudi, tidawalangiza omwe adapatsidwa buku patsogolo panu ndi inunso kuti muopeni Allah. Koma ngati mungakane, ndithudi, zonse za kumwamba ndi pansi nza Allah. Ndipo Allah Ngokhupuka kwabasi Wotamandidwa. info
التفاسير:

external-link copy
132 : 4

وَلِلَّهِ مَا فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَمَا فِي ٱلۡأَرۡضِۚ وَكَفَىٰ بِٱللَّهِ وَكِيلًا

Zonse za kumwamba ndi pansi nza Allah; ndipo Allah akukwana kukhala Mtetezi (kwa anthu Ake). info
التفاسير:

external-link copy
133 : 4

إِن يَشَأۡ يُذۡهِبۡكُمۡ أَيُّهَا ٱلنَّاسُ وَيَأۡتِ بِـَٔاخَرِينَۚ وَكَانَ ٱللَّهُ عَلَىٰ ذَٰلِكَ قَدِيرٗا

Ngati atafuna, akuchotsani, inu anthu, ndi kubweretsa ena. Ndipo Allah ali Wokhoza pazimenezo. info
التفاسير:

external-link copy
134 : 4

مَّن كَانَ يُرِيدُ ثَوَابَ ٱلدُّنۡيَا فَعِندَ ٱللَّهِ ثَوَابُ ٱلدُّنۡيَا وَٱلۡأٓخِرَةِۚ وَكَانَ ٱللَّهُ سَمِيعَۢا بَصِيرٗا

Amene afuna mphoto ya dziko lapansi, (afunefune kwa Allah). Kwa Allah ndikumene kuli mphoto ya pa dziko lapansi ndi ya tsiku lachimaliziro. Ndipo Allah Ngwakumva, Ngopenya. info
التفاسير: